1 Petulo 1:1-25
1 Ine Petulo mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu,+ amene muli alendo osakhalitsa,+ amene mwamwazikana+ ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya,+ Asia, ndi ku Bituniya.
2 Ndikukulemberani inu amene Mulungu Atate+ anakudziwiranitu mwa kukuyeretsani ndi mzimu+ kuti mukhale omvera ndi owazidwa+ magazi a Yesu Khristu, kuti:+
Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere ziwonjezeke kwa inu.+
3 Atamandike Mulungu amenenso ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu,+ pakuti mwachifundo chake chachikulu, anatibereka mwatsopano+ kuti tikhale ndi chiyembekezo cha moyo+ mwa kuukitsidwa+ kwa Yesu Khristu.
4 Anatibereka kuti tikhale ndi cholowa chosawonongeka,+ chosadetsedwa ndiponso chosasuluka. Cholowa chimenechi anasungira inuyo kumwamba,+
5 inuyo amene Mulungu akukutetezani ndi mphamvu yake chifukwa muli ndi chikhulupiriro.+ Mulungu akukutetezani kuti mudzalandire chipulumutso,+ ndipo chipulumutso chimenechi chidzaonekera+ mu nthawi ya mapeto.+
6 Pa chifukwa chimenechi, mukusangalala kwambiri ngakhale kuti padakali pano n’koyenera kuti muvutike kwa kanthawi chifukwa cha mayesero osiyanasiyana amene akukuchititsani chisoni.+
7 Zimenezi zikukuchitikirani kuti chikhulupiriro chanu, chimene chayesedwa+ ndipo n’chamtengo wapatali kuposa golide amene amawonongekabe ngakhale kuti anadutsa m’moto,+ chidzakuchititseni kutamandidwa ndiponso kulandira ulemerero ndi ulemu, zochita za Yesu Khristu zikadzaululika.*+
8 Ngakhale kuti simunamuonepo, mumamukonda.+ Ngakhale simukumuona panopa, mumakhulupirira mwa iye ndipo mukusangalala kwambiri ndi chimwemwe chachikulu ndiponso chosaneneka,
9 popeza ndinu otsimikiza kuti chikhulupiriro chanu chidzachititsa kuti miyoyo yanu ipulumuke.+
10 Aneneri amene analosera+ za kukoma mtima kwakukulu kumene munali kudzasonyezedwa,+ anafufuza za chipulumutso chimenechi mwakhama ndi mosamala.+
11 Anali kufufuza nyengo+ yake kapena mtundu wa nyengo imene mzimu+ umene unali mwa iwo unali kuwasonyeza yokhudzana ndi Khristu.+ Mzimuwo unali kuchitira umboni za masautso a Khristu+ ndi za ulemerero+ wobwera pambuyo pake.
12 Zinaululidwa kwa iwo kuti sanali kudzitumikira okha,+ koma anali kutumikira inu mwa zinthu zimene tsopano zalengezedwa+ kwa inu. Zimenezi zalengezedwa kwa inu ndi olengeza uthenga wabwino, mwa mzimu woyera+ wotumizidwa kuchokera kumwamba. M’zinthu zimenezi angelo akulakalaka kusuzumiramo.+
13 Konzekeretsani maganizo anu kuti mugwire ntchito mwamphamvu,+ khalanibe oganiza bwino,+ ndipo ikani chiyembekezo chanu pa kukoma mtima kwakukulu+ kumene kudzafika kwa inu, Yesu Khristu akadzaonekera.*+
14 Monga ana omvera, lekani kukhala motsatira+ zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziwa.
15 Koma khalani motsanzira Woyera amene anakuitanani. Inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse,+
16 chifukwa Malemba amati: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.”+
17 Ndiponso, ngati mukupempha zinthu kwa Atate, amene amaweruza mopanda tsankho+ malinga ndi ntchito za aliyense, chitani zinthu ndi mantha+ pa nthawi imene muli ngati alendo m’dzikoli.+
18 Pajatu mukudziwa kuti sizinali zinthu zotha kuvunda,+ siliva kapena golide, zimene zinakumasulani+ ku khalidwe lanu lopanda phindu limene munalilandira kuchokera kwa makolo anu mwa chikhalidwe chanu.
19 Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali,+ monga a nkhosa yopanda chilema ndi yopanda mawanga,+ magazi a Khristu.+
20 Iye anadziwikiratu dziko lisanakhazikitsidwe,+ koma anaonekera pa nthawi ya mapeto chifukwa cha inuyo,+
21 amene kudzera mwa iye, mukukhulupirira Mulungu,+ amene anamuukitsa kwa akufa+ ndi kum’patsa ulemerero,+ kuti chikhulupiriro ndiponso chiyembekezo chanu zikhale mwa Mulungu.+
22 Tsopano, popeza mwayeretsa+ miyoyo yanu mwa kukhala omvera choonadi ndipo zotsatira zake n’zakuti mumakonda abale mopanda chinyengo,+ kondanani kwambiri kuchokera mumtima.+
23 Pakuti inu mwabadwa mwatsopano,+ osati kuchokera m’mbewu yotha kuwonongeka,+ koma m’mbewu+ yosatha kuwonongeka,+ kudzera m’mawu+ a Mulungu wamoyo ndi wamuyaya.+
24 Pakuti “anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo wonse uli ngati duwa la udzu.+ Udzuwo umafota ndipo duwalo limathothoka,+
25 koma mawu a Yehova amakhala kosatha.”+ “Mawu”+ amenewo ndi amene alengezedwa+ kwa inu monga uthenga wabwino.