2 Mbiri 30:1-27
30 Hezekiya anatumiza uthenga kwa Aisiraeli+ ndi Ayuda onse ndipo analembanso makalata ku Efuraimu+ ndi ku Manase,+ kuti abwere kunyumba ya Yehova+ ku Yerusalemu kudzachita pasika+ kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli.
2 Koma mfumuyo, akalonga ake+ ndi mpingo wonse+ ku Yerusalemu anagwirizana zoti achite pasikayo m’mwezi wachiwiri.+
3 Iwo sanathe kuchita pasikayo m’mwezi woyamba+ popeza ansembe amene anadziyeretsa sanali okwanira+ komanso anthuwo sanasonkhane ku Yerusalemu.
4 Nkhaniyi inakomera mfumu ndi mpingo wonsewo.+
5 Choncho anagwirizana kuti alengeze+ zimenezi mu Isiraeli yense kuyambira ku Beere-seba+ mpaka ku Dani,+ ndipo auze anthuwo kuti abwere ku Yerusalemu adzachite pasika kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli, chifukwa m’mbuyomo, iwo sanali kusonkhana onse pamodzi+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.+
6 Ndiyeno asilikali othamanga+ amene anatenga makalata ochokera kwa mfumu ndi kwa akalonga ake,+ anapita mu Isiraeli ndi Yuda yense mogwirizana ndi lamulo la mfumu, lakuti: “Inu ana a Isiraeli, bwererani+ kwa Yehova Mulungu+ wa Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli, kuti iye abwerere kwa anthu anu otsala+ amene anapulumuka m’manja mwa mafumu a Asuri.+
7 Musakhale ngati makolo anu+ ndi abale anu amene anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wa makolo awo, mwakuti anawachititsa kukhala chinthu chodabwitsa+ monga mmene mukuoneramu.
8 Tsopano musaumitse khosi lanu+ ngati mmene anachitira makolo anu. Gonjerani Yehova,+ pitani kunyumba yake yopatulika+ imene waiyeretsa+ mpaka kalekale. Tumikirani+ Yehova Mulungu wanu kuti mkwiyo wake umene wakuyakirani+ ukuchokereni.
9 Mukabwerera+ kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo+ ndi anthu amene anawagwira n’kupita nawo kudziko lina. Chotero iwo adzaloledwa kubwerera kudziko lino+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi wachisomo+ ndiponso wachifundo,+ ndipo sadzayang’ana kumbali mukabwerera kwa iye.”+
10 Asilikali othamangawo+ anapitiriza ulendo wawo ndipo anapita kumzinda ndi mzinda m’dziko lonse la Efuraimu+ ndi Manase mpaka ku Zebuloni. Koma anthuwo ankangokhalira kuwatonza ndi kuwaseka.+
11 Anthu+ ochokera ku Aseri, ku Manase, ndi ku Zebuloni okha ndi amene anadzichepetsa+ n’kubwera ku Yerusalemu.
12 Dzanja la Mulungu woona linakhalanso ndi anthu a ku Yuda, moti anawapatsa mtima umodzi+ kuti amvere lamulo+ la mfumu ndi la akalonga pa nkhani zokhudza kutumikira Yehova.+
13 Tsopano chikhamu cha anthu chinasonkhana ku Yerusalemu+ kuti achite chikondwerero+ cha mkate wopanda chofufumitsa m’mwezi wachiwiri,+ ndipo unali mpingo waukulu kwambiri.
14 Kenako iwo ananyamuka n’kuchotsa maguwa ansembe+ amene anali mu Yerusalemu. Anachotsanso maguwa ansembe onse ofukizirapo+ n’kukawataya kuchigwa cha Kidironi.+
15 Atatero anapha nyama ya pasika+ pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Ansembe ndi Alevi anali atachititsidwa manyazi moti anadziyeretsa+ n’kubweretsa nsembe zopsereza kunyumba ya Yehova.
16 Iwo anaimirira+ m’malo mwawo mogwirizana ndi zimene analamulidwa, malinga ndi lamulo la Mose munthu wa Mulungu woona. Ansembe+ anali kuwaza paguwa lansembe magazi amene anali kulandira kwa Alevi.
17 Koma panali anthu ambiri mumpingowo amene sanadziyeretse. Choncho Alevi+ ndi amene anali kugwira ntchito yophera nyama za pasika+ anthu onse amene sanali oyera, kuti awayeretse kwa Yehova.
18 Panali anthu ambiri ochokera ku Efuraimu,+ ku Manase,+ ku Isakara ndi ku Zebuloni+ amene sanadziyeretse+ ndipo anadya pasikayo mosatsatira zimene zinalembedwa.+ Koma Hezekiya anawapempherera+ kuti: “Yehova wabwino+ asakwiyire
19 aliyense amene wakonza mtima wake+ kuti afunefune Mulungu woona Yehova, Mulungu wa makolo ake, ngakhale kuti sanadziyeretse mogwirizana ndi zinthu zopatulika.”+
20 Choncho Yehova anamvera Hezekiya ndipo anakhululukira anthuwo.+
21 Chotero ana a Isiraeli amene anali ku Yerusalemu anachita chikondwerero+ cha mkate wopanda chofufumitsa masiku 7 mosangalala kwambiri.+ Alevi+ ndi ansembe+ anali kutamanda Yehova tsiku ndi tsiku ndi zipangizo zoimbira za mawu okwera zotamandira Yehova.+
22 Kuwonjezera apo, Hezekiya analankhula mokoma mtima+ kwa Alevi onse amene anali kutumikira Yehova mwanzeru.+ Anthuwo anachita phwando loikidwiratu kwa masiku 7.+ Anali kupereka nsembe zachiyanjano+ ndi kulapa+ kwa Yehova Mulungu wa makolo awo.
23 Ndiyeno mpingo wonsewo unagwirizana+ kuti uchitenso phwandolo masiku ena 7.+ Choncho analichitanso masiku 7 mosangalala.
24 Hezekiya mfumu ya Yuda anapereka+ ku mpingowo ng’ombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa 7,000. Akalonganso+ anapereka ku mpingowo ng’ombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa 10,000, ndipo ansembe+ ambiri anali kudziyeretsa.
25 Mpingo wonse wa Ayuda,+ ansembe, Alevi+ ndiponso mpingo wonse wa anthu amene anachokera ku Isiraeli,+ alendo+ amene anachokera m’dziko la Isiraeli+ ndi amene anali kukhala m’dziko la Yuda, anapitiriza kusangalala.+
26 Chotero munali chikondwerero chachikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambira m’masiku a Solomo+ mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli, kunali kusanachitike chikondwerero ngati chimenechi ku Yerusalemu.+
27 Pomalizira pake ansembe achilevi anaimirira n’kudalitsa+ anthuwo, ndipo mawu awo anamvedwa moti pemphero lawo linafika kumwamba, kumalo oyera okhala Mulungu.+