MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA
Zimene Mungachite Mwana Akayamba Kuvuta
VUTO LIMENE LIMAKHALAPO
Mwana wanu wa zaka ziwiri akakwiya amayamba kulira kwambiri, kudziponya pansi komanso kutaya zinthu. Mwina mumadzifunsa kuti: ‘Koma mwana wangayu ndi wabwinobwino? Kodi akuvuta chifukwa chakuti sindikumulera bwino? Kodi adzasiya kuvuta?’
N’zotheka kuthandiza mwana wanu kusiya kuvuta. Komano choyamba, tiyeni tione chimene chimapangitsa kuti mwana ayambe kuvuta.
CHIMENE CHIMACHITITSA
Ana aang’ono sadziwa zimene angachite akakhumudwa. Zimenezi zingapangitse kuti nthawi zina azivuta. Komanso pali zifukwa zina.
Mwana akafika zaka ziwiri zinthu zina zimasintha pamoyo wake. Atangobadwa munkamuchitira chilichonse. Mwachitsanzo, akangolira munkasiya chilichonse chomwe mumapanga n’kukamusamalira. Mwina munkadzifunsa kuti ‘Kodi akudwala? Ali ndi njala? Akufuna kumunyamula? Kapena ndimusinthe thewera?’ Munkayesetsa kuchita chilichonse kuti asiye kulira ndipo simunkalakwitsa kuchita zimenezi chifukwa mwana wamng’ono amadalira makolo ake nthawi zonse.
Koma akafika zaka ziwiri, mwana amayamba kuzindikira kuti makolo ake sakumusamaliranso kwambiri ngati mmene ankachitira poyamba. Amaona kuti m’malo moti makolo azichita zimene iyeyo akufuna, makolowo amafuna kuti iyeyo azichita zimene iwowo akufuna. Mwanayo sangasangalale ndi kusintha kumeneku choncho angayambe kuvuta posonyeza kukwiya.
N’kupita kwa nthawi, mwanayo amazindikira kuti makolo ake ali ndi udindo womupatsa malangizo osati kungomusamalira. Komanso amazindikira kuti iyeyo monga mwana ayenera ‘kumvera makolo.’ (Akolose 3:20) Komabe nthawi imeneyi isanafike, mwanayo angamavute kwambiri ndipo zimenezi zingamasowetse mtendere makolowo.
ZIMENE MUNGACHITE
Muzimumvetsa. Muzikumbukira kuti mwana ndi mwana. Chifukwa chakuti sadziwa zimene angachite akakhumudwa, nthawi zina amangoyamba kuvuta. Choncho, muziyerekeza kuti zimene zikumuchitikirazo zikukuchitikirani inuyo.—Lemba lothandiza: 1 Akorinto 13:11.
Musamafulumire kupsa mtima. Mwana wanu akayamba kuvuta, musamafulumire kupsa mtima. Muzingoona kuti chamuchititsa kuyamba kuvuta n’chiyani. Kudziwa chifukwa chimene chachititsa mwanayo kuti ayambe kuvuta kungathandize kuti musamupsere mtima.—Lemba lothandiza: Miyambo 19:11.
Musamangomuchitira zimene akufuna. Mukamangopatsa mwana wanu chilichonse chomwe akufuna n’cholinga choti asiye kuvuta, ndiye kuti nthawi zonse azingovuta akafuna chinthu. Muzimuuza modekha kuti simusintha zimene mwanena.—Lemba lothandiza: Mateyu 5:37.
Kudziwa chifukwa chimene chachititsa mwanayo kuti ayambe kuvuta kungathandize kuti musamupsere mtima
Muzileza mtima. Musamaganize kuti mwana wanu angangosiya kuvuta lero ndi lero, makamaka ngati mumamuchitira zimene akufuna akayamba kuvuta. Choncho, mukamapewa kupsa mtima kapena kumangochitira mwana wanu zimene akufuna akayamba kuvuta, pang’ono ndi pang’ono amasiya kuvuta. Baibulo limanena kuti: “Chikondi n’choleza mtima.”—1 Akorinto 13:4.
Mwina mukhoza kuchitanso zotsatirazi:
Mwana wanu akayamba kuvuta muzimunyamula kuti asafulukutefulukute, koma musampane. M’malo momukalipira muzingodikira kuti mtima wake ukhale pansi. Pamapeto pake, mwanayo amazindikira kuti kuvuta sikungamuthandize chilichonse.
Pezani malo amene mungamuike kapena kumutsekera akayamba kuvuta. Muzimusiya konko ndipo muzimutulutsa akasiya kuvuta.
Ngati mwana wanu wayamba kuvuta muli pagulu, pitani naye pambali. Musamupatse zimene akufunazo chifukwa chakuti pali anthu. Ngati mutamupatsa angayambe kuganiza kuti ngati atayamba kuvuta, muzimupatsa chilichonse chomwe akufuna.