Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani?
Kodi mukuganiza kuti lili m’manja mwa . . .
Mulungu?
anthu?
kapena mwa winawake?
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.
“Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.”—1 Yoh. 3:8, Baibulo la Dziko Latsopano.
KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?
Zikutithandiza kudziwa chifukwa chake m’dzikoli muli mavuto ochuluka chonchi.—Chivumbulutso 12:12.
Tingakhulupirire kuti zinthu m’dzikoli zidzakhala bwino.—1 Yohane 2:17.
KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI?
Inde, tingazikhulupirire pa zifukwa zitatu izi:
Ulamuliro wa Satana utha posachedwapa. Yehova akufunitsitsa kuthetsa ulamuliro wa Satana. Iye analonjeza kuti adzawononga Mdyerekezi ndi kuchotseratu mavuto onse amene Satana wabweretsa.—Aheberi 2:14, Baibulo la Dziko Latsopano.
Mulungu anasankha Yesu Khristu kuti alamulire dziko lonse. Yesu ndi wosiyana kwambiri ndi Satana, yemwe ndi wolamulira wankhanza komanso wodzikonda. Ponena za ulamuliro wa Yesu, Mulungu analonjeza kuti: “Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka. . . . Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa.”—Salimo 72:13, 14.
Mulungu sanganame. Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “N’zosatheka kuti Mulungu aname.” (Aheberi 6:18) Yehova akalonjeza kuti achita chinachake, zimakhala ngati wachita kale. (Yesaya 55:10, 11) Choncho sitikukayikira kuti “wolamulira wa dzikoli aponyedwa kunja.”—Yohane 12:31.
GANIZIRANI MFUNDO IYI
Kodi wolamulira wadzikoli akadzawonongedwa, dzikoli lidzakhala bwanji?
Baibulo limayankha funso limeneli pa SALIMO 37:10, 11 ndi pa CHIVUMBULUTSO 21:3, 4.
Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi
ESSENTIAL BIBLE TEACHINGS
N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?
Anthu ambiri amafuna kudziwa kuti n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri. Baibulo limapereka yankho logwira mtima pa nkhaniyi.
KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi Mdyerekezi Alipodi?
Kodi Mdyerekezi ndi uchimo umene umakhala mumtima mwa munthu kapena ndi mngelo woti alipodi?
ZOKHUDZA IFEYO
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo—Vidiyo Yathunthu
Baibulo likuthandiza anthu ambirimbiri padziko lonse lapansi kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri. Kodi inunso mungakonde?
ZOKHUDZA IFEYO
Pemphani Kuti Tidzakuyendereni
Mutha kukhala ndi mwayi wokambirana nkhani inayake ya m’Baibulo kapena kudziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova.