2 Mbiri 14:1-15
14 Pomalizira pake, Abiya anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide.+ Kenako Asa+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. M’masiku ake, m’dzikolo munalibe chosokoneza chilichonse+ kwa zaka 10.
2 Asa anachita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake.
3 Choncho iye anachotsa maguwa ansembe achilendo,+ anagwetsa malo okwezeka,+ anaphwanya zipilala zopatulika+ ndi kudula mizati yopatulika.+
4 Kuwonjezera apo, anauza Ayuda kuti afunefune+ Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kutsatira chilamulo.+
5 Iye anachotsa malo okwezeka ndi maguwa ofukizirapo zonunkhira+ m’mizinda yonse ya Yuda, ndipo ufumuwo unapitiriza kukhala wopanda chosokoneza chilichonse+ mu ulamuliro wake.
6 Kenako anamanga mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri m’dziko la Yuda,+ chifukwa m’dzikolo munalibe chosokoneza chilichonse, komanso palibe anachita naye nkhondo pa zaka zimenezi, chifukwa Yehova anam’patsa mpumulo.+
7 Choncho iye anauza Ayuda kuti: “Tiyeni timange mizindayi ndi mipanda+ yoizungulira. Timangenso nsanja+ ndipo tipange makomo a zitseko ziwiriziwiri ndi mipiringidzo.+ Malo m’dzikoli akadalipo chifukwa tafunafuna Yehova Mulungu wathu.+ Tam’funafuna ndipo watipatsa mpumulo pakati pa adani athu onse otizungulira.”+ Chotero iwo anamangadi ndipo zinthu zinawayendera bwino.+
8 Asa anakhala ndi gulu lankhondo lonyamula zishango zazikulu+ ndi mikondo ing’onoing’ono,+ la asilikali 300,000 a fuko la Yuda.+ Analinso ndi asilikali onyamula zishango zazing’ono+ ndi odziwa kupinda uta okwanira 280,000+ a fuko la Benjamini. Onsewa anali amuna amphamvu ndi olimba mtima.
9 Pambuyo pake Zera Mwitiyopiya+ anabwera kudzamenyana nawo ali ndi gulu lankhondo la asilikali 1,000,000+ ndi magaleta 300, ndipo anafika ku Maresha.+
10 Asa anapita kukamenyana naye ndipo iwo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo m’chigwa cha Sefata ku Maresha.
11 Tsopano Asa anayamba kupemphera kwa Yehova Mulungu wake,+ kuti: “Inu Yehova mukafuna kuthandiza, zilibe kanthu kuti anthuwo ndi ambiri kapena ndi opanda mphamvu.+ Tithandizeni Yehova Mulungu wathu chifukwa tikudalira inu,+ ndipo tabwera m’dzina lanu+ kudzamenyana ndi khamuli. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu.+ Musalole kuti munthu akuposeni mphamvu.”+
12 Atatero, Yehova anagonjetsa+ Aitiyopiyawo pamaso pa Asa ndi Ayuda, ndipo Aitiyopiyawo anayamba kuthawa.
13 Asa ndi anthu amene anali naye anawathamangitsa mpaka kukafika ku Gerari,+ ndipo Aitiyopiyawo anapitiriza kuphedwa mpaka palibe amene anatsala ndi moyo, popeza Yehova+ ndi gulu lake+ anawagonjetseratu. Pambuyo pake, anthuwo anatenga zofunkha zochuluka zedi.+
14 Kuwonjezera apo, anawononga mizinda yonse yozungulira Gerari chifukwa mantha+ ochokera kwa Yehova anagwira anthu a m’mizindayo. Iwo anafunkha mizinda yonseyo, chifukwa munali zambiri zoti afunkhe.+
15 Anawononganso mahema+ a anthu okhala ndi ziweto n’kutengamo+ ziweto zambiri ndi ngamila.+ Atatero anabwerera ku Yerusalemu.