2 Mbiri 1:1-17

1  Solomo mwana wa Davide anapitiriza kukhala wamphamvu mu ufumu wake.+ Yehova Mulungu wake anali naye,+ ndipo anapitiriza kumukulitsa kuposa wina aliyense.+  Tsopano Solomo anaitanitsa Aisiraeli onse, atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ atsogoleri a magulu a anthu 100,+ oweruza,+ ndi akuluakulu onse a Isiraeli+ yense, amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo.+  Kenako Solomo ndi mpingo wonsewo anapitira limodzi kumalo okwezeka a ku Gibeoni.+ Anapita kumeneko chifukwa ndi kumene kunali chihema chokumanako+ cha Mulungu woona, chimene Mose mtumiki+ wa Yehova anapanga m’chipululu.  Koma Davide anali atachotsa likasa+ la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu+ n’kukaliika kumalo amene iye anakonza,+ pakuti anali atamanga hema wa likasalo ku Yerusalemu.+  Ndipo guwa lansembe lamkuwa+ limene Bezaleli+ mwana wa Uri mwana wa Hura+ anapanga, anali ataliika patsogolo pa chihema chopatulika cha Yehova. Choncho Solomo ndi mpingowo anafunsira paguwalo monga mwa nthawi zonse.  Ndiyeno kumeneko Solomo anapereka nsembe pamaso pa Yehova paguwa lansembe lamkuwalo limene linali kuchihema chokumanako. Iye anapereka nsembe zopsereza 1,000 paguwalo.+  Usiku wa tsiku limenelo, Mulungu anaonekera kwa Solomo ndi kumuuza kuti: “Tandiuza, ukufuna ndikupatse chiyani?”+  Solomo atamva zimenezi anauza Mulungu kuti: “Inu ndinu amene mwasonyeza kukoma mtima kosatha kwa Davide bambo anga,+ ndipo mwandiika kukhala mfumu m’malo mwake.+  Tsopano inu Yehova Mulungu, kwaniritsani+ lonjezo limene munapereka kwa Davide bambo anga. Pakuti ndinu amene mwandiika kukhala mfumu+ ya anthuwa amene ndi ochuluka kwambiri ngati fumbi lapadziko lapansi.+ 10  Mundipatse nzeru ndi luntha lodziwa zinthu+ kuti ndizitha kutsogolera+ anthuwa, pakuti ndani angaweruze anthu anu ochulukawa?”+ 11  Pamenepo Mulungu anauza Solomo kuti: “Chifukwa chakuti zimenezi ndi zimene zili mumtima mwako+ ndipo sunapemphe katundu, chuma ndi ulemu kapenanso moyo wa anthu amene amadana nawe, sunapemphenso kuti ukhale ndi moyo masiku ambiri,+ koma wapempha kuti ukhale ndi nzeru ndi luntha lodziwa zinthu kuti uweruze anthu anga amene ndakupatsa kuti ukhale mfumu yawo,+ 12  upatsidwa nzeru ndi luntha lodziwa zinthu.+ Ndikupatsanso katundu, chuma, ndi ulemu zochuluka kwambiri kuposa zimene anali nazo mafumu amene anakhalako iwe usanakhale,+ ndiponso zoposa zimene aliyense wobwera pambuyo pako adzakhale nazo.”+ 13  Zitatero, Solomo anabwerera ku Yerusalemu kuchokera kumalo okwezeka a ku Gibeoni,+ kuchihema chokumanako,+ ndipo anapitiriza kulamulira Isiraeli.+ 14  Ndiyeno Solomo anali kusonkhanitsa magaleta* ndi mahatchi* ankhondo, moti anakhala ndi magaleta 1,400 ndi mahatchi ankhondo 12,000.+ Zimenezi anali kuzisunga m’mizinda yosungiramo magaleta+ ndiponso pafupi ndi mfumuyo ku Yerusalemu. 15  Mfumuyo inachititsa kuti ku Yerusalemu siliva ndi golide akhale wochuluka kwambiri ngati miyala,+ ndiponso kuti matabwa a mkungudza akhale ochuluka kwambiri ngati mitengo yamkuyu+ ya ku Sefela.+ 16  Panalinso mahatchi amene Solomo anali kugula kuchokera ku Iguputo,+ ndipo gulu la amalonda a mfumu ndilo linali kugula mahatchiwo m’magulumagulu.+ 17  Nthawi ndi nthawi anali kugula galeta lochokera ku Iguputo pamtengo wa ndalama zasiliva 600. Hatchi anali kuigula pamtengo wa ndalama zasiliva 150. Umu ndi mmene mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a ku Siriya+ anali kuchitira. Mafumuwa anali kugwiritsa ntchito amalondawo pogula zinthuzo.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati, “mahosi” kapena “akavalo.”