2 Mbiri 19:1-11
19 Yehosafati mfumu ya Yuda anabwerera mu mtendere+ kunyumba kwake ku Yerusalemu.
2 Tsopano Yehu+ mwana wa Haneni+ wamasomphenya,+ anapita kukaonekera kwa Mfumu Yehosafati ndipo anaifunsa kuti: “Kodi chithandizo chiyenera kuperekedwa+ kwa oipa, ndipo kodi muyenera kukonda anthu odana+ ndi Yehova?+ Chifukwa cha zimenezi Yehova wakukwiyirani.+
3 Komabe, pali zinthu zabwino+ zimene zapezeka mwa inu, chifukwa mwachotsa mizati yopatulika m’dzikoli,+ ndipo mwakonza mtima wanu kuti mufunefune Mulungu woona.”+
4 Yehosafati anapitiriza kukhala ku Yerusalemu. Iye anayambanso kupita pakati pa anthu, kuyambira ku Beere-seba+ mpaka kudera lamapiri la Efuraimu,+ kuti awabwezere kwa Yehova Mulungu wa makolo awo.+
5 Anaika oweruza m’dziko lonselo, mumzinda ndi mzinda, m’mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+
6 Ndiyeno anauza oweruzawo kuti: “Samalani zochita zanu+ chifukwa simukuweruzira munthu koma mukuweruzira Yehova,+ ndipo iye ali nanu pa ntchito yoweruzayi.+
7 Tsopano mantha+ a Yehova akugwireni.+ Samalani mmene mukuchitira+ chifukwa Yehova Mulungu wathu si wopanda chilungamo+ kapena watsankho,+ ndipo salandira chiphuphu.”+
8 Ku Yerusalemu nakonso Yehosafati anaikako Alevi ena,+ ansembe,+ ndi ena mwa atsogoleri a nyumba za makolo+ a Isiraeli, kuti azionetsetsa kuti anthu akutsatira chilamulo+ cha Yehova ndi kuti aziweruza milandu+ ya anthu a ku Yerusalemu.
9 Kuwonjezera apo, anawalamula kuti: “Muzichita zimenezi moopa+ Yehova ndi mokhulupirika ndiponso ndi mtima wathunthu.
10 Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene akukhala m’mizinda yawo, wokhudza kukhetsa magazi,+ chilamulo,+ ndi zigamulo,+ muziwachenjeza kuti asalakwire Yehova kuopera kuti mkwiyo wa Mulungu+ ungakuyakireni inuyo ndi abale anu. Muzichita zimenezi n’cholinga choti musapalamule mlandu.
11 Ndakupatsani wansembe wamkulu Amariya kuti azisamalira nkhani iliyonse yokhudza Yehova.+ Zebadiya mwana wa Isimaeli mtsogoleri wa nyumba ya Yuda aziyang’anira nkhani iliyonse yokhudza mfumu. Ndakupatsaninso Alevi kuti akhale oyang’anira anu. Khalani olimba mtima+ ndipo gwirani ntchitoyi. Yehova+ adalitse zabwino zimene muzichita.”+