Wolembedwa ndi Yohane 6:1-71

  • Yesu anadyetsa anthu 5,000 (1-15)

  • Yesu anayenda pamadzi (16-21)

  • Yesu ndi “chakudya chopatsa moyo” (22-59)

  • Ambiri anakhumudwa ndi mawu a Yesu (60-71)

6  Pambuyo pa zimenezi, Yesu anawolokera kutsidya lina la nyanja ya Galileya,* kapena kuti nyanja ya Tiberiyo.+  Ndipo gulu lalikulu la anthu linkamutsatira+ chifukwa linkaona zizindikiro zimene iye ankachita pochiritsa anthu odwala.+  Choncho Yesu anakwera mʼphiri ndipo anakhala pansi pamodzi ndi ophunzira ake.  Tsopano chikondwerero cha Ayuda cha Pasika+ chinali chitayandikira.  Yesu atakweza maso ake nʼkuona gulu lalikulu la anthu likubwera kwa iye, anafunsa Filipo kuti: “Kodi mitanda ya mkate yodyetsa anthu onsewa tingakaigule kuti?”+  Komatu iye ananena zimenezi pongofuna kumuyesa chifukwa ankadziwa kale zimene akufuna kuchita.  Filipo anamuyankha kuti: “Mitanda ya mkate ya ndalama zokwana madinari 200* singawakwanire ngakhale titati aliyense angolandirako pangʼono.”  Mmodzi wa ophunzira ake, Andireya mchimwene wake wa Simoni Petulo, anati:  “Pali kamnyamata pano kamene kali ndi mitanda 5 ya mkate wa balere ndi tinsomba tiwiri. Koma nanga zimenezi zingakwanire chigulu cha anthu chonsechi?”+ 10  Yesu ananena kuti: “Auzeni anthuwa kuti akhale pansi.” Pamalopo panali udzu wambiri. Choncho amuna pafupifupi 5,000 anakhaladi pansi.+ 11  Ndiyeno Yesu anatenga mitanda ya mkate ija. Atayamika, anaigawa kwa anthu onse amene anakhala pansi aja. Anachitanso chimodzimodzi ndi tinsomba tija ndipo anthuwo anadya mmene aliyense anafunira. 12  Anthu onsewo atakhuta, iye anauza ophunzira ake kuti: “Sonkhanitsani zotsala zonse, kuti pasawonongeke chilichonse.” 13  Choncho anatolera zonse, ndipo zinadzaza madengu 12 kuchokera pa mitanda ya mkate wa balere 5 ija, imene onse anadya mpaka kuilephera. 14  Anthuwo ataona chizindikiro chimene anachitacho, anayamba kunena kuti: “Mosakayika uyu ndi mneneri uja amene anati adzabwera padziko.”+ 15  Kenako Yesu atadziwa kuti anthu akufuna kubwera kudzamugwira kuti amuveke ufumu, anachoka+ nʼkupitanso kuphiri yekhayekha.+ 16  Chakumadzulo ndithu, ophunzira ake anapita kunyanja.+ 17  Iwo anakwera ngalawa nʼkuyamba kuwoloka nyanja kulowera ku Kaperenao. Pa nthawiyi nʼkuti mdima utagwa ndipo Yesu anali asanabwerebe kwa iwo.+ 18  Komanso nyanja inayamba kuchita mafunde chifukwa kunkawomba mphepo yamphamvu.+ 19  Koma atapalasa makilomita pafupifupi 5 kapena 6,* anaona Yesu akuyenda panyanja kuyandikira ngalawayo ndipo iwo anachita mantha. 20  Koma Yesu anawauza kuti: “Ndine, musachite mantha!”+ 21  Kenako anamulola kuti akwere mʼngalawa yawo, ndipo nthawi yomweyo ngalawa ija inakafika kumtunda kumene ankapita.+ 22  Tsiku lotsatira, anthu amene anali kutsidya lina la nyanjayo anaona kuti palibe ngalawa iliyonse. Pamalopo panali ngalawa imodzi yaingʼono, koma Yesu sanakwere ngalawayo limodzi ndi ophunzira ake chifukwa ophunzira akewo anachoka paokha. 23  Koma ngalawa zochokera ku Tiberiyo zinafika pafupi ndi pamalo amene anthuwo anadyera mkate uja Ambuye atayamika. 24  Choncho gulu la anthulo litaona kuti Yesu komanso ophunzira ake kulibe, linakwera ngalawa zawo nʼkupita ku Kaperenao kukafunafuna Yesu. 25  Atamupeza kutsidya kwa nyanjayo anamufunsa kuti: “Rabi,+ mwafika nthawi yanji kuno?” 26  Yesu anawayankha kuti: “Ndithu ndikukuuzani, sikuti mukundifunafuna chifukwa choti munaona zizindikiro ayi, koma chifukwa choti munadya mikate nʼkukhuta.+ 27  Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka, koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chimabweretsa moyo wosatha.+ Mwana wa munthu adzakupatsani chakudya chimenechi chifukwa Atate, Mulungu yekhayo, waika chidindo chake pa iye chomuvomereza.”+ 28  Choncho anthuwo anamufunsa kuti: “Kodi titani kuti tizichita zimene Mulungu amafuna?” 29  Yesu anawayankha kuti: “Zimene Mulungu akufuna kuti muzichita ndi zakuti muzisonyeza chikhulupiriro mwa amene anamutuma.”+ 30  Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Ndiye inuyo muchita chizindikiro chotani+ kuti ife tichione nʼkukukhulupirirani? Muchita ntchito yotani? 31  Makolo athu anadya mana mʼchipululu,+ monga mmene Malemba amanenera kuti: ‘Anawapatsa chakudya chochokera kumwamba kuti adye.’”+ 32  Kenako Yesu anati: “Ndithudi ndikukuuzani, Mose sanakupatseni chakudya chochokera kumwamba, koma Atate wanga amakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba. 33  Chifukwa chakudya chimene Mulungu wapereka ndi iye amene wabwera kuchokera kumwamba nʼkupereka moyo kudziko.” 34  Choncho iwo anamuuza kuti: “Ambuye, muzitipatsa chakudya chimenechi nthawi zonse.” 35  Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Ine ndine chakudya chopatsa moyo.* Aliyense wobwera kwa ine sadzamva njala ngakhale pangʼono, ndipo wokhulupirira mwa ine sadzamva ludzu.+ 36  Koma paja ndakuuzani kuti, ngakhale mwandiona, simukukhulupirirabe.+ 37  Aliyense amene Atate adzandipatse adzabwera kwa ine, ndipo amene wabwera kwa ine sindidzamuthamangitsa.+ 38  Chifukwa ndinabwera kuchokera kumwamba+ kudzachita zofuna za amene anandituma, osati zofuna zanga.+ 39  Chifuniro cha amene anandituma ine nʼchakuti, ndisataye aliyense mwa onse amene iye wandipatsa, koma kuti ndidzawaukitse+ pa tsiku lomaliza. 40  Zimene Atate wanga akufuna ndi zoti aliyense wovomereza Mwana komanso kumukhulupirira akhale ndi moyo wosatha,+ ndipo ine ndidzamuukitsa+ pa tsiku lomaliza.” 41  Atatero, Ayudawo anayamba kungʼungʼudza za iye chifukwa ananena kuti: “Ine ndine chakudya chochokera kumwamba.”+ 42  Iwo anayamba kunena kuti: “Kodi uyu si Yesu mwana wa Yosefe, amene bambo ake ndi mayi ake tikuwadziwa?+ Nanga bwanji pano akunena kuti, ‘Ndinachokera kumwambaʼ?” 43  Poyankha Yesu anati: “Siyani kungʼungʼudza inu. 44  Palibe munthu amene angabwere kwa ine pokhapokha Atate amene anandituma atamukoka+ ndipo ine ndidzamuukitsa pa tsiku lomaliza.+ 45  Zinalembedwa mʼMabuku a Aneneri kuti: ‘Onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.’*+ Aliyense amene wamva kwa Atate ndipo waphunzira amabwera kwa ine. 46  Palibe munthu amene anaonapo Atate,+ kupatulapo yekhayo amene anachokera kwa Mulungu, ameneyu anaona Atate.+ 47  Ndithudi ndikukuuzani, aliyense wokhulupirira adzapeza moyo wosatha.+ 48  Ine ndine chakudya chopatsa moyo.+ 49  Makolo anu anadya mana mʼchipululu koma anamwalirabe.+ 50  Ichi ndi chakudya chochokera kumwamba, choti aliyense adyeko kuti asamwalire. 51  Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati wina atadya chakudya chimenechi adzakhala ndi moyo wosatha. Ndipotu chakudya chimene ndidzapereke kuti dzikoli lipeze moyo, ndi mnofu wangawu.”+ 52  Kenako Ayudawo anayamba kutsutsana okhaokha kuti: “Kodi munthu ameneyu angathe bwanji kutipatsa mnofu wake kuti tidye?” 53  Choncho Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mukapanda kudya mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake, simudzapeza moyo.*+ 54  Aliyense amene amadya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga adzapeza moyo wosatha, ndipo ndidzamuukitsa+ pa tsiku lomaliza. 55  Chifukwa mnofu wanga ndi chakudya chenicheni ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. 56  Aliyense amene amadya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga, iyeyo ndi ine timakhala ogwirizana.+ 57  Atate wamoyo anandituma ine ndipo ine ndili ndi moyo chifukwa cha Atate. Mofanana ndi zimenezi, amene akudya mnofu wanga adzakhala ndi moyo chifukwa cha ine.+ 58  Chimenechi ndi chakudya chimene chinachokera kumwamba. Nʼchosiyana ndi chakudya chimene makolo anu anadya koma nʼkumwalirabe. Aliyense wakudya chakudya chimenechi adzakhala ndi moyo wosatha.”+ 59  Ananena zinthu zimenezi pamene ankaphunzitsa mʼsunagoge* ku Kaperenao. 60  Atamva zimenezi, ambiri mwa ophunzira ake anati: “Mawu amenewa ndi ozunguza. Ndi ndani angamvetsere zimenezi?” 61  Koma Yesu atadziwa kuti ophunzira ake akungʼungʼudza chifukwa cha zimene ananenazo, anawafunsa kuti: “Kodi mawuwa mwakhumudwa nawo? 62  Ndiye zidzakhala bwanji mukadzaona Mwana wa munthu akukwera kupita kumene anali poyamba?+ 63  Mzimu ndi umene umapatsa moyo+ koma mnofu ulibe ntchito iliyonse. Mawu amene ndakuuzaniwa ndi mzimu ndiponso ndi moyo.+ 64  Koma pali ena mwa inu amene sakukhulupirira.” Kuchokera pachiyambi, Yesu ankadziwa amene sankakhulupirira komanso amene adzamupereke.+ 65  Iye anapitiriza kunena kuti: “Nʼchifukwa chake ndinakuuzani kuti, palibe munthu amene angabwere kwa ine pokhapokha Atate atamulola.”+ 66  Chifukwa cha zimenezi, ophunzira ake ambiri anamusiya nʼkubwerera ku zinthu zakumbuyo+ ndipo sankayendanso naye. 67  Ndiyeno Yesu anafunsa ophunzira ake 12 aja kuti: “Inunso mukufuna kupita kapena?” 68  Simoni Petulo anayankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani?+ Inu ndi amene muli ndi mawu othandiza munthu kuti adzapeze moyo wosatha.+ 69  Ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera amene Mulungu anamutumiza.”+ 70  Yesu anawauza kuti: “Ine ndinakusankhani inu 12, si choncho?+ Komatu mmodzi wa inu ndi wonenera anzake zoipa.”*+ 71  Kwenikweni ankanena za Yudasi mwana wa Simoni Isikariyoti, chifukwa ameneyu anali kudzamupereka, ngakhale kuti anali mmodzi wa ophunzira 12 aja.+

Mawu a M'munsi

MʼBaibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti komanso nyanja ya Genesarete.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Masitadiya pafupifupi 25 kapena 30.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate wamoyo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mulibe moyo mwa inu nokha.”
Mabaibulo ena amati, “ankaphunzitsa pamalo amene ankachitira misonkhano.”
Kapena kuti, “ndi mdyerekezi.”