2 Mbiri 24:1-27
24 Yehoasi anali ndi zaka 7 pamene anayamba kulamulira.+ Iye analamulira zaka 40 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Beere-seba+ ndipo dzina lawo linali Zibiya.
2 Yehoasi+ anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova,+ masiku onse a wansembe Yehoyada.+
3 Yehoyada anapezera Yehoasi akazi awiri, choncho iye anabereka ana aamuna ndi aakazi.+
4 Pambuyo pake Yehoasi anafunitsitsa mumtima mwake kukonzanso nyumba ya Yehova.+
5 Chotero anasonkhanitsa ansembe+ ndi Alevi n’kuwauza kuti: “Pitani m’mizinda ya Yuda kukasonkhanitsa ndalama kwa Aisiraeli onse kuti muzikonzera+ nyumba ya Mulungu wanu chaka ndi chaka.+ Chitani zimenezi mwachangu.” Koma Aleviwo sanachite zimenezo mwachangu.+
6 Ndiyeno mfumuyo inaitana mtsogoleri wawo Yehoyada n’kumufunsa kuti:+ “Bwanji simunafunse Alevi kuti afotokoze za nkhani yobweretsa msonkho wopatulika kuchokera kwa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu? Si paja anayenera kubweretsa msonkho umene Mose+ mtumiki wa Yehova analamula, msonkho wopatulika wa mpingo wa Isiraeli wogwiritsa ntchito pachihema cha Umboni?+
7 Pajatu ana+ a Ataliya mkazi woipa uja anathyola nyumba ya Mulungu woona,+ n’kutenga zinthu zonse zopatulika+ za m’nyumba ya Yehovayo n’kukazipereka kwa Abaala.”+
8 Tsopano mfumuyo inawauza zochita ndipo anapanga bokosi+ n’kuliika panja, pachipata cha nyumba ya Yehova.
9 Atatero anauza anthu onse a ku Yuda ndi ku Yerusalemu kuti abweretse kwa Yehova msonkho wopatulika+ umene Mose+ mtumiki wa Mulungu woona analamula Aisiraeli m’chipululu.
10 Akalonga onse+ ndi anthu onse anayamba kusangalala,+ ndipo anali kubweretsa ndalama za msonkhowo n’kumaziponya m’bokosi+ lija kufikira aliyense anapereka.
11 Pa nthawi yoyenera, Alevi+ ankanyamula bokosilo n’kupita nalo kwa mfumu. Iwo akangoona kuti muli ndalama zambiri,+ mlembi+ wa mfumu ndi mtumiki wa wansembe wamkulu ankabwera n’kukhuthula ndalama zimene zinali m’bokosilo, n’kulinyamula kukalibwezeretsa pamalo ake. Ankachita zimenezi tsiku ndi tsiku moti anasonkhetsa ndalama zambiri.
12 Mfumuyo ndi Yehoyada ankapereka ndalamazo kwa anthu ogwira ntchito+ yokonza nyumba ya Yehova.+ Iwowo analemba ntchito anthu osema miyala+ ndi amisiri+ okonza nyumba ya Yehova.+ Analembanso ntchito amisiri a mkuwa ndi a zitsulo oti akonze nyumba ya Yehova.+
13 Anthu ogwira ntchitowo anayamba ntchito yawo+ ndipo ntchito yokonza nyumbayo inali kuyenda bwino. Pomaliza pake anakonza nyumba ya Mulungu woona kuti ikhale mmene inayenera kukhalira ndipo anailimbitsa.
14 Atangomaliza ntchitoyo anabweretsa ndalama zotsalazo kwa mfumu ndi Yehoyada. Ndi ndalamazo, iwo anapanga ziwiya za nyumba ya Yehova ndiponso ziwiya zogwiritsira ntchito pa utumiki+ ndi popereka zopereka. Anapanganso makapu+ ndi ziwiya zagolide+ ndi siliva, ndipo nsembe zopsereza+ zinayamba kuperekedwa nthawi zonse m’nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.
15 Yehoyada anakalamba atakhutira ndi moyo wake wa zaka zambiri,+ ndipo anamwalira ali ndi zaka 130.
16 Choncho anamuika m’manda a mafumu mu Mzinda wa Davide,+ chifukwa anachita zabwino mu Isiraeli+ ndiponso kwa Mulungu woona ndi nyumba Yake.
17 Yehoyada atamwalira, akalonga+ a Yuda anabwera n’kudzagwada pamaso pa mfumu ndipo mfumuyo inawamvera.+
18 M’kupita kwa nthawi iwo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo awo n’kuyamba kutumikira mizati yopatulika+ ndiponso mafano.+ Chotero mkwiyo wa Mulungu unagwera Yuda ndi Yerusalemu chifukwa cha kupalamula kwawoko.+
19 Yehova anapitiriza kutumiza aneneri+ pakati pawo kuti awabwezere kwa iye. Aneneriwo anapitiriza kupereka umboni wowatsutsa, koma sanamvere.+
20 Tsopano mzimu wa Mulungu+ unadzaza+ Zekariya+ mwana wa wansembe Yehoyada+ ndipo anaimirira pamalo okwera, n’kuyamba kuuza anthuwo kuti: “Mulungu woona wanena kuti, ‘N’chifukwa chiyani mukuphwanya malamulo a Yehova? Kodi simukuona kuti zinthu sizikukuyenderani bwino?+ Popeza mwamusiya Yehova, iyenso akusiyani.’”+
21 Pamapeto pake anthuwo anam’konzera chiwembu+ ndipo anam’ponya miyala+ pabwalo la nyumba ya Yehova, atalamulidwa ndi mfumu.
22 Mfumu Yehoasi sanakumbukire kukoma mtima kosatha kumene Yehoyada bambo a Zekariya anamusonyeza,+ ndipo anapha mwana wawo yemwe pakufa ananena kuti: “Yehova aone zimene mwachitazi ndi kubwezera.”+
23 Kumayambiriro+ kwa chaka chotsatira, gulu lankhondo la ku Siriya+ linabwera kudzamenyana naye,+ ndipo linalowa mu Yuda ndi Yerusalemu. Asilikaliwo anachotsa akalonga onse+ pakati pa anthuwo n’kuwapha, ndipo zinthu zonse zimene anafunkha anazitumiza kwa mfumu ya ku Damasiko.+
24 Gulu lankhondo la Siriyalo linalowa m’dzikolo ndi amuna ochepa,+ koma Yehova anapereka m’manja mwawo gulu lankhondo lalikulu kwambiri+ popeza iwo anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo. Asiriyawo anaperekanso chiweruzo kwa Yehoasi.+
25 Asilikaliwo atachoka (popeza anamusiya akuvutika kwambiri),+ atumiki ake anam’konzera chiwembu+ chifukwa cha magazi+ a ana a wansembe Yehoyada+ ndipo anamuphera pabedi+ lake. Kenako anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide+ koma sanamuike m’manda a mafumu.+
26 Amene anam’konzera chiwembucho ndi awa: Zabadi+ yemwe mayi ake anali Simeyati Muamoni ndi Yehozabadi yemwe mayi ake anali Simiriti Mmowabu.
27 Nkhani zokhudza ana ake, mauthenga ochuluka omutsutsa,+ ndi ntchito yokonzanso maziko+ a nyumba ya Mulungu woona, zinalembedwa m’ndemanga za Buku+ la Mafumu. Kenako Amaziya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.