2 Mbiri 13:1-22
13 M’chaka cha 18 cha Mfumu Yerobowamu, Abiya anayamba kulamulira Yuda.+
2 Iye analamulira zaka zitatu ku Yerusalemu. Mayi ake dzina lawo linali Mikaya+ mwana wa Uriyeli wa ku Gibeya.+ Kenako pakati pa Abiya ndi Yerobowamu panachitika nkhondo.+
3 Choncho Abiya anapita kukamenya nkhondoyo ndi gulu la amuna amphamvu ankhondo+ osankhidwa mwapadera okwanira 400,000. Yerobowamu nayenso anapita kukamenyana ndi Abiya ndipo anapita ndi asilikali 800,000. Amenewa anali amuna amphamvu ndi olimba mtima osankhidwa mwapadera, ndipo anakafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+
4 Tsopano Abiya anaimirira paphiri la Zemaraimu limene lili m’dera lamapiri la Efuraimu,+ n’kunena kuti: “Tamvera, iwe Yerobowamu ndi Aisiraeli onsewo.
5 Kodi simukudziwa kuti Yehova Mulungu wa Isiraeli anapereka ufumu kwa Davide+ kuti azilamulira Isiraeli mpaka kalekale?+ Simukudziwa kodi kuti anaupereka kwa iye ndi ana ake+ pochita naye pangano losatha?*+
6 Koma Yerobowamu+ mwana wa Nebati, amene anali mtumiki+ wa Solomo mwana wa Davide, anapanduka+ n’kuukira mbuye wake.+
7 Ndipo anthu osowa chochita+ ndi opanda pake+ anasonkhana kumbali yake. Pamapeto pake iwo anakhala amphamvu kuposa Rehobowamu+ mwana wa Solomo pamene Rehobowamuyo anali wamng’ono komanso wamantha,+ ndipo sanathe kulimbana nawo.
8 “Tsopano anthu inu mukuganiza zolimbana ndi ufumu wa Yehova umene uli m’manja mwa ana a Davide,+ popeza ndinu khamu lalikulu+ ndipo muli ndi ana a ng’ombe agolide amene Yerobowamu anakupangirani kuti akhale milungu yanu.+
9 Kodi simunathamangitse ansembe a Yehova,+ omwe ndi ana a Aroni, komanso Alevi? Ndipo kodi simukudziikira ansembe ngati mmene amachitira anthu a mayiko ena?+ Aliyense amene wabwera n’kudziika pa udindo waunsembe mwa kupereka ng’ombe yaing’ono yamphongo ndi nkhosa zamphongo 7, amakhala wansembe wa mafano omwe si milungu.+
10 Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu+ ndipo sitinamusiye. Ansembe, omwe ndi ana a Aroni, akutumikira Yehova, ndiponso Alevi akugwira ntchito yawo.+
11 Iwo akufukiza nsembe zopsereza kwa Yehova m’mawa uliwonse ndi madzulo alionse.+ Akufukizanso mafuta onunkhira+ ndipo mikate yosanjikiza ili patebulo la golide woyenga bwino.+ Tilinso ndi choikapo nyale chagolide+ ndi nyale zake zimene amayatsa madzulo alionse.+ Tikuchita zimenezi chifukwa tikukwaniritsa udindo wathu+ kwa Yehova Mulungu wathu, koma inuyo mwamusiya.+
12 Taonani, ife patsogolo pathu pali Mulungu woona+ ndi ansembe ake,+ ndi malipenga+ otiitanira ku nkhondo yomenyana nanu. Inu ana a Isiraeli, musamenyane ndi Yehova Mulungu wa makolo anu,+ chifukwa simupambana.”+
13 Pamenepo Yerobowamu anatumiza asilikali kuti akawabisalire kumbuyo, choncho Yerobowamuyo ndi asilikali ake anakhala kutsogolo kwa Ayuda ndipo obisalawo anali kumbuyo kwa Ayudawo.+
14 Ayudawo atatembenuka, anangoona kuti adani awo ali kumbuyo ndi kutsogolo kwawo.+ Choncho anayamba kufuulira Yehova+ pamene ansembe anali kuliza malipenga mokweza.
15 Kenako amuna a Yuda anayamba kufuula mfuu ya nkhondo.+ Atafuula mfuu ya nkhondoyo, Mulungu woona anagonjetsa+ Yerobowamu ndi Aisiraeli onse pamaso pa Abiya+ ndi Ayuda.
16 Kenako ana a Isiraeli anayamba kuthawa pamaso pa Ayuda, koma Mulungu anawapereka m’manja mwa Ayudawo.+
17 Abiya ndi anthu ake anapha Aisiraeli ambirimbiri. Aisiraeliwo anapitirira kuphedwa mpaka ophedwawo anakwana amuna 500,000 osankhidwa mwapadera.
18 Choncho ana a Isiraeli anachititsidwa manyazi pa nthawi imeneyo, koma ana a Yuda anapambana chifukwa anadalira+ Yehova Mulungu wa makolo awo.
19 Abiya anapitiriza kuthamangitsa Yerobowamu ndipo anamulanda mizinda yake. Analanda Beteli+ ndi midzi yake yozungulira, Yesana ndi midzi yake yozungulira, ndiponso Efuraini ndi midzi yake yozungulira.+
20 Yerobowamu sanakhalenso ndi mphamvu+ m’masiku a Abiya, ndipo Yehova anamukantha+ moti anafa.
21 Abiya anapitiriza kulimbitsa ufumu wake.+ M’kupita kwa nthawi, anakwatira akazi 14+ ndipo anabereka ana aamuna 22+ ndi aakazi 16.
22 Nkhani zina zokhudza Abiya, njira zake ndi mawu ake, zinalembedwa m’buku la ndemanga la mneneri Ido.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “pangano la mchere.”