MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | BANJA
Zimene Mungachite Kuti Musamakangane
ZOMWE ZIMACHITIKA
Kodi inuyo ndi mkazi kapena mwamuna wanu simutha kukambirana zinthu mwamtendere? Kodi nthawi zambiri mumada nkhawa kuti mwina zimene munene kapena kuchita ziyambitsa mkangano?
Ngati zili choncho musadandaule chifukwa zimenezi zikhoza kutha. Koma choyamba muyenera kufufuza chimene chimachititsa kuti muzikangana kawirikawiri.
ZOMWE ZIMACHITITSA
Kusamvetsetsana.
Mkazi wina wapabanja, dzina lake Jillian, * ananena kuti: “Nthawi zina ndimati ndikauza mwamuna wanga zinazake, iye amazimva mwanjira ina. Komanso nthawi zina ndimaganiza kuti ndamuuza zinazake pomwe sindinamuuze.”
Kusiyana maganizo.
Ngakhale kuti mumagwirizana kwambiri ndi mkazi kapena mwamuna wanu, nthawi zina mungasiyane maganizo pa nkhani inayake. Zili choncho chifukwa munthu aliyense ndi wosiyana ndi mnzake. Kusiyana kumeneku kungachititse kuti anthu azisangalala m’banja kapena azingokhalira kukangana ngati mmene zilili m’mabanja ambiri.
Kusowa chitsanzo chabwino.
Mkazi wina wapabanja, dzina lake Rachel, ananena kuti: “Makolo anga ankakonda kukangana komanso kulalatirana. Ndiyeno nditakwatiwa, ndinkakonda kulalatira mwamuna wanga ngati mmene mayi anga ankachitira. Makolo anga sanandiphunzitse kulemekeza mwamuna.”
Pamakhala chifukwa china.
Kawirikawiri m’banja anthu akamakangana pamakhala chifukwa china chomwe chikuchititsa kuti azikangana. Mwachitsanzo, mkazi akanena kuti, “Mumakonda kubwera mochedwa inu!” nthawi zambiri vuto silimakhala kuchedwako. Mwina amakhala akutanthauza kuti mwamunayo sakuchita zinthu momuganizira.
Kaya inuyo mumakangana pazifukwa zotani, koma dziwani kuti kumangokhalira kukangana kungachititse kuti mudwale kapena kuti banja lanu lithe. Ndiyeno kodi mungatani kuti musamakangane?
ZIMENE MUNGACHITE
Mukakangana, choyamba muzidziwa chomwe chachititsa kuti mukangane. Ndiyeno mitima yanu ikakhala pansi, muziyesa kuchita zotsatirazi.
1. Pezani mapepala awiri ndipo aliyense alembe chomwe chinachititsa kuti mukangane. Mwachitsanzo, mwamuna angalembe kuti, “Umangokhalira kucheza ndi azinzako tsiku lonse ndipo sunandiimbire kuti undiuze kumene unali.” Pomwe mkazi angalembe kuti, “Munakwiya chifukwa choti ndimacheza ndi azinzanga.”
2. Kambiranani moona mtima mfundo izi: Kodi nkhaniyi inayeneradi kufika mpaka pokangana? Kapena mukanatha kungoinyalanyalaza? Nthawi zina mungangofunika kulolera zinazake ngakhale kuti simukugwirizana nazo. Zimenezi zingathandize kuti muzikhala pa mtendere ndipo chikondi n’chimene chingakuthandizeni kuchita zimenezi.
Ngati nkhaniyo inali yaikulu, mungachite bwino kupepesana n’kuiiwala.
Koma ngati nonse mukuona kuti nkhaniyo ndi yaikulu kwambiri, chitani zotsatirazi.
3. Lembani mmene mumamvera pa nthawi imene mumakanganayo ndipo mwamuna kapena mkazi wanuyonso alembe. Mwachitsanzo, mwamuna angalembe kuti, “Ndimaona ngati umasangalala kucheza ndi azinzako kuposa ine.” Mkazi angalembe kuti, “Ndimaona ngati mumandilondalonda kwambiri ngati ndine mwana.”
4. Sinthanani mapepalawo kuti aliyense awerenge zimene mnzake walemba. Kodi mwamuna kapena mkazi wanu amada nkhawa ndi chiyani pa nthawi imene mumakanganayo? Kambiranani zimene aliyense akanachita pothana ndi vutolo m’malo mokangana.
5. Kambiranani zimene mwaphunzira. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji zimene mwaphunzira kuti mupewe kukangana?
^ ndime 7 Mayina asinthidwa.