1 Yohane 2:1-29
2 Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zinthu izi kuti musachite tchimo.+ Komabe, wina akachita tchimo, tili ndi mthandizi+ wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.+
2 Iye ndi nsembe+ yophimba+ machimo athu.+ Osati athu+ okha, komanso a dziko lonse lapansi.+
3 Tikapitiriza kusunga malamulo ake ndiye kuti tikumudziwa.+
4 Munthu amene amanena kuti: “Ine ndikumudziwa,”+ koma sasunga malamulo ake,+ ameneyo ndi wabodza, ndipo mwa munthu ameneyo mulibe choonadi.+
5 Koma aliyense wosunga mawu ake,+ amasonyeza kuti amakondadi Mulungu.+ Chifukwa cha zimenezi, timadziwa kuti ndife ogwirizana naye.+
6 Amene amanena kuti ndi wogwirizana+ naye, ayenera kupitiriza kuyenda mmene iyeyo anayendera.+
7 Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano, koma lamulo lakale+ limene mwakhala nalo kuyambira pa chiyambi.+ Lamulo lakale limeneli ndiwo mawu amene munamva.
8 Komabe, ndikukulemberani lamulo latsopano limene Yesu analitsatira, limenenso inuyo mukulitsatira, chifukwa chakuti mdima+ ukupita ndipo kuwala kwenikweni+ kwayamba kale kuunika.
9 Amene amanena kuti ali m’kuunika koma amadana+ ndi m’bale wake, ndiye kuti ali mu mdima mpaka pano.+
10 Amene amakonda m’bale wake ndiye kuti ali m’kuunika,+ ndipo palibe chimene chingamukhumudwitse.+
11 Koma amene amadana ndi m’bale wake ndiye kuti ali mu mdima ndipo akuyenda mu mdimawo,+ ndiponso sakudziwa kumene akupita+ chifukwa maso ake achita khungu chifukwa cha mdimawo.
12 Ndikukulemberani inu ana anga okondedwa, pakuti machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina lake.+
13 Ndikulembera abambo inu, chifukwa mukumudziwa amene wakhala alipo kuyambira pa chiyambi.+ Ndikulemberanso inu anyamata+ chifukwa mwagonjetsa woipayo.+ Ndikulembera inu ana+ chifukwa mukuwadziwa Atate.+
14 Ndikulembera inu abambo+ chifukwa mukumudziwa iye amene wakhalapo kuyambira pa chiyambi.+ Ndikulembera inu anyamata chifukwa ndinu olimba+ ndipo mawu a Mulungu akhaladi mwa inu+ ndiponso mwagonjetsa woipayo.+
15 Musamakonde dziko kapena zinthu za m’dziko.+ Ngati wina akukonda dziko, ndiye kuti sakonda Atate.+
16 Pakuti chilichonse cha m’dziko,+ monga chilakolako cha thupi,+ chilakolako cha maso+ ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake,+ sizichokera kwa Atate, koma kudziko.+
17 Ndiponso, dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake,+ koma wochita chifuniro+ cha Mulungu adzakhala kosatha.+
18 Ana inu, ino ndi nthawi yakumapeto,+ ndipo monga mmene munamvera kuti wokana Khristu akubwera,+ ngakhale panopa alipo okana Khristu ambiri.+ Chifukwa cha zimenezi timadziwa kuti ino ndi nthawi yakumapeto.
19 Amenewo anachoka pakati pathu, koma sanali m’gulu lathu,+ chifukwa akanakhala a m’gulu lathu, akanakhalabe ndi ife.+ Sikuti onse ali m’gulu lathu ayi, ndipo iwo achoka m’gulu lathu, kuti zimenezi zidziwike.+
20 Inu munadzozedwa ndi woyerayo,+ ndipo nonsenu ndinu odziwa choonadi.+
21 Ndikukulemberani izi, osati chifukwa chakuti simudziwa choonadi,+ koma chifukwa chakuti mukuchidziwa,+ ndiponso chifukwa chakuti palibe bodza lililonse limene limachokera m’choonadi.+
22 Kodi wabodza angakhalenso ndani, kuposa amene amatsutsa kuti Yesu ndiye Khristu?+ Ameneyu ndiye wokana Khristu,+ amene amakana Atate ndi Mwana.+
23 Aliyense amene amakana Mwana sangakhale pa ubwenzi ndi Atate.+ Amene wavomereza+ Mwana amakhalanso pa ubwenzi ndi Atate.+
24 Koma zimene inu munamva pa chiyambi zikhalebe mumtima mwanu.+ Zimene munamva pa chiyambi zikakhalabe mumtima mwanu, mudzakhalanso ogwirizana+ ndi Mwana ndi Atate.+
25 Ndipotu, lonjezo limene iye watipatsa ndi la moyo wosatha.+
26 Ndikukulemberani za anthu amene akufuna kukusocheretsani.+
27 Inuyo, Mulungu anakudzozani ndi mzimu+ ndipo mzimu umenewo udakali mwa inu. Chotero simukufunikira wina aliyense kuti azikuphunzitsani,+ koma popeza kuti munadzozedwadi moona+ osati monama, chifukwa cha kudzozedwako, mukuphunzitsidwa zinthu zonse.+ Monga mmene mwaphunzitsidwira, pitirizani kukhala ogwirizana+ naye.
28 Tsopano inu ana anga okondedwa,+ khalanibe ogwirizana+ naye, kuti akadzaonetsedwa,+ tidzakhale ndi ufulu wa kulankhula.+ Kutinso tisadzachititsidwe manyazi ndi kuchotsedwa kwa iye pa nthawi ya kukhalapo*+ kwake.
29 Ngati mwadziwa kuti iye ndi wolungama,+ mwadziwa kuti aliyense wochita zolungama anabadwa kuchokera kwa iye.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 8.