1 Mafumu 10:1-29

10  Mfumukazi ya ku Sheba+ inali kumva za Solomo, ndi zoti anatchuka chifukwa cha dzina la Yehova.+ Choncho inabwera kuti idzamuyese pomufunsa mafunso ovuta.+  Mfumukaziyo inafika ku Yerusalemu ndi anthu ambiri oiperekeza.+ Inabwera ndi ngamila+ zitanyamula mafuta a basamu,+ golide wambiri, ndi miyala yamtengo wapatali. Inafika kwa Solomo n’kuyamba kunena zonse zimene zinali kumtima kwake.+  Solomo anaiyankha mfumukaziyo mafunso ake onse.+ Panalibe chimene mfumuyo inalephera kuyankha.+  Mfumukazi ya ku Sheba itaona nzeru zonse za Solomo,+ nyumba imene anamanga,+  chakudya cha patebulo pake,+ mmene atumiki ake anali kukhalira pa nthawi ya chakudya, mmene atumiki ake operekera zakudya anali kuchitira zinthu, zovala zawo, zakumwa zake,+ ndi nsembe zake zopsereza zimene ankapereka panyumba ya Yehova nthawi zonse, inazizira nkhongono ndipo inasowa chonena.+  Choncho inauza mfumuyo kuti: “Nkhani za zochita zanu ndi nzeru zanu zimene ndinamva kudziko langa, n’zoonadi.+  Sindinakhulupirire mawuwo mpaka pamene ndabwera n’kuona ndi maso anga, ndipo ndaona kuti ndinangouzidwa hafu chabe.+ Nzeru zanu ndi ulemerero wanu zaposa zinthu zimene ndinamva.+  Odala anthu anu,+ odala+ atumiki anuwa amene amatumikira pamaso panu nthawi zonse, n’kumamva nzeru zanu.+  Adalitsike+ Yehova Mulungu wanu, amene wasangalala+ nanu mwa kukuikani pampando wachifumu wa Isiraeli.+ Popeza Yehova adzakonda Isiraeli mpaka kalekale,+ wakuikani kuti mukhale mfumu+ kuti muzipereka zigamulo+ ndi kuchita chilungamo.”+ 10  Kenako mfumukaziyo inapatsa+ mfumuyo golide wokwana matalente* 120,+ mafuta a basamu+ ochuluka zedi, ndi miyala yamtengo wapatali. Mafuta a basamu amene mfumukazi ya ku Sheba inapatsa Mfumu Solomo, anali ochuluka kwambiri moti sipanakhalenso mafuta ochuluka ngati amenewo. 11  Zombo+ za Hiramu zimene zinabweretsa golide kuchokera ku Ofiri,+ zinabweretsanso matabwa a mtengo wa m’bawa+ ochuluka zedi ndi miyala yamtengo wapatali.+ 12  Mfumuyo inapanga zochirikizira nyumba ya Yehova+ ndi nyumba ya mfumu, pogwiritsira ntchito matabwa a m’bawawo. Inapanganso azeze+ ndi zoimbira za zingwe+ n’kupatsa oimba. Matabwa a m’bawa ochuluka chonchi sanayambe abwerapo kapena kuonedwapo mpaka lero. 13  Mfumu Solomo inapatsa mfumukazi ya ku Sheba zofuna zake zonse zimene inapempha, kuwonjezera pa zimene Mfumu Solomo inam’patsa malinga ndi kuwolowa manja+ kwa mfumuyo. Pambuyo pake, mfumukaziyo inatembenuka n’kubwerera kudziko lake, pamodzi ndi antchito ake.+ 14  Golide+ amene ankabwera kwa Solomo chaka chimodzi, anali wolemera matalente 666,*+ 15  osawerengera golide wochokera kwa amalonda oyendayenda, ndi phindu lochokera kwa amalonda, komanso golide wochokera kwa mafumu onse+ a Aluya,+ ndi kwa abwanamkubwa a m’dzikolo. 16  Mfumu Solomo inapanga zishango 200 zikuluzikulu za golide wosakaniza ndi zitsulo zina.+ (Chishango chachikulu chilichonse anachikuta ndi golide wolemera masekeli* 600.)+ 17  Inapanganso zishango 300 zing’onozing’ono za golide wosakaniza ndi zitsulo zina. (Chishango chaching’ono chilichonse anachikuta ndi golide wolemera ma mina* atatu.)+ Kenako mfumuyo inaika zishangozi m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+ 18  Itatero, mfumuyo inapanga mpando wachifumu+ waukulu waminyanga ya njovu,+ n’kuukuta ndi golide woyenga bwino.+ 19  Panali masitepe 6 okafika kumpando wachifumuwo. Kuseri kwa mpando wachifumuwo kunali chotchingira chozungulira. Mpandowo unali ndi moika manja mbali zonse ziwiri. M’mphepete mwake munali zifaniziro ziwiri za mikango+ itaimirira.+ 20  Pamasitepe 6 amenewo, panali zifaniziro 12 za mikango itaimirira, mbali iyi ndi iyi. Panalibenso ufumu wina umene unali ndi mpando wachifumu ngati umenewo.+ 21  Ziwiya zonse zomweramo Mfumu Solomo zinali zagolide, ndipo ziwiya zonse za m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni+ zinali za golide woyenga bwino.+ Panalibe chiwiya chasiliva. Siliva sankaoneka ngati kanthu m’masiku a Solomo. 22  Zinali choncho chifukwa mfumuyo inali ndi zombo za ku Tarisi+ panyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu. Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombo za ku Tarisizo zinkabweretsa golide,+ siliva, minyanga ya njovu,+ anyani, ndi mbalame zotchedwa pikoko. 23  Chotero Mfumu Solomo inali yolemera kwambiri+ ndiponso yanzeru+ kwambiri kuposa mafumu ena onse a padziko lapansi. 24  Anthu onse a padziko lapansi ankafuna kuonana ndi Solomo, kuti amve nzeru zake zimene Mulungu anaika mumtima mwake.+ 25  Aliyense anali kubweretsa mphatso+ chaka chilichonse+ monga zinthu zasiliva,+ zinthu zagolide, zovala, zida zankhondo,+ mafuta a basamu, mahatchi, ndi nyulu.+ 26  Solomo anali kusonkhanitsa magaleta ambiri ndi mahatchi ankhondo, ndipo anakhala ndi magaleta 1,400 ndi mahatchi ankhondo 12,000.+ Zimenezi anali kuzisunga m’mizinda yake yosungiramo magaleta ndiponso pafupi ndi mfumuyo ku Yerusalemu.+ 27  Mfumuyo inachititsa kuti ku Yerusalemu siliva akhale wochuluka kwambiri ngati miyala,+ ndiponso kuti matabwa a mkungudza akhale ochuluka kwambiri ngati mitengo yamkuyu ya ku Sefela.+ 28  Panalinso mahatchi amene Solomo anali kugula kuchokera ku Iguputo, ndipo gulu la amalonda a mfumu ndilo linali kugula mahatchiwo m’magulumagulu.+ 29  Nthawi ndi nthawi anali kugula galeta lochokera ku Iguputo pamtengo wa ndalama zasiliva 600. Hatchi anali kuigula pamtengo wa ndalama zasiliva 150. Umu ndi mmene mafumu onse a Ahiti+ ndi mafumu a ku Siriya anali kuchitira. Mafumuwa ankagwiritsa ntchito amalondawo pogula zinthuzo.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.
Golide ameneyu angakwane ndalama pafupifupi madola 256,643,000 a ku America.
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
Onani Zakumapeto 12.