Kusunga Chinsinsi Komanso Pulogalamu Yosunga Mawu
Munthu aliyense ali ndi ufulu wosunga zinthu zokhudza iyeyo mwachinsinsi. Choncho, gulu la Mboni za Yehova limayesetsa kusunga chinsinsi cha anthu ena. Dinani apa ngati mukufuna kudziwa mfundo zimene gululi limatsatira pofuna kuteteza nkhani zosiyanasiyana zoti anthu osayenerera asazidziwe.
Mfundo zimene a Mboni amatsatira, zimafotokoza zimene iwo amachita poteteza zinthu zachinsinsi zokhudza anthu ena. Kuonjezera pamenepo, malangizo ena osiyanasiyana okhudza webusaiti ino afotokozedwa m’munsimu.
Webusaiti ino ndi ya bungwe la Watchtower Bible and Tract Society of New York. Bungweli ndi lomwe limayendetsa ntchito zosiyanasiyana zimene a Mboni za Yehova amachita kuphatikizapo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo. Zipangizo zina zimene zimasunga nkhani zomwe zimapezeka pa webusaitiyi zili m’dziko la United States.
Zokhudza Inuyo
Zinthu zokhudza inuyo zimene munalemba pawebusaiti ino, zimagwiritsidwa ntchito pa zolinga zokhazo zimene inuyo munauzidwa pa nthawi imene munkatsegula akaunti yanu.
Sitimapereka zinthu zokhudza inuyo kwa ena popanda chifukwa chomveka. Bungweli lingapereke zinthuzo kwa ena pokhapokha ngati inuyo mwapempha n’cholinga choti azigwiritse ntchito pokuthandizani pa zinthu zina ndipo adzakudziwitsani asanachite zimenezi. Lingaperekenso zinthuzo pofuna kutsatira malamulo kapena zimene akuluakulu a boma anena, ngati bungweli likufuna kupewa zachinyengo komanso ngati akufuna kukonza mavuto ena. Mukamagwiritsa ntchito webusaiti ino mumakhala mukuvomereza kuti enanso angapatsidwe zinthu zokhudza inuyo pa zifukwa zomwe tatchulazi. Sitidzagulitsa zinthu zilizonse zokhudza inuyo zimene mwatitumizira, zivute zitani.
Kukulumikizani ndi Mawebusaiti Ena. Nthawi zina pawebusaitiyi pamapezeka ma linki a mawebusaiti ena omwe tawavomereza kuti azichita zinthu zina m’malo mwathu, monga kulemba mafomu a pa intaneti. Pali zinthu ziwiri zimene zingakuthandizeni kudziwa ngati mwalumikizidwa ku mawebusaiti ena. Kaonekedwe ka webusaitiyo kamakhala kosiyana ndi kaonekedwe ka webusaiti yathu komanso malo amene mumalembapo adiresi yanu amasintha kaonekedwe. Ngati tikufuna kukulumikizani ndi webusaiti ina, timayamba taona kaye mfundo zimene iwo amatsatira akamafuna kuteteza nkhani zosiyanasiyana zoti anthu osayenerera asazidziwe ndipo timachita zimenezi nthawi ndi nthawi. Mfundozo ziyenera kukhala zogwirizana ndi mfundo zimene ifenso timayendera. Mungathe kuwerenga mfundo zimene webusaiti imene takulumikizani nayo imayendera mukatsegula webusaitiyo.
Kuteteza Zinthu Zokhudza Inuyo
Kuteteza zinthu zokhudza inuyo ndi nkhani yofunika kwambiri kwa ife. Timagwiritsa ntchito mapulogalamu apakompyuta amene amathandiza kuti anthu asapeze zinthu zachinsinsi zimene inuyo mwatitumizira. Mwachitsanzo timagwiritsa ntchito njira yoti anthu ena asathe kuwerenga zimene mwatumizazo monga yotchedwa Transport Layer Security (TLS).
Zokhudza Akaunti
Adiresi ya imelo imene mumapereka potsegula akaunti pawebusaiti ino imagwiritsidwa ntchito pokudziwitsani zina n’zina zokhudza akaunti yanu. Mwachitsanzo, ngati mwaiwala dzina kapena mawu achinsinsi olowera pa akaunti yanu ndipo mwapempha kuti akuthandizeni, mudzalandira uthenga wofotokoza zimene mungachite kudzera pa adiresi ya imelo imene munapereka potsegula akaunti yanu.
Kupereka Ndalama
Ngati mwapereka ndalama kudzera pa intaneti, timalemba dzina lanu komanso zimene zingatithandize kuti tilumikizane nanu. Kuti tithe kulandira ndalama zimene mungapereke pogwiritsa ntchito khadi logulira zinthu pangongole, timagwiritsa ntchito njira zapaintaneti zovomerezeka zokhala ndi mfundo zapamwamba zotetezera chinsinsi. Sitisunga kapena kudziwa zinthu zokhudza khadi lanulo, nambala ya akaunti yanu ya kubanki kapenanso zina zilizonse zimene munatumiza kwa amene munawagwiritsa ntchito potumiza ndalamazo. Tikalandira ndalama zanu, timasunga zinthu zonse zokhudza kuperekedwa kwa ndalamazo kwa zaka zosachepera 10. Zinthuzi ndi monga tsiku limene munapereka ndalama, kuchuluka kwake komanso njira imene munagwiritsa ntchito popereka ndalamazo. Zimenezi zimatithandiza kutsatira ndondomeko zonse zokhudzana ndi ndalama komanso kuti tithe kuyankha mafunso amene mungakhale nawo. Sitidzakupemphani kuti muonjezere ndalama zina.
Zinthu Zina Zokhudza Inuyo
Kupatula pa kupereka ndalama komanso kutsegula akaunti, mungathenso kutumiza zinthu zokhudza inuyo monga dzina lanu, adiresi komanso nambala yanu ya foni pa zifukwa zina monga pamene mukufuna kuti munthu wina azikuphunzitsani Baibulo kwaulere. Timasunga komanso kugwiritsa ntchito zinthu zokhudza inuyo pa zifukwa zokhazo zimene mwatumizira komanso panthawi yokhayo imene zigwiritsidwe ntchito.
Pulogalamu Yosunga Mawu ndi Mapulogalamu Ena
Pali zinthu zina zimene timasunga mukatsegula webusaiti yathu. Kuti zimenezi zitheke timagwiritsa ntchito “pulogalamu yosunga mawu,” “pulogalamu imene imasonyeza zinthu zimene munaziona” komanso mapulogalamu ena ofanana ndi amenewa. Kusunga mawu kumene tikufotokoza pano kukutanthauza zinthu zosiyanasiyana ndipo kumaphatikizapo zinthu monga mapulogalamu osungira zinthu a m’chipangizo chimene mukugwiritsa ntchito.
Pulogalamu Yosunga Mawu. Monga mmene zimakhalira ndi mawebusaiti ena, mukatsegula webusaiti ino pamakhala mawu ochepa amene angathe kusungidwa mu foni, tabuleti kapenanso kompyuta imene mukugwiritsa ntchito. Pali mitundu yosiyanasiyana ya mapulogalamu osungira mawu ndipo amagwiranso ntchito zosiyanasiyana. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzolowere kugwiritsa ntchito webusaitiyi. Timagwiritsa ntchito mapulogalamu osungira mawu kuti tidziwe ngati munatsegulapo webusaitiyi m’mbuyomu komanso kukukumbutsani zimene mumakonda kufufuza mukamagwiritsa ntchito webusaiti ino. Mwachitsanzo, pulogalamuyi imatha kusunga chinenero chimene mumakonda kugwiritsa ntchito. Izi zimathandiza kuti mukatsegulanso webusaitiyi, chinenerocho chizikhala choyamba kuoneka. Sitigwiritsa ntchito pulogalamuyi pofuna kulengeza zinthu.
M’munsimu tafotokoza mitundu itatu ya mapulogalamu osungira mawu amene amagwiritsidwa ntchito pawebusaiti ino.
Mapulogalamu Osungira Mawu Ofunika Kwambiri—Mapulogalamu amenewa amathandiza kwambiri kuti muthe kugwiritsa ntchito zinthu zina za pawebusaiti ino, monga kulowa kapena kutumiza mafomu pawebusaitiyi. Simungathe kuchita zinthu zosiyanasiyana zimene mukufuna popanda mapulogalamu amenewa. Mwachitsanzo, sizingatheke kuti muthe kupereka ndalama kudzera pawebusaiti. Mapulogalamu amenewa amatithandizanso kuti tithe kukuthandizani pamene mwapempha zinazake panthawi imene mukufufuza zinthu. Mapulogalamuwa sasunga zinthu zokhudza inuyo zimene zikhoza kugwiritsidwa ntchito pa nkhani zamalonda kapena kukumbukira malo osiyanasiyana amene munatsegula pa intaneti.
Mapulogalamu Okumbukira Zomwe Mumalemba Kawirikawiri—Mapulogalamuwa amathandiza kuti webusaiti izikumbukira zinthu zimene mumasankha, monga ngati dzina lanu lolowera pawebusaiti, chiyankhulo kapena dera limene muli. Mapulogalamu amenewa amakhala ndi zinthu zimene zingakuthandizeni kuti muzolowere kugwiritsa ntchito webusaitiyi.
Mapulogalamu Otha Kuwerengera—Mapulogalamuwa amathandiza kuti webusaitiyi izikumbukira zinthu monga nthawi zimene mwakhala mukutsegula webusaiti komanso kuti munatenga nthawi yaitali bwanji mutatsegula. Zimenezi zimatithandiza kuti tizikonza webusaitiyi n’cholinga choti izigwira bwino ntchito.
Kuonjezera pa mapulogalamu osunga mawu a webusaiti yathu palinso mapulogalamu osunga mawu opangidwa ndi mawebusaiti ena. Ife timagwiritsa ntchito mapulogalamu okhawo omwe ndi a webusaiti yathu koma timathanso kugwiritsira ntchito mapulogalamu a mawebusaiti enawo pokhapokha ngati ali opangidwa ndi kampani ya Google monga yotchedwa reCAPTCHA. Pulogalamuyi imathandiza kudziwa ngati munthu amene akulowa pa akaunti inayake ndi mwini wake wa akauntiyo kapena ndi kazitape yemwe akugwiritsa ntchito kompyuta yake. Mungathe kuwerenga mfundo zimene a kampani ya Google amayendera pofuna kuteteza chinsinsi cha ena mukadina pa linki iyi https://www.google.com/intl/en/policies/privacy/.
Kusunga Zomwe Mwachita. Malo amene mwatsegula pawebusaiti yathu, amatha kukhala ndi timafailo tomwe timasunga zomwe mwachita, monga kusunga tsamba limene mwatsegula. Timafailo timeneti timathandiza kuti tizidziwa mmene anthu akugwiritsira ntchito webusaiti ino komanso mmene ikugwirira ntchito.
Kugwiritsa ntchito adiresi ya IP. Adiresi ya IP ndi nambala imene imathandiza kuti kompyuta yanu izidziwika pa intaneti. Timagwiritsa ntchito adiresi yanu ya IP komanso pulogalamu yanu yolowera pa intaneti kuti tiziona mmene webusaitiyi ikugwirira ntchito, tizidziwa mavuto amene angakhale pa webusaitiyi komanso kuti tiziona zimene tingachite kuti tizikuthandizani m’njira yapamwamba kwambiri.
Zimene Mungasankhe Kuchita. Mapulogalamu ambiri olowera pa intaneti amakupatsani mwayi woti muzimitse pulogalamu yosunga mawu kapena kukuchenjezani pulogalamu yosunga mawuyo isanasungidwe mu chipangizo chanu. Kuti mudziwe mmene mungachitire zimenezi, onani malangizo amene ali m’pulogalamu yanu yolowera pa intaneti. Komabe, dziwani kuti simungathe kugwiritsa ntchito zinthu zina zimene zili pawebusaiti yathu popanda pulogalamu yosunga mawu.
Kuika Script kapena JavaScript
Kuika Script kumathandiza kuti webusaiti izigwira bwino ntchito. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti webusaiti izionetsa zinthu zimene mukufuna mofulumira. Dziwani kuti webusaiti simagwiritsa ntchito Script pofuna kuika mapulogalamu pakompyuta yanu kapena kutenga zinthu kwa inuyo popanda chilolezo chanu.
Kuti mbali zina za webusaiti zizigwira bwino ntchito, muyenera kuonetsetsa kuti JavaScript ndi yotsegula m’pulogalamu yanu yolowera pa Intaneti. Pa mawebusaiti ena, mapulogalamu olowera pa Intaneti amakupatsani mwayi wotsegula kapena kutseka JavaScript. Ngati mukufuna kudziwa mmene mungatsegulire JavaScript pa mawebusaiti ena, pitani pagawo lakuti “Zokuthandizani,” lomwe lili pa pulogalamu imene mukugwiritsa ntchito polowa pa Intaneti.
Ufulu Wanu
Kugwiritsa ntchito webusaiti ino komanso kupanga dawunilodi mabuku, mavidiyo kapena zinthu zongomvetsera, ndi kwaulere. Kuti muthe kugwiritsa ntchito webusaitiyi, simukufunika kuchita kutsegula akaunti, kupereka ndalama kapena kupereka zinthu zachinsinsi zokhudza inuyo. Komabe, nthawi zina mungasankhe kupereka ndalama, kutsegula akaunti, kupempha munthu woti aziphunzira nanu Baibulo kwaulere kapena kuchita zinthu zina zomwe zingafune kuti mupereka zinthu zachinsinsi zokhudza inuyo. Ngati mwasankha kuchita zimenezi, mumakhala kuti mukugwirizana ndi zomwe zili mu mfundo zokhudza kusunga chinsinsi. Mumakhalanso mukuvomereza kuti zinthu zokhudza inuyo zikhoza kusungidwa m’zipangizo zathu zosungira zinthu zomwe zili m’dziko la United States. Kuchita zimenezi kumasonyezanso kuti zinthu zokhudza inuyo zikhoza kutengedwa, kusungidwa komanso kugwiritsidwa ntchito ndi bungwe la Watchtower komanso mabungwe ena a Mboni za Yehova a m’mayiko osiyanasiyana kuti athe kukuthandizani malinga ndi zimene mwapempha. Timasunga zinthu zokhudza inuyo zimene n’zogwirizana ndi zomwe inuyo mwachita pa webusaiti yathu. Mwachitsanzo, ngati mukupereka ndalama ku gulu limene limayendetsa ntchito ya Mboni m’dziko lanu, dzina lanu komanso adiresi yanu zidzaperekedwa ku gulu lokhalo basi. Ngati mukupempha kuti wina aziphunzira nanu Baibulo, ndiye kuti dzina lanu komanso zinthu zina zokhudza inuyo zidzaperekedwa ku ofesi ya Mboni za Yehova m’dziko limene mukukhala kuti akuthandizeni.
Ngati simungapereke zinthu zachinsinsi zokhudza inuyo, simungathe kutsegula akaunti, kupereka ndalama kapena kuchita zinthu zina pa webusaitiyi zomwe zimatheka mukapereka zinthu zachinsinsi zokhudza inuyo ndipo tingalephere kukuthandizani.
Ngati taona kuti pakufunika kusintha mfundo zina pagawo lakuti “Kusunga Chinsinsi Komanso Pulogalamu Yosunga Mawu,” tidzalemba mfundo zatsopanozo patsamba lino n’cholinga choti nthawi zonse muzidziwa zinthu zimene timasunga komanso mmene timazigwiritsira ntchito.
Mogwirizana ndi malamulo, muli ndi ufulu woti mukhoza kuona zinthu zokhudza inuyo zimene munatumiza pawebusaiti ino, kuzikonza kapenanso kuzifufuta. Ngati kuchita zimenezi n’kotheka m’dziko lanu, mudzapeza zokuthandizani patsamba lino. Pa nkhani yokhudza kupereka ndalama, mungathe kukonza, kufufuta kapena kuona zokhudza inuyo zimene munatumiza, podziwitsa amene munauzidwa kuti mulumikizane nawo omwenso amalembedwa pa lisiti lanu losonyeza kuti mwatumiza ndalama.