Mfundo Zotetezera Nkhani Zachinsinsi
A Mboni za Yehova amalemekeza ufulu umene munthu aliyense ali nawo wosunga zinthu zokhudza iyeyo mwachinsinsi chifukwa chakuti amatsatira mfundo za m’Baibulo. Iwo amazindikira kufunika kolankhulana momasuka komanso kufunika kosunga zinthu zokhudza wina aliyense amene ndi wa Mboni ndi cholinga choti athe kumuthandiza malinga ndi zimene akufuna. Kuchita zimenezi n’kothandizanso pa nkhani zokhudza chipembedzo cha Mboni za Yehova komanso kuthandiza anthu amene ali ndi mavuto ena ake. A Mboni amaonetsetsanso kuti sakuulula zinthu zachinsinsi zokhudza munthu komanso kuonetsetsa kuti zinthuzo ndi zotetezedwa. (Miyambo 15:22; 25:9) Amaona kuti kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri.—Miyambo 20:19.
Mayiko ambiri anakhazikitsa malamulo pofuna kuonetsetsa kuti ufulu umene munthu aliyense ali nawo wosunga zinthu zokhudza iyeyo mwachinsinsi sukuphwanyidwa. Kwa nthawi yaitali, gulu la Mboni za Yehova lakhala likulemekeza ufuluwu ndipo linayamba kuchita zimenezi ngakhale panthawi imene mayiko anali asanakhazikitse malamulo okhudza nkhaniyi. Gululi lipitirizabe kuteteza zinthu zili zonse zokhudza munthu zimene lapatsidwa monga mmene lakhala likuchitira kwa nthawi yayitali, ndipo zimenezi zafotokozedwa mu mfundo zotetezera nkhani zachinsinsi zimene zili m’munsimu.
Amene Ayenera Kutsatira Mfundozi
Mfundo zotetezera nkhani zachinsinsi zimene zili m’munsimu ndi zimene gulu la Mboni za Yehova limatsatira kudzera m’maofesi a nthambi amene ali m’mayiko osiyanasiyana.
Kuteteza Zinthu Zokhudza Inuyo
Munthu akapereka zinthu zachinsinsi zokhudza iyeyo ku gulu la Mboni za Yehova, a Mboniwo amatsatira mfundo zimene zafotokozedwa m’munsimu pofuna kuteteza zinthuzo:
Zinthu zachinsinsi zokhudza munthu zimagwiritsidwa ntchito wachilungamo komanso mogwirizana ndi malamulo.
Zinthu zachinsinsi zokhudza munthu zimatengedwa ndi kugwiritsidwa ntchito pa nkhani zokhazo zokhudza chipembedzo cha Mboni za Yehova komanso kuthandiza anthu amene ali ndi mavuto ena ake.
Zinthu zachinsinsi zokhudza munthu ziyenera kukhala zolondola komanso zimasinthidwa kuti zigwirizane ndi m’mene zinthu zilili pamoyo wa munthuyo. Ngati pali zina zilizonse zolakwika, zimakonzedwa mwansanga.
Zinthu zokhudza munthu zimasungidwa kwa nthawi yokhayo imene zikufunika kuti zigwiritsidwe ntchito ndipo kenako zimafufutidwa.
Kulemekeza ufulu wa anthu amene apereka zinthu zokhudza iwowo ndi nkhani yofunika kwambiri kwa ife.
Gululi limagwiritsa ntchito zipangizo komanso njira zoyenera ndi cholinga choti anthu osayenera asadziwe zinthu zokhudza munthu zimene lapatsidwa. Makompyuta amene mumasungidwa zinthu zokhudza munthu amakhala ndi mawu achinsinsi olowera ndipo anthu ovomerezeka okha ndi amene amadziwa mawuwa. Maofesi amene mumakhala makompyutawa amakhomedwa nthawi yoweruka ikakwana ndipo anthu ovomerezeka okha ndi amene amakhala ndi makiyi.
Ofesi ya nthambi situmiza zinthu zokhudza munthu ku maofesi a nthambi a mayiko ena pokhapokha ngati kuchita zimenezi kuthandize pa ntchito ya Mboni za Yehova komanso pa ntchito yothandiza anthu amene akukumana ndi mavuto ena ake. Pamene munthu wasankha mwakufuna kwake kukhala wa Mboni za Yehova, amakhala akuvomereza kuti zinthu zokhudza iyeyo zikhoza kutumizidwa ku nthambi za mayiko ena ngati pangafunike kutero.
Ufulu Umene Munthu Ali Nawo
Mogwirizana ndi mfundo zimene a Mboni za Yehova amayendera poteteza zinthu zokhudza munthu, aliyense amene wapereka zinthu zokhudza iyeyo amapatsidwa ufulu woteteza zinthuzo, kuzifufuta kapenanso kukonza zomwe zalakwika.
Munthu aliyense amene wapempha kuti akufuna kuchita zina zake ndi zinthu zokhudza iyeyo zimene anatitumizira, ayenera kupereka umboni wokwanira wotsimikiza kuti ndi mwini wakedi wa zinthuzo.
Ngati munthu amene anatipatsa zinthu zokhudza iyeyo wapempha kuti apatsidwe zinthuzo, kukonza zinthu zolakwika kapena kuzifufuta, adzapatsidwa mwayi wochita zimenezi pambuyo poti gulu la Mboni za Yehova lawunika zolinga za munthuyo komanso latsimikiza kuti kuchita zimenezi sikungaike pangozi ufulu umene gululi lili nawo wochita zinthu zokhudza chipembedzo chawo.
Gulu la Mboni za Yehova limasunga zinthu zokhudza wina aliyense amene ndi wa Mboni kwa nthawi yonse imene munthuyo ali wa Mboni za Yehova. Kufufuta zinthu zimenezi ndi kosagwirizana ndi zimene gululi limakhulupirira komanso kuchita.
Zimene Mungachite Ngati Ufulu Wanu Waphwanyidwa
Ngati munthu akuona kuti ufulu wake waphwanyidwa mwa njira ina yake, akhoza kulemba kalata yofotokoza dandaulo lake ku Komiti ya Nthambi. Kalatayo iyenera kutumizidwa pasanathe milungu iwiri kuchokera pamene ufuluwo waphwanyidwa.