2 Mafumu 19:1-37

19  Mfumu Hezekiya+ itangomva zimenezi, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake+ n’kuvala chiguduli.+ Kenako inapita m’nyumba ya Yehova.+  Komanso, inatuma Eliyakimu+ amene anali woyang’anira banja la mfumu, Sebina+ mlembi, ndi akuluakulu a ansembe, onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi.+  Iwo anamuuza kuti: “Hezekiya wanena kuti, ‘Lero ndi tsiku la zowawa+ ndi lodzudzula,+ tsiku la mnyozo ndi mwano.+ Tili ngati mkazi amene watsala pang’ono kubereka,+ koma alibe mphamvu zoti aberekere.+  Mwina Yehova Mulungu amva+ mawu onse a Rabisake, amene mbuye wake mfumu ya Asuri yam’tuma, kuti adzatonze+ nawo Mulungu wamoyo. Ndipo mwina amulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva.+ Inuyo mupereke pemphero+ m’malo mwa otsalira+ amene alipo.’”  Choncho atumiki a Mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.+  Ndiyeno Yesaya anawauza kuti: “Mukauze mbuye wanu kuti, ‘Yehova wanena kuti:+ “Usachite mantha+ chifukwa cha mawu amene wamva, amene atumiki a mfumu ya Asuri andilankhulira monyoza.+  Ndiika maganizo mwa iye,+ kuti akamva nkhani inayake,+ abwerere kudziko lake. Ndipo mosalephera ndidzachititsa kuti akaphedwe ndi lupanga m’dziko lake.”’”+  Koma Rabisake+ anali atamva kuti mfumu ya Asuri yachoka ku Lakisi,+ choncho anabwerera kwa mfumuyo n’kukaipeza ikumenyana ndi Libina.+  Mfumuyo inamva kuti Tirihaka mfumu ya Itiyopiya wabwera kudzamenyana nayo. Choncho inatumizanso amithenga+ kwa Hezekiya n’kuwauza kuti: 10  “Amuna inu mukamuuze Hezekiya mfumu ya Yuda kuti, ‘Usalole Mulungu wako amene ukum’dalira kuti akunamize,+ ponena kuti: “Yerusalemu+ saperekedwa m’manja mwa mfumu ya Asuri.”+ 11  Iweyo wamva zimene mafumu a Asuri anachita kumayiko onse amene anawawononga.+ Ndiye kodi iweyo ukuona ngati upulumuka?+ 12  Kodi milungu+ ya mitundu imene makolo anga anaiwononga inawalanditsa? Kodi inalanditsa Gozani,+ Harana,+ Rezefi ndi ana a Edeni+ amene anali ku Tela-sara?+ 13  Ili kuti mfumu ya Hamati,+ mfumu ya Aripadi,+ ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu, Hena, ndi Iva?’”+ 14  Kenako Hezekiya anatenga kalatayo m’manja mwa amithengawo n’kuiwerenga.+ Pambuyo pake iye anapita nayo kunyumba ya Yehova n’kukaitambasula pamaso pa Yehova.+ 15  Ndiyeno Hezekiya anayamba kupemphera+ pamaso pa Yehova, kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli+ wokhala pa akerubi,+ inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse+ a padziko lapansi.+ Inuyo munapanga kumwamba+ ndi dziko lapansi.+ 16  Tcherani khutu lanu, inu Yehova, mumve.+ Tsegulani maso anu,+ inu Yehova, muone, ndipo imvani mawu a Senakeribu amene watumiza kudzatonza nawo+ Mulungu wamoyo. 17  N’zoonadi Yehova, kuti mafumu a Asuri awononga mitundu ndi mayiko awo.+ 18  Atentha milungu yawo pamoto, chifukwa sinali milungu,+ koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala, n’chifukwa chake anaiwononga. 19  Tsopano inu Yehova Mulungu wathu,+ chonde tipulumutseni+ m’manja mwake, kuti maufumu onse a padziko lapansi adziwe kuti inu Yehova, inu nokha ndiye Mulungu.”+ 20  Ndiyeno Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya, wakuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti,+ ‘Ndamva pemphero+ limene wapemphera kwa ine lokhudza Senakeribu mfumu ya Asuri.+ 21  Awa ndi mawu otsutsana naye amene Yehova wanena:“Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza+ ndipo wakuseka.+Kumbuyo kwako, mwana wamkazi wa Yerusalemu+ wakupukusira mutu.+ 22  Kodi ndani amene iwe wamutonza+ ndi kumulankhula monyoza?+Ndipo ndani amene iwe wam’kwezera mawu,+Ndi kum’kwezera maso ako m’mwamba?+Ndi Woyera wa Isiraeli!+ 23  Kudzera mwa amithenga ako+ watonza Yehova ndipo wanena kuti,+‘Ndi magaleta anga ankhondo ambiri, ine,+Ineyo ndidzakwera ndithu madera amapiri mpaka pamwamba.+Ndidzafika kumadera akutali kwambiri a Lebanoni+Ndipo ndidzadula mitengo yake ya mkungudza+ italiitali, ndi mitengo yake yabwino kwambiri yofanana ndi mkungudza.+Ndidzalowa kumalo ake okhala akutali kwambiri, kunkhalango yokongola.+ 24  Ndithu ineyo ndidzakumba zitsime ndi kumwa madzi achilendo,Ndidzaumitsa ndi mapazi anga ngalande zonse zamadzi za mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo.’+ 25  Kodi sunamve?+ Kuyambira nthawi zakale, izi n’zimene ndidzachite.+Ndinakonza zimenezi kuyambira masiku amakedzana.+Tsopano ndizichita.+Iweyo udzagwira ntchito yosandutsa mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, kukhala yopanda anthu ngati milu ya mabwinja.+ 26  Anthu okhala m’mizindayo adzafooka manja.+Adzachita mantha kwambiri ndiponso adzachita manyazi.+Adzakhala ngati zomera zakutchire, ndi udzu wanthete wobiriwira,+Ngati udzu womera padenga+ ukawauka ndi mphepo yotentha yakum’mawa.+ 27  Ukakhala phee, ukamatuluka,+ ndiponso ukamalowa, ine ndimadziwa bwino,+Ndimadziwanso ukandipsera mtima,+ 28  Chifukwa kundipsera mtima kwako+ ndi kufuula kwako zafika m’makutu mwanga,+Ndithu ndidzakola mphuno yako ndi ngowe yanga, ndipo ndidzamanga zingwe zanga pakamwa pako.+Kenako ndidzakukoka n’kukubweza kudzera njira imene unadutsa pobwera.”+ 29  “‘Ichi chidzakhala chizindikiro chanu:+ Chaka chino mudya mmera wa mbewu zimene zinagwera pansi.+ M’chaka chachiwiri mudzadya mbewu zongomera zokha, koma m’chaka chachitatu, anthu inu mudzabzale mbewu+ n’kukolola, ndipo mudzalime minda ya mpesa ndi kudya zipatso zake.+ 30  Anthu a nyumba ya Yuda amene adzapulumuke, amene adzatsale,+ ndithu adzazika mizu pansi n’kubereka zipatso m’mwamba.+ 31  Chifukwa anthu otsala adzachokera ku Yerusalemu,+ ndipo opulumuka adzachokera kuphiri la Ziyoni.+ Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+ 32  “‘N’chifukwa chake Yehova wanena izi zokhudza mfumu ya Asuri:+ “Sadzalowa mumzinda uno,+ kapena kuponyamo muvi,+ kapena kufikamo ndi chishango, kapenanso kumanga chiunda chomenyerapo nkhondo* pafupi ndi mpanda wa mzindawu atauzungulira.+ 33  Adzabwerera kudzera njira imene anadutsa pobwera, ndipo sadzalowa mumzinda uno, ndiwo mawu a Yehova.+ 34  Ndithu ndidzateteza+ mzinda uno kuti ndiupulumutse chifukwa cha ine mwini+ ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.”’”+ 35  Ndiyeno usiku umenewo, mngelo wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri+ n’kukapha asilikali 185,000.+ Anthu podzuka m’mawa, anangoona kuti onse aja ndi mitembo yokhayokha.+ 36  Choncho Senakeribu+ mfumu ya Asuri inachokako n’kubwerera+ kukakhala ku Ninive.+ 37  Pamene Senakeribu anali kugwada m’kachisi wa mulungu wake+ Nisiroki,+ ana ake Adarameleki ndi Sarezere anamupha ndi lupanga,+ iwo n’kuthawira kudziko la Ararati.+ Kenako Esari-hadoni+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.