2 Mafumu 21:1-26
21 Manase+ anali ndi zaka 12 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka 55 ku Yerusalemu. Mayi ake dzina lawo linali Hefiziba.
2 Iye anachita zoipa pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonyansa za mitundu+ imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa ana a Isiraeli.
3 Choncho iye anamanganso malo okwezeka amene Hezekiya bambo ake anachotsa.+ Anamanga maguwa ansembe a Baala n’kumanga mzati wopatulika, monga momwe Ahabu+ mfumu ya Isiraeli anachitira. Iye anayambanso kugwadira+ khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ n’kumazitumikira.+
4 Anamanga maguwa ansembe m’nyumba ya Yehova,+ imene ponena za iyo Yehova anati: “Ku Yerusalemu ndidzaikako dzina langa.”+
5 Iye anamangira maguwa ansembe khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ m’mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.+
6 Manase anatentha* mwana wake wamwamuna pamoto,+ ndipo ankachita zamatsenga,+ ankawombeza,*+ ndiponso anaika anthu olankhula ndi mizimu ndi olosera+ zam’tsogolo. Iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.
7 Komanso iye anaika m’nyumbayo chifaniziro+ cha mzati wopatulika chimene anapanga. Koma ponena za nyumba imeneyo,+ Yehova anauza Davide ndi Solomo mwana wake kuti: “M’nyumba iyi ndiponso mu Yerusalemu mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Isiraeli, ndidzaikamo dzina langa mpaka kalekale.+
8 Sindidzachititsanso phazi la Isiraeli kuchoka panthaka imene ndinapatsa makolo awo,+ ngati atayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zonse zimene ndinawalamula,+ ndiponso mogwirizana ndi chilamulo chonse chimene Mose mtumiki wanga anawalamula.”
9 Koma sanamvere,+ ndipo Manase anapitiriza kunyengerera anthu kuti achite zinthu zoipa+ kuposa zimene inkachita mitundu+ yomwe Yehova anaiwononga pamaso pa ana a Isiraeli.
10 Yehova anapitiriza kulankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri,+ kuti:
11 “Manase+ mfumu ya Yuda yachita zinthu zonyansazi.+ Yachita zinthu zoipa kwambiri kuposa zonse zimene anachita Aamori+ amene analiko iye asanakhale mfumu. Iye wachimwitsa ngakhale Yuda+ ndi mafano ake onyansa.
12 Pa chifukwa chimenechi Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndikubweretsa tsoka pa Yerusalemu+ ndi Yuda loti aliyense akamva, adzadabwa kwambiri.*+
13 Ndithu ndidzayeza Yerusalemu ndi chingwe chimene ndinayezera+ Samariya,+ ndiponso ndidzamuyeza ndi thabwa lowongolera limene ndinayezera nyumba ya Ahabu.+ Yerusalemu ndidzam’pukuta+ mpaka kuyera mbee ngati mmene munthu amapukutira mbale yolowa mpaka kuyera mbee, n’kuitembenuza.+
14 Ndidzataya otsala+ a cholowa changa+ n’kuwapereka m’manja mwa adani awo. Iwo adzakhala zofunkha ndipo katundu wawo adzalandidwa ndi adani awo onse.+
15 Ndidzachita zimenezi chifukwa chakuti iwo anachita zoipa pamaso panga ndipo akhala akundikwiyitsa kuyambira tsiku limene makolo awo anatuluka ku Iguputo mpaka lero.’”+
16 Manase anakhetsanso magazi osalakwa ochuluka zedi,+ mpaka magaziwo anadzaza nawo Yerusalemu kuyambira koyambirira mpaka kumapeto, kuwonjezera pa tchimo lake limene anachimwitsa nalo Yuda mwa kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+
17 Nkhani zina zokhudza Manase ndi zonse zimene anachita, ndiponso tchimo lake limene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda.
18 Pomalizira pake, Manase anagona pamodzi ndi makolo ake+ ndipo anaikidwa m’manda m’munda wa panyumba pake, m’munda wa Uziza.+ Kenako Amoni mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.
19 Amoni+ anali ndi zaka 22 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira zaka ziwiri+ ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Yotiba, ndipo dzina lawo linali Mesulemeti mwana wa Haruzi.
20 Amoni anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, monga anachitira Manase bambo ake.+
21 Iye anapitiriza kuyenda m’njira zonse zimene bambo ake anayendamo,+ ndipo anapitiriza kutumikira mafano onyansa+ amene bambo ake anawatumikira, n’kumawagwadira.
22 Chotero anasiya Yehova,+ Mulungu wa makolo ake, ndipo sanayende m’njira ya Yehova.+
23 Pomaliza pake, atumiki a mfumu Amoni anam’chitira chiwembu n’kumupha+ m’nyumba mwake momwe.
24 Koma anthu a m’dzikolo anapha anthu onse amene anachitira chiwembu+ Mfumu Amoni. Kenako anthu a m’dzikolo anaika Yosiya+ mwana wake kuti akhale mfumu m’malo mwake.
25 Nkhani zina zokhudza Amoni ndi zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda.
26 Chotero anamuika m’manda ake m’munda wa Uziza,+ ndipo Yosiya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.
Mawu a M'munsi
^ Mawu akuti “kuwombeza” akutanthauza kufuna kudziwa zam’tsogolo, kapena kufufuza ngati zochitika kapena zinthu zinazake zikulosera kuti m’tsogolo mudzachitika zabwino kapena zoipa.
^ Mawu ake enieni, “Kudutsitsa pamoto.”
^ Mawu ake enieni, “Adzamva kubayabaya m’makutu mwake.”