1 Mafumu 1:1-53

1  Mfumu Davide anali atakalamba+ ndipo anali ndi zaka zambiri. Ankamufunditsa zovala koma sankamva kutentha.  Choncho atumiki ake anamuuza kuti: “Mbuyanga mfumu, anthu akufunireni namwali wamng’ono+ woti azisamalira+ inu mfumu. Akhale mlezi+ wanu woti azigona pafupi nanu+ ndipo mbuyanga mfumu muzitenthedwa.”+  Ndiyeno anakafunafuna mtsikana wokongola m’dziko lonse la Isiraeli. Pamapeto pake anapeza Abisagi+ Msunemu+ n’kubwera naye kwa mfumu.  Mtsikanayo anali chiphadzuwa+ ndipo anakhala wosamalira mfumu. Mfumuyo sinagonepo naye.  Pa nthawi imeneyi Adoniya+ mwana wa Hagiti+ anadzikweza+ n’kumati: “Ineyo ndikhala mfumu yolamulira!”+ Kenako anapangitsa galeta* lake. Analinso ndi amuna okwera pamahatchi,* ndi amuna 50 amene ankathamanga patsogolo pake.+  Bambo ake sanafune kumukhumudwitsa pa nthawi ina iliyonse, choncho sanam’dzudzulepo kuti: “Wachitiranji zinthu m’njira imeneyi?”+ Iye analinso wooneka bwino kwambiri,+ ndipo mayi ake anam’bereka pambuyo pobereka Abisalomu.  Iye anayamba kuchitira zinthu limodzi ndi Yowabu mwana wa Zeruya komanso wansembe Abiyatara.+ Iwowa anayamba kumuthandiza Adoniya+ monga otsatira ake.  Koma wansembe Zadoki,+ Benaya+ mwana wa Yehoyada, mneneri Natani,+ Simeyi,+ Reyi, ndi amuna amphamvu+ a Davide, sanagwirizane+ ndi Adoniya.  Pomaliza Adoniya anapereka nsembe+ za nkhosa, ng’ombe, ndi ana a ng’ombe onenepa pafupi ndi mwala wa Zoheleti umene uli pafupi ndi Eni-rogeli.+ Kumeneko anaitanirako abale ake onse, omwe anali ana a mfumu,+ ndi amuna onse a mu Yuda, omwe anali atumiki a mfumu. 10  Koma mneneri Natani, Benaya, amuna amphamvu a Davide, ndi Solomo m’bale wake sanawaitane. 11  Kenako Natani+ anauza Bati-seba+ mayi wake wa Solomo+ kuti: “Kodi simunamve kuti Adoniya mwana wa Hagiti+ wakhala mfumu koma mbuye wathu Davide sakuzidziwa n’komwe zimenezi? 12  Tsopano mvetserani malangizo amphamvu amene ndikupatseni,+ kuti mupulumutse moyo wanu ndi moyo wa mwana wanu Solomo.+ 13  Pitani kwa Mfumu Davide mukanene kuti, ‘Kodi si inu mbuyanga mfumu amene munalumbirira ine kapolo wanu kuti: “Solomo mwana wako ndi amene adzakhale mfumu pambuyo panga, ndipo iye ndi amene adzakhale pampando wanga wachifumu”?+ Nanga n’chifukwa chiyani Adoniya wakhala mfumu?’ 14  Inu muli mkati molankhula ndi mfumuyo, ineyo ndidzabwera pambuyo panu n’kutsimikizira mawu anuwo.”+ 15  Zitatero, Bati-seba analowa kuchipinda kumene kunali mfumu.+ Mfumuyo inali yokalamba+ kwambiri ndipo Abisagi+ Msunemu anali kuisamalira. 16  Bati-seba anagwada n’kuweramira pansi+ pamaso pa mfumu. Mfumuyo inati: “Ukufuna kupempha chiyani?”+ 17  Bati-seba anayankha kuti: “Mbuyanga,+ ndinu amene munalumbira pa Yehova Mulungu wanu kwa ine kapolo wanu kuti, ‘Solomo mwana wako ndi amene adzakhale mfumu pambuyo pa ine, ndipo iye ndi amene adzakhale pampando wanga wachifumu.’+ 18  Koma tsopano onani, Adoniya+ wakhala mfumu ndipo inu mbuyanga mfumu simukuzidziwa n’komwe zimenezi.+ 19  Iye wapereka nsembe zambiri, za ng’ombe zamphongo, ana a ng’ombe onenepa, ndiponso nkhosa. Waitananso ana onse a mfumu,+ wansembe Abiyatara,+ ndi Yowabu+ mkulu wa asilikali, koma Solomo mtumiki wanu sanamuitane.+ 20  Tsopano maso+ a Aisiraeli onse ali pa inuyo mbuyanga mfumu, kuti muwauze amene akhale pampando wachifumu wa mbuyanga mfumu pambuyo panu.+ 21  Zomwe zidzachitike n’zoti, inuyo mbuyanga mfumu mukadzangogona m’manda limodzi ndi makolo anu,+ ineyo ndi mwana wanga Solomo tidzaoneka ngati olakwa.” 22  Bati-seba ali mkati molankhula ndi mfumuyo, mneneri Natani analowa.+ 23  Nthawi yomweyo anthu anauza mfumu kuti: “Kwabwera mneneri Natani!” Kenako Natani anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi pamaso pa mfumu.+ 24  Ndiyeno Natani anati: “Mbuyanga mfumu, kodi munanena kuti, ‘Adoniya ndiye adzakhale mfumu pambuyo panga ndipo ndiye amene adzakhale pampando wanga wachifumu’?+ 25  Chifukwatu lero wapita kukapereka nsembe+ zambiri, za ng’ombe zamphongo, ana a ng’ombe onenepa, ndi nkhosa. Waitananso ana onse a mfumu, akulu a asilikali ndi wansembe Abiyatara.+ Moti panopa ali kumeneko ndipo akudya ndi kumwa pamaso pake n’kumanena kuti, ‘Mfumu Adoniya ikhale ndi moyo wautali!’+ 26  Koma ineyo mtumiki wanu, wansembe Zadoki,+ Benaya+ mwana wa Yehoyada, ndi Solomo mtumiki wanu, sanatiitane.+ 27  Ngati zimenezi zachokera kwa inu mbuyanga mfumu, ndiye kuti simunandidziwitse ineyo mtumiki wanu,+ za amene ayenera kukhala pampando wachifumu wa mbuyanga mfumu pambuyo panu.” 28  Tsopano Mfumu Davide inayankha kuti: “Amuna inu, ndiitanireni Bati-seba.”+ Choncho Bati-seba analowa n’kuima pamaso pa mfumu. 29  Mfumuyo inalumbira+ kuti: “Pali Yehova+ amene anapulumutsa+ moyo wanga+ m’masautso onse,+ 30  monga momwe ndinakulumbirira pa Yehova Mulungu wa Isiraeli, kuti, ‘Mwana wako Solomo adzakhala mfumu pambuyo panga ndipo iye ndi amene adzakhale pampando wanga wachifumu m’malo mwanga,’ ndi mmene ndichitire lero.”+ 31  Kenako Bati-seba anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi+ pamaso pa mfumu, n’kunena kuti: “Mbuyanga Mfumu Davide akhale ndi moyo mpaka kalekale!”*+ 32  Nthawi yomweyo Mfumu Davide inati: “Amuna inu, ndiitanireni wansembe Zadoki,+ mneneri Natani ndi Benaya+ mwana wa Yehoyada.” Anthuwo anabweradi. 33  Mfumuyo inawauza kuti: “Tengani atumiki+ a mbuye wanu, n’kukweza Solomo mwana wanga panyulu* yanga yaikazi,+ ndipo mupite naye ku Gihoni.+ 34  Kumeneko, wansembe Zadoki ndi mneneri Natani akam’dzoze+ kukhala mfumu ya Isiraeli. Ndiyeno mukalize lipenga+ ndi kunena kuti, ‘Mfumu Solomo ikhale ndi moyo wautali!’+ 35  Ndiye pobwera muzikamulondola, ndipo adzafike kuno n’kukhala pampando wanga wachifumu. Iyeyo adzakhala mfumu m’malo mwanga ndipo ndidzamuika kukhala mtsogoleri wa Isiraeli ndi Yuda.” 36  Nthawi yomweyo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu kuti: “Zikhale momwemo!*+ Yehova, Mulungu wa mbuyanga mfumu, atsimikizire zimenezi.+ 37  Monga momwe Yehova anakhalira ndi inu mbuyanga mfumu,+ akhalenso ndi Solomo+ ndipo achititse mpando wake wachifumu kukhala waukulu+ kuposa mpando wanu wachifumu, mbuyanga Mfumu Davide.” 38  Wansembe Zadoki,+ mneneri Natani,+ Benaya+ mwana wa Yehoyada, Akereti+ ndi Apeleti+ anatsetsereka n’kukakweza Solomo panyulu yaikazi ya Mfumu Davide,+ kenako anapita naye ku Gihoni.+ 39  Tsopano wansembe Zadoki anatenga nyanga ya mafuta+ m’chihema+ n’kudzoza+ Solomo. Ndiyeno anthuwo anayamba kuliza lipenga ndipo anthu onse anafuula kuti: “Mfumu Solomo ikhale ndi moyo wautali!”+ 40  Atatero anthuwo anayamba kumulondola ndipo anali kuimba zitoliro+ ndi kusangalala kwambiri,+ moti nthaka+ inang’ambika chifukwa cha phokoso lawo. 41  Adoniya ndi anthu onse amene anawaitana omwe anali naye limodzi anamva phokosolo atamaliza kudya.+ Yowabu atamva phokoso la lipenga, nthawi yomweyo anati: “Kodi phokoso+ likumveka m’mudzili n’lachiyani?” 42  Akulankhula mawu amenewa, kunabwera Yonatani+ mwana wa wansembe Abiyatara. Ndipo Adoniya anati: “Lowa, uyenera kuti wabweretsa nkhani yabwino+ popeza ndiwe mwamuna wolimba mtima.” 43  Koma Yonatani anamuyankha Adoniya kuti: “Ayi, si nkhani yabwino! Mbuyathu Mfumu Davide waveka Solomo ufumu.+ 44  Choncho mfumu inatuma wansembe Zadoki, mneneri Natani, Benaya mwana wa Yehoyada, Akereti ndi Apeleti ndipo iwo anakweza Solomo panyulu yaikazi ya mfumu.+ 45  Ndiyeno wansembe Zadoki ndi mneneri Natani akamudzoza ku Gihoni kukhala mfumu.+ Kenako abwerako akusangalala ndipo m’mudzimo muli phokoso lokhalokha. Phokoso limenelo ndi limene munamva lija.+ 46  Komanso, Solomo wakhala pampando wachifumu.+ 47  Kuwonjezera apo, atumiki a mfumu abwera kudzafunira mafuno abwino mbuye wathu Mfumu Davide kuti: ‘Mulungu wanu akulitse dzina la Solomo kuposa dzina lanu ndiponso akweze ufumu wake kuposa ufumu wanu!’+ Kenako mfumuyo inaweramira pabedi.+ 48  Komanso mfumu inati, ‘Adalitsike+ Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene lero wapereka munthu woti akhale pampando wanga wachifumu, ine ndikuona ndi maso anga.’”+ 49  Anthu onse oitanidwa amene anali ndi Adoniya anayamba kunjenjemera ndipo anaimirira, aliyense n’kumapita kwawo.+ 50  Adoniya anachita mantha chifukwa cha Solomo. Choncho ananyamuka n’kupita kukagwira nyanga za guwa lansembe.+ 51  Patapita nthawi Solomo anauzidwa kuti: “Adoniya wachita mantha ndi Mfumu Solomo moti wakagwira nyanga za guwa lansembe, ndipo wati, ‘Mfumu Solomo indilumbirire kaye kuti siipha mtumiki wakene ndi lupanga.’” 52  Solomo atamva anati: “Akadzakhala munthu wolimba mtima, ngakhale tsitsi lake limodzi+ silidzathothoka n’kugwera pansi, koma choipa chikadzapezeka mwa iye,+ adzaphedwa.”+ 53  Choncho Mfumu Solomo inatumiza anthu kuti akachotse Adoniya paguwa lansembe lija n’kubwera naye. Kenako Adoniya analowa n’kugwadira Mfumu Solomo. Ndiyeno Solomo anamuuza kuti: “Pita kunyumba kwako.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.
Kapena kuti “Ame” m’Chiheberi.