Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Mmene Mungathandizire Mwana Wanu Amene Amadzivulaza Mwadala

Mmene Mungathandizire Mwana Wanu Amene Amadzivulaza Mwadala

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Tayerekezani kuti mwadziwa kuti mwana wanu wakhala akudzivulaza mwadala. Mwina mungadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani mwana wanga amadzivulaza? Kapena mwina akufuna kudzipha?’

Nthawi zambiri sikuti mwana akamadzivulaza ndiye kuti akufuna kudzipha. * Koma ngati ali ndi vuto limeneli m’pofunika kumuthandiza. Kodi mungamuthandize bwanji? Choyamba, mufunika kudziwa chimene chikumuchititsa kuti azidzivulaza.

ZIMENE ZIMACHITITSA

Kodi achinyamata amadzivulaza chifukwa chongotengera anzawo? N’zoona kuti achinyamata ena amayamba kudzivulaza chifukwa chotengera anzawo. Komabe sikuti achinyamata onse amadzivulaza pa chifukwa chimenechi. N’chifukwa chiyani tikutero? Nthawi zambiri wachinyamata amene amadzivulaza amachita zimenezi mobisa ndipo amachita nazo manyazi. Mtsikana wina wazaka 20, dzina lake Celia, * ananena kuti: “Sindinkafuna kuti aliyense adziwe zimene ndinkachita ndipo ndinkabisa mabala anga kuti aliyense asawaone.”

Kodi amadzivulaza n’cholinga choti anthu ena awaone? N’zoona kuti achinyamata ena angamadzivulaze kuti ena awaone. Koma achinyamata amene tikunena m’nkhani ino ndi amene amayesa kubisa kuti anthu asadziwe kuti amadzivulaza. Komabe wachinyamata wina yemwe poyamba ankadzivulaza ananena kuti akadzivulaza ankafunitsitsa kuti wina aone mabala akewo n’cholinga choti amuthandize kuthana ndi mavuto ake.

Ndiyeno n’chifukwa chiyani amadzivulaza? Pali zinthu zambiri zimene zingachititse kuti achinyamata azidzivulaza. Koma vuto lalikulu limakhala lakuti akuvutika maganizo kwambiri. Katswiri wina wa matenda a maganizo, dzina lake Steven Levenkron, anafotokoza kuti “anthu ena ovutika maganizo amaona kuti amapezako bwino akadzivulaza.”

Munthu amene amadzivulaza amavutika kwambiri maganizo moti amalephera kufotokoza mmene akumvera

Kodi makolo ayenera kudziimba mlandu? Ayi. M’malo momangoganiza kuti mwina munalakwitsa chinachake, ndi bwino kuganizira zimene mungachite kuti mukhale kholo labwino komanso zimene mungachite kuti mwana wanuyo asiye khalidwe lodzivulaza.

 ZIMENE MUNGACHITE

Muuzeni mwana wanu kuti azinena momasuka zimene zikumuvutitsa maganizo. Kuti zimenezi zitheke mungachite zotsatirazi:

Muzimulimbikitsa. Mwana wanu akakuuzani kuti amadzivulaza, musafulumire kukwiya kapena kusonyeza kuti mukudabwa kwambiri. Muzimulankhula modekha komanso molimbikitsa.—Lemba lothandiza: 1 Atesalonika 5:14.

Musamamufunse momuwopseza. Mwachitsanzo, munganene kuti: “Ndimadziwa kuti pali zinthu zina zimene iweyo umaona ngati umalephera, tandiuza n’chiyani chimene chimakupweteketsa mtima kwambiri? Kapena munganene kuti, “Kodi ukuona kuti ndizitani ukakhala kuti ukuvutika maganizo kwambiri?” Kapenanso munganene kuti “Kodi ukuganiza kuti ndizitani kuti tizimasukirana?” Muzimvetsera akamayankha ndipo musamudule mawu.—Lemba lothandiza: Yakobo 1:19.

Muzimulimbikitsa kuti aziganizira kwambiri zimene amachita bwino. Popeza kuti nthawi zambiri anthu amene amadzivulaza amaganizira kwambiri zimene amalephera, mwina mungamulimbikitse kuti aziganizira kwambiri zimene amachita bwino. Mwachitsanzo, mungamuuze kuti alembe zinthu zitatu zimene amaona kuti amachita bwino. Mtsikana wina, dzina lake Briana, * ananena kuti: “Kulemba zimene ndimachita bwino kunandithandiza kudziwa kuti ndilinso ndi makhalidwe ena abwino.”

Muzimulimbikitsa kuti azipemphera kwa Yehova Mulungu. Baibulo limanena kuti: ‘Muzimutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Mtsikana wina wazaka 17, dzina lake Lorena, ananena kuti: “Ndinkayesetsa kumuuza Yehova mmene ndikumvera makamaka ndikamafuna kudzivulaza. Zimenezi zinkandithandiza kwambiri kupewa kudzivulaza.”—Lemba lothandiza: 1 Atesalonika 5:17.

^ ndime 5 Munthu amene amadzivulaza amadzipweteka yekha mwadala kaya kudzicheka, kudzimenya kapena kudzivulaza mwanjira ina.

^ ndime 7 Tasintha mayina m’nkhaniyi.

^ ndime 15 Nthawi zambiri munthu akamadzivulaza amakhala kuti akuvutika maganizo kapena ali ndi matenda enaake. Choncho, angafunike kupita kuchipatala. Magazini ya Galamukani! simasankhira anthu zochita pa nkhani ya mankhwala. Komabe, Akhristu ayenera kuonetsetsa kuti thandizo lililonse lomwe angapeze lisakhale losemphana ndi mfundo za m’Baibulo.