1 Akorinto 16:1-24

16  Tsopano ponena za chopereka+ chopita kwa oyerawo,+ inunso tsatirani malangizo amene ndinapereka ku mipingo ya ku Galatiya.+  Tsiku lililonse loyamba la mlungu, aliyense wa inu aziika kenakake pambali kunyumba kwake malinga ndi mmene zinthu zikuyendera pa moyo wake, kuti ndikadzafika, zopereka zisadzaperekedwe pa nthawi imeneyo.  Koma ndikadzafika kumeneko, amuna alionse amene mungawavomereze m’makalata,+ ndidzawatuma kuti adzapititse mphatso yanu yachifundoyo ku Yerusalemu.  Komabe, ngati kudzakhala kofunika kuti inenso ndidzapite, tidzapitira limodzi.  Ndidzafika kwa inu pochokera ku Makedoniya, pakuti ndipita ku Makedoniya.+  Mwina ndidzakhala nanu pang’ono kumeneko, ngakhalenso kwa nyengo yonse yachisanu, kuti mudzandiperekeze+ kumene ndizidzapitako.  Pakuti sindikufuna kukuonani panopo mongodutsa chabe, koma ndikufuna kuti ndidzakhale nanu kanthawi ndithu,+ ngati Yehova+ alola.+  Koma ndikhalabe kuno ku Efeso+ mpaka chikondwerero cha Pentekosite,  pakuti khomo lalikulu la mwayi wautumiki landitsegukira,+ koma pali otsutsa ambiri. 10  Komabe, Timoteyo+ akadzafika mudzaonetsetse kuti asadzakhale ndi mantha pakati panu, pakuti iye akuchita ntchito ya Yehova,+ mmenenso ine ndikuchitira. 11  Choncho pasadzapezeke munthu womuderera.+ Mudzamuperekeze mu mtendere kuti adzafike kwa ine kunoko, pakuti ineyo ndikumuyembekezera pamodzi ndi abale. 12  Tsopano kunena za m’bale wathu Apolo,+ ndinamuchonderera kwambiri kuti abwere kwanuko pamodzi ndi abale, koma iye sanafune kubwera pa nthawi ino. Adzabwera akadzapeza mpata. 13  Khalani maso,+ limbani m’chikhulupiriro,+ pitirizani kuchita chamuna,+ khalani amphamvu.+ 14  Zonse zimene mukuchita, muzichite mwachikondi.+ 15  Tsopano ndikukulimbikitsani mokudandaulirani, abale, kuti: Mukudziwa kuti banja la Sitefana ndilo chipatso choyambirira+ mu Akaya ndi kuti anadzipereka kutumikira oyera.+ 16  Inunso pitirizani kudzipereka kwa anthu ngati amenewo, ndi kwa aliyense wogwirizana nafe pa ntchitoyi, ndiponso wogwira ntchito molimbika.+ 17  Koma ndikusangalala kuti Sitefana+ ndi Fotunato ndi Akayiko ali kuno ndi ine, pakuti alowa m’malo mwanu. 18  Pakuti atsitsimutsa mtima wanga+ ndi wanunso. Chotero, anthu otere muziwalemekeza.+ 19  Mipingo ya ku Asia ikupereka moni.+ Akula ndi Purisika, pamodzi ndi mpingo umene umasonkhana m’nyumba mwawo,+ akupereka moni wochokera pansi pa mtima kwa inu nonse, mwa Ambuye. 20  Abale onse akukupatsani moni. Mupatsane moni ndi kupsompsonana kopatulika.+ 21  Tsopano landirani moni wanga wolemba ndekha ndi dzanja langa, ineyo Paulo.+ 22  Ngati wina aliyense sakonda Ambuye, atembereredwe.+ Inde, idzani Ambuye!+ 23  Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu kukhale nanu. 24  Nonsenu landirani chikondi changa mwa Khristu Yesu.

Mawu a M'munsi