2 Akorinto 10:1-18

10  Tsopano ineyo Paulo, ndikukudandaulirani mwa kufatsa+ ndi kukoma mtima+ kwa Khristu, ngakhale kuti ndimaoneka wosanunkha kanthu+ ndikakhala pakati panu, koma wolimba mtima polankhula nanu ndili kwina.+  Ndithu ndikanakonda kuti anthu amene akuona kuti ifeyo timachita zinthu motsatira maganizo a dzikoli,* asinthe maganizo awo, kuti ndikadzabwera kumeneko ndisadzachite zinthu zazikulu zotsutsana nawo.+  Pakuti ngakhale kuti moyo wathu ndi wofanana ndi wa anthu ena onse,+ sitikumenya nkhondo motsatira maganizo a dzikoli.+  Pakuti zida za nkhondo yathu si zochokera m’dziko lino,+ koma ndi zida zamphamvu zimene Mulungu watipatsa,+ zimene zimatha kugwetsa zinthu zozikika molimba.  Pakuti tikugubuduza maganizo komanso chotchinga chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu,+ ndipo tikugonjetsa ganizo lililonse n’kulimanga ngati mkaidi kuti lizimvera Khristu.  Komanso ndife okonzeka kupereka chilango pa aliyense wosamvera,+ inuyo mukadzasonyeza kuti ndinu omvera pa chilichonse.+  Mukuona zinthu mogwirizana ndi maonekedwe ake akunja.+ Ngati aliyense amakhulupirira mumtima mwake kuti ndi wotsatira Khristu, adziwenso kuti, monga mmene iye alili wotsatira Khristu, ifenso ndife otsatira Khristu.+  Pakuti ngakhale nditati ndidzitamandire+ mopitirirako muyezo za ulamuliro umene Ambuye anatipatsa kuti tikulimbikitseni, osati kukupasulani,+ sindingachite manyazi.  Ponena zimenezi, sindikufuna kuti muganize kuti makalata anga cholinga chake n’kukuopsezani. 10  Pakuti ena amati: “Makalata ake ndi olemerera ndi amphamvu, koma iyeyo akakhala pakati pathu amaoneka wofooka+ ndipo nkhani zake n’zosagwira mtima.”+ 11  Munthu woteroyo adziwe kuti zimene tikunena m’makalata athu tili kwina, tidzachitanso zomwezo tikadzakhala pakati panu.+ 12  Pakuti sitidzayesa n’komwe kudziona ngati ndife ofanana ndi anthu enaake kapena kudziyerekezera ndi ena amene amadzikweza.+ Ndithudi anthu amenewo samvetsa kanthu kalikonse chifukwa akuyezana okhaokha pogwiritsira ntchito miyezo yawo yomwe, ndipo akudziyerekezera ndi iwo eni.+ 13  Koma ifeyo tidzadzitamandira, osati pa zinthu zimene zili kunja kwa malire amene tapatsidwa,+ koma pa zinthu zimene zili mkati mwa malire a gawo limene Mulungu anatipatsa pochita kutiyezera, limene analifikitsa mpaka kwanuko.+ 14  Choncho sitikupitirira malire a gawo lathu, ngati kuti gawolo silikufika kwa inu. Ayi ndithu, pakuti tinayamba ndife kufika kwanuko polengeza uthenga wabwino wonena za Khristu.+ 15  Sitikudzitamandira kunja kwa malire a gawo limene tinapatsidwa, podzitamandira chifukwa cha ntchito za munthu wina ayi,+ koma tili ndi chiyembekezo chakuti chikhulupiriro chanu chikadzawonjezeka,+ ntchito yathunso idzakula pakati panu, limene ndi gawo lathu.+ Ndiyeno tidzachitanso zowonjezereka, 16  polengeza uthenga wabwino kumayiko akutali kupitirira kwanuko,+ kuti tisadzitamande m’gawo la wina, mmene anakonzamo kale. 17  “Koma amene akudzitamandira, adzitamande mwa Yehova.”+ 18  Pakuti wodzikweza yekha si amene amavomerezedwa,+ koma amene Yehova+ wamuvomereza.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mwakuthupi.”