1 Akorinto 1:1-31
1 Ine Paulo, woitanidwa kukhala mtumwi+ wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu,+ pamodzi ndi Sositene+ m’bale wathu,
2 ndikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto,+ kwa inu amene mwayeretsedwa+ mwa Khristu Yesu, amene mwaitanidwa kuti mukhale oyera,+ pamodzi ndi onse amene kulikonse akuitana pa dzina+ la Ambuye wathu, Yesu Khristu, Ambuye wawo ndiponso wathu.+
3 Kukoma mtima kwakukulu+ ndi mtendere+ zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu+ zikhale ndi inu.
4 Nthawi zonse ndimayamika Mulungu chifukwa cha inu, poona kukoma mtima kwakukulu+ kwa Mulungu kumene anakusonyezani kudzera mwa Khristu Yesu,+
5 kuti mwa iye mwakhala olemera+ m’zinthu zonse, pokhala ndi mphamvu zonse za kulankhula ndi kudziwa zinthu zonse,+
6 popeza kuti umboni wonena za Khristu+ wakhazikika pakati pa inu,
7 moti palibe mphatso+ imene ikuperewera mwa inu, pamene mukudikira mwachidwi kuululidwa+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
8 Mulungu adzakulimbitsani+ mpaka pa mapeto, kuti musakhale ndi chifukwa chokunenezerani+ m’tsiku+ la Ambuye wathu Yesu Khristu.+
9 Mulungu amene anakuitanani kuti mukhale oyanjana+ ndi Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu, ndi wokhulupirika.+
10 Tsopano ndikukudandaulirani+ abale, m’dzina+ la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti nonse muzilankhula mogwirizana ndi kuti pasakhale magawano+ pakati panu, koma kuti mukhale ogwirizana+ pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.+
11 Pakuti a m’banja la Kuloe andiuza+ za inu, abale anga, kuti pali magawano pakati panu.
12 Ndikutanthauza kuti, ena mwa inu amanena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” ena amati, “Ine ndine wa Apolo,”+ enanso amati “Ine ndine wa Kefa,” pamene ena amati, “Ine ndine wa Khristu.”
13 Choncho Khristu wakhala wogawanika.+ Paulo sanapachikidwe chifukwa cha inu, anatero kodi? Kapena kodi munabatizidwa+ m’dzina la Paulo?
14 Ndikusangalala kuti sindinabatize aliyense wa inu kupatulapo Kirisipo+ ndi Gayo,+
15 moti wina sanganene kuti munabatizidwa m’dzina langa.
16 Inde, ndinabatizanso banja la Sitefana.+ Koma za enawo, sindikudziwa ngati ndinabatizapo aliyense.
17 Pakuti Khristu sananditume+ kukabatiza anthu, koma kukalengeza uthenga wabwino, osati mwa nzeru za kulankhula,+ kuti mtengo wozunzikirapo* wa Khristu ungakhale wopanda pake.
18 Nkhani yokhudza mtengo wozunzikirapowo ndi chinthu chopusa+ kwa anthu amene akupita kukawonongedwa,+ koma kwa ife amene tikupulumutsidwa+ ndi mphamvu ya Mulungu.+
19 Pakuti Malemba amati: “Ndidzathetsa nzeru zonse za anthu anzeru,+ ndipo ndidzakankhira pambali+ kuchenjera kwa anthu ophunzira.”+
20 Kodi wanzeru ali kuti? Mlembi ali kuti?+ Katswiri wa mtsutso+ wa nthawi* ino ali kuti?+ Kodi Mulungu sanapange nzeru za dzikoli kukhala zopusa?+
21 Pakuti ngakhale kuti dziko mwa nzeru zake+ silinathe kumudziwa Mulungu,+ kunamukomera Mulungu mwa nzeru zake kupulumutsa okhulupirira kudzera mu nkhani yopusayo,+ imene ikulalikidwa.
22 Pakuti Ayuda amafuna kuona zizindikiro+ ndipo Agiriki amafunafuna nzeru,+
23 koma ife timalalikira za Khristu amene anapachikidwa.+ Kwa Ayuda, chimenechi ndi chinthu chokhumudwitsa+ ndipo kwa mitundu ina ndi kupusa.+
24 Ngakhale zili choncho, kwa amene anaitanidwa, Ayuda ndiponso Agiriki, Khristu ndiye mphamvu+ ya Mulungu ndi nzeru+ za Mulungu.
25 Pakuti chinthu chopusa cha Mulungu ndi chanzeru kuposa anthu, ndipo chinthu chofooka cha Mulungu n’champhamvu kuposa anthu.+
26 Mukuona mmene anakuitanirani, abale, kuti si ambiri amene anthu amawaona kuti ndi anzeru+ omwe anaitanidwa,+ si ambiri amphamvu+ amene anaitanidwa, si ambiri a m’mabanja achifumu.
27 Koma Mulungu anasankha zopusa za dziko+ kuti achititse manyazi anthu anzeru, ndipo Mulungu anasankha zinthu zofooka za dziko kuti achititse manyazi+ zinthu zamphamvu.
28 Mulungu anasankha zinthu zonyozeka za dziko ndi zinthu zimene anthu amaziona ngati zachabechabe, zinthu zimene palibe,+ kuti athetse+ mphamvu zinthu zimene zilipo,
29 kuti pasapezeke munthu wodzitama+ pamaso pa Mulungu.
30 Koma inu muli ogwirizana ndi Khristu Yesu chifukwa cha Mulunguyo. Yesuyo amatisonyeza nzeru+ za Mulungu ndiponso chilungamo+ cha Mulungu. Kudzera mwa Yesu, anthu akhoza kuyeretsedwa,+ ndipo kudzera mwa dipo* akhoza kumasulidwa,+
31 kuti zikhale monga Malemba amanenera kuti: “Amene akudzitama, adzitame mwa Yehova.”+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 9.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.