2 Atesalonika 1:1-12

1  Ine Paulo, pamene ndili limodzi ndi Silivano ndi Timoteyo,+ ndikulembera mpingo wa Atesalonika wogwirizana ndi Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu, kuti:  Kukoma mtima kwakukulu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu,+ zikhale nanu.  Tiyeneradi kumayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu+ abale. N’koyenera kutero chifukwa chikhulupiriro chanu chikukula+ kwambiri, ndipo chikondi cha aliyense wa inu kwa mnzake chikuwirikiza.+  Choncho ifeyo timakunyadirani+ ku mipingo ya Mulungu chifukwa cha kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu pokumana ndi mazunzo ndi masautso onse amene mukulimbana nawo.+  Umenewu ndi umboni wakuti Mulungu amaweruza molungama,+ ndipo chifukwa cha zimenezi mwaonedwa kuti ndinu oyenerera ufumu wa Mulungu,+ umene mukuuvutikira.+  Chiweruzo cha Mulunguchi n’cholungama chifukwa akubwezera masautso kwa amene amakusautsani.+  Pa nthawi imene Ambuye Yesu adzaonekere*+ kuchokera kumwamba limodzi ndi angelo ake amphamvu+ m’moto walawilawi, inuyo amene panopo mukuvutika mudzapeza mpumulo pamodzi nafe.  Pa nthawi imeneyo adzabwezera chilango+ kwa anthu osadziwa Mulungu+ ndi kwa anthu osamvera uthenga wabwino+ wonena za Ambuye wathu Yesu.+  Amenewa adzawaweruza kuti alandire chilango+ cha chiwonongeko chamuyaya,+ kuwachotsa pamaso pa Ambuye ndi ku ulemerero wa mphamvu zake.+ 10  Adzatero pa nthawi imene adzabwere kudzalandira ulemerero mogwirizana ndi oyera ake.+ Pa tsiku limenelo, onse amene anakhulupirira mwa iye, adzamusirira ndi kumuyang’anitsitsa, chifukwa pakati panu, munakhulupirira umboni umene tinapereka. 11  Pa chifukwa chimenechi, ndithu timakupemphererani nthawi zonse. Timatero kuti Mulungu wathu akuoneni kuti ndinu oyenereradi kuitanidwa ndi iye.+ Mulunguyo achite mokwanira zinthu zonse zabwino zimene akufuna kuchita ndi mphamvu zake, ndipo achititse kuti ntchito zanu zachikhulupiriro zikhale zopindulitsa, 12  kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezeke mwa inu,+ ndi inu mwa iye,+ mogwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu+ kwa Mulungu wathu, ndi kwa Ambuye Yesu Khristu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “adzaululike.”