2 Mbiri 2:1-18

2  Tsopano Solomo analamula kuti amange nyumba+ ya dzina la Yehova,+ ndi nyumba yachifumu ya Solomoyo.+  Chotero Solomo anasankha amuna 70,000 kuti akhale onyamula katundu, ndi ena 80,000 kuti akhale osema miyala kumapiri.+ Anasankhanso amuna 3,600 kuti akhale owayang’anira.+  Ndipo Solomo anatumiza uthenga kwa Hiramu+ mfumu ya Turo, kuti: “Monga momwe munachitira ndi Davide+ bambo anga pomawatumizira mitengo ya mkungudza kuti amangire nyumba yawo yokhalamo . . .  ine ndikumanga+ nyumba ya dzina+ la Yehova Mulungu wanga kuti ndiipatule+ ikhale yake. Ndikufuna kuti ndizifukiziramo mafuta onunkhira+ pamaso pake, ndi kuti nthawi zonse muzikhala mkate wosanjikiza.+ Ndiponso m’nyumbayo ndiziperekeramo nsembe zopsereza m’mawa ndi madzulo+ pa masabata,+ pa masiku okhala mwezi,+ ndi pa nyengo ya zikondwerero+ za Yehova Mulungu wathu. Zimenezi zizichitika mu Isiraeli mpaka kalekale.*+  Nyumba imene ndikumangayi idzakhala yogometsa,+ pakuti Mulungu wathu ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse.+  Ndipo ndani angakhale ndi mphamvu zomangira Mulunguyo nyumba?+ Pakuti kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, ndi kosakwanira kuti akhaleko.+ Ndiye ine ndine ndani+ kuti ndimumangire nyumba, kupatulapo yofukiziramo nsembe yautsi pamaso pake?+  Choncho nditumizireni munthu waluso pa ntchito zagolide, zasiliva, zamkuwa,+ zachitsulo, ndiponso waluso pa ntchito za ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira ndi wabuluu. Munthuyo akhalenso wodziwa kujambula ndi kulemba mochita kugoba, kuti adzagwire ntchito pamodzi ndi anthu aluso amene ndili nawo kuno ku Yuda ndi ku Yerusalemu, omwe Davide bambo anga anawasankha.+  Munditumizirenso matabwa a mitengo ya mkungudza,+ mitengo ina yofanana ndi mkungudza,+ ndiponso a mitengo ya m’bawa+ kuchokera ku Lebanoni,+ popeza ndikudziwa bwino kuti antchito anu ndi akatswiri odziwa kudula mitengo ya ku Lebanoni,+ (antchito anga adzagwira ntchito pamodzi ndi antchito anu,)  kuti andikonzere matabwa ambirimbiri, chifukwa nyumba imene ndikumanga idzakhaladi yaikulu ndi yochititsa kaso. 10  Ineyo ndipereka chakudya cha antchito anu otola nkhuni ndi odula mitengo. Ndipereka tirigu wokwanira makori* 20,000,+ balere makori 20,000, vinyo mitsuko* 20,000,+ ndi mafuta mitsuko 20,000.” 11  Hiramu mfumu ya Turo+ atamva, analemba kalata ndi kuitumiza kwa Solomo, kuti: “Popeza kuti Yehova anakonda+ anthu ake, waika inu kukhala mfumu yawo.”+ 12  Kenako Hiramu anapitiriza kuti: “Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi,+ chifukwa wapereka kwa Davide mfumu mwana wanzeru, wochenjera, ndi wozindikira,+ yemwe amangire Yehova nyumba ndi kudzimangira nyumba ya ufumu wake.+ 13  Tsopano ndikutumiza munthu waluso ndi wozindikira, dzina lake Hiramu-abi.+ 14  Ameneyu ndi mwana wa mayi winawake wa fuko la Dani, koma bambo ake anali a ku Turo. Iye ndi wodziwa ntchito zagolide, zasiliva, zamkuwa,+ zachitsulo, zamiyala,+ ndi zamatabwa. Amadziwanso ntchito za ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira+ ndi utoto wabuluu,+ komanso ntchito za nsalu+ zabwino kwambiri ndi zofiira.+ Iye amadziwanso ntchito zamtundu uliwonse zojambula ndi kulemba mochita kugoba.+ Amadziwanso ntchito zokonza zipangizo zamtundu uliwonse+ zimene angapatsidwe kuti achite pamodzi ndi anthu anu aluso ndi anthu aluso a mbuye wanga Davide bambo anu. 15  Ndipo tirigu, balere, mafuta, ndi vinyo, zimene inu mbuye wanga mwalonjeza, zitumizeni kwa ife akapolo anu.+ 16  Ife tidula mitengo yonse+ imene mukufunayo+ kuchokera ku Lebanoni, ndipo tiziimanga pamodzi m’maphaka oyandama n’kuitumiza kwa inu panyanja+ kukafika ku Yopa.+ Inu muzikaitengera kumeneko kupita nayo ku Yerusalemu.” 17  Kenako Solomo anawerenga amuna onse amene anali alendo m’dziko la Isiraeli.+ Anachita zimenezi pambuyo pa ntchito yowerenga alendowo imene Davide bambo ake anachita.+ Ndipo panapezeka amuna okwanira 153,600. 18  Choncho iye anasankhapo amuna 70,000 kuti akhale onyamula katundu,+ amuna 80,000 kuti akhale osema miyala+ kumapiri, ndi amuna 3,600 kuti akhale oyang’anira anthuwo pa ntchito yawo.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.