2 Akorinto 12:1-21

12  Ndiyenera kudzitama. Zoona, kudzitama si kopindulitsa. Koma tiyeni tisiye kaye nkhani imeneyi, tipite ku nkhani yokhudza masomphenya+ ndi mauthenga ochokera kwa Ambuye.  Ndikudziwa munthu wina wogwirizana ndi Khristu. Zaka 14 zapitazo, munthu ameneyu anakwatulidwira kumwamba kwachitatu. Kaya zimenezo zinachitika ali m’thupi kapena ali kunja kwa thupi sindikudziwa. Akudziwa ndi Mulungu.+  Zoonadi, ndikumudziwa munthu ameneyu. Kaya anakwatulidwa ali m’thupi kapena kunja kwa thupi,+ sindikudziwa. Akudziwa ndi Mulungu.  Iye anakwatulidwa n’kukalowa m’paradaiso,+ ndipo ali m’paradaisomo anamva mawu osatchulika, amene sikololeka munthu kuwanena.  Ndidzadzitamandira chifukwa cha munthu ameneyo, koma sindidzadzitamandira chifukwa cha ineyo, kupatulapo pa kufooka kwanga.+  Ngati ndingafune kudzitamandira, si kuti ndikhala wodzikweza,+ chifukwa ndikhala ndikunena choonadi. Koma sindikudzitamandira, chifukwa ndikufuna kuti inuyo mundiyamikire pa zinthu zokhazo zimene mukuona kapena kumva kwa ine.  Chifukwa cha kuchuluka kwa mauthenga amene anaululidwa kwa ine, aliyense asandiganizire koposa mmene ayenera kundiganizira. Chotero, kuti ndisadzikweze mopitirira muyezo,+ ndinapatsidwa munga m’thupi,+ mngelo wa Satana woti azindimenya nthawi zonse, kuti ndisadzikweze mopitirira muyezo.  Pa nkhaniyi, katatu+ konse ndinachonderera Ambuye kuti mungawu undichoke,  koma anandiuza motsimikiza kuti: “Kukoma mtima kwakukulu kumene ndakusonyeza n’kokukwanira,+ pakuti mphamvu yanga imakhala yokwanira iweyo ukakhala wofooka.”+ Choncho, ndidzadzitamandira mosangalala kwambiri pa kufooka kwanga,+ kuti mphamvu ya Khristu ikhalebe pamutu panga ngati hema. 10  Chotero ndimasangalala ndi kufooka, zitonzo, zosowa zanga, mazunzo ndi zovuta zina, chifukwa cha Khristu. Pakuti pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu.+ 11  Ndakhala wodzikweza tsopano. Ndinu mwandikakamiza+ kukhala wotero, popeza simunanene za zinthu zabwino zimene ndachita, ngakhale kuti munayenera kutero. Pakuti sindinachepe mwanjira ina iliyonse kwa atumwi anu apamwambawo,+ ngakhale kuti si ine kanthu m’maso mwanu.+ 12  Ndithudi inuyo munaona umboni wakuti ndine mtumwi,+ poona mmene ndinapiririra,+ komanso poona zizindikiro, zodabwitsa, ndi ntchito zamphamvu zimene ndinachita.+ 13  Kodi munakhala ochepa m’njira yotani kwa mipingo yonse? Mwina m’njira yoti ineyo sindinakhale katundu wolemetsa kwa inu.+ Chonde, ndikhululukireni cholakwa chimenechi. 14  Kanotu ndi kachitatu+ kukhala wokonzeka kubwera kwa inu, koma sindidzakhala katundu wolemetsa. Pakuti sindikufuna zinthu zanu,+ koma inuyo. Paja ana+ sayenera kusunga chuma kuti chidzathandize makolo awo m’tsogolo, koma makolo ndi amene ayenera kusungira ana awo.+ 15  Koma ineyo ndidzagwiritsa ntchito zinthu zanga zonse ndipo ndidzadzipereka ndi moyo wanga wonse chifukwa cha miyoyo yanu.+ Ngati ineyo ndimakukondani kwambiri chonchi, kodi inuyo mukuyenera kundikonda mochepa? 16  Mulimonse mmene zinakhalira, sindinakulemetseni.+ Ngakhale zili choncho, inuyo mukuti, “ndinakuchenjererani” ndi kukukolani “mwachinyengo.”+ 17  Koma sindinakuchenjerereni kudzera mwa aliyense wa anthu amene ndinawatumiza kwa inu, ndinatero ngati? 18  Tito ndinamuchonderera kuti abwere kwa inu ndipo ndinatumiza m’bale wina limodzi naye. Kodi Titoyo anakuchenjererani m’pang’ono pomwe ngati?+ Ayi ndithu sanatero. Tinayenda mumzimu umodzi,+ kodi si choncho? M’mapazi amodzimodzi, si choncho kodi? 19  Kodi nthawi yonseyi mwakhala mukuganiza kuti tikudzitchinjiriza pamaso panu? Tikulankhula pamaso pa Mulungu mogwirizana ndi Khristu. Komatu okondedwa, tikuchita zonse kuti tikulimbikitseni.+ 20  Ndikuopa kuti mwinamwake ndikadzafika,+ sindidzakupezani mmene ndikanafunira. Kwa inunso sindidzakhala mmene mukanafunira. M’malomwake, ndidzapeza ndewu, nsanje,+ kukwiyitsana, mikangano, miseche, manong’onong’o, kudzitukumula, ndi zisokonezo.+ 21  Mwina ndikadzabweranso, Mulungu wanga adzandichititsa manyazi pakati panu. Ndipo mwina ndidzalirira anthu ambiri amene anachimwa+ koma sanalape pa zonyansa zawo, dama*+ lawo, ndi khalidwe lawo lotayirira+ limene akhala akuchita.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 7.