2 Mbiri 31:1-21
31 Atangomaliza kuchita zonsezi, Aisiraeli+ onse amene anali pamenepo anapita kumizinda ya Yuda+ n’kukaphwanya zipilala zopatulika,+ kukadula mizati yopatulika+ ndi kukagwetsa malo okwezeka+ ndi maguwa ansembe+ mu Yuda yense,+ mu Benjamini, mu Efuraimu+ ndi m’Manase+ mpaka kumaliza ntchitoyo. Atatero, ana onse a Isiraeli anabwerera kumizinda yawo, aliyense kumalo ake.
2 Kenako Hezekiya anaika magulu+ a ansembe ndi Alevi+ mogwirizana ndi magulu awo. Gulu lililonse analiika mogwirizana ndi utumiki wawo monga ansembe+ ndi Alevi+ ogwira ntchito yokhudza nsembe yopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano.+ Anawaika m’maguluwa kuti azitumikira,+ kuyamika+ ndi kutamanda+ Mulungu m’zipata za kachisi wa Yehova.
3 Kuchokera pa katundu wake,+ mfumuyo inapereka nsembe zopsereza za m’mawa+ ndi za madzulo, komanso nsembe zopsereza za masabata,+ za masiku okhala mwezi+ ndi za panyengo zochita chikondwerero,+ monga gawo limene inayenera kupereka la nsembe zopsereza,+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’chilamulo cha Yehova.+
4 Kuwonjezera pamenepo, Hezekiya anauza anthu okhala mu Yerusalemu kuti apereke gawo loyenera kupita kwa ansembe+ ndi Alevi,+ n’cholinga choti iwo azitsatira+ mosamala chilamulo cha Yehova.+
5 Ana a Isiraeli+ atangomva mawuwo, anawonjezera zipatso zoyambirira zimene ankapereka za mbewu,+ vinyo watsopano,+ mafuta,+ uchi,+ ndi zokolola zonse zakumunda+ ndipo anabweretsa chakhumi cha zonsezi chochuluka zedi.+
6 Ana a Isiraeli ndi Yuda amene anali kukhala m’mizinda ya Yuda+ anabweretsa chakhumi cha ng’ombe, nkhosa, ndi chakhumi cha zinthu zopatulika+ zimene anaziyeretsera Yehova Mulungu wawo. Anabweretsa zinthu zimenezi zambiri mpaka kukwana milumilu.
7 M’mwezi wachitatu+ anayamba kuunjika milu ya mphatsozo, ndipo m’mwezi wa 7+ anamaliza.
8 Hezekiya ndi akalonga+ atabwera n’kuona miluyo, anatamanda Yehova ndi kudalitsa+ anthu ake Aisiraeli.+
9 Patapita nthawi Hezekiya anafunsa ansembe ndi Alevi za miluyo.+
10 Ndiyeno Azariya,+ wansembe wamkulu wa nyumba ya Zadoki,+ anamuyankha kuti: “Kuyambira pamene anthu anayamba kubweretsa zopereka+ m’nyumba ya Yehova, pakhala kudya ndi kukhuta+ ndipo pali zotsala zambiri,+ chifukwa Yehova wadalitsa anthu ake+ ndipo zonse mukuzionazi n’zimene zatsala.”
11 Pamenepo Hezekiya anawauza kuti akonze zipinda zodyera+ m’nyumba ya Yehova, ndipo iwo anakonzadi.
12 Anthuwo anapitiriza kubweretsa zopereka,+ chakhumi,+ ndi zinthu zopatulika. Iwo ankabweretsa zimenezi mokhulupirika.+ Konaniya Mlevi ndiye anali kuyang’anira monga mtsogoleri, ndipo Simeyi m’bale wake anali wachiwiri wake.
13 Yehiela, Azaziya, Nahati, Asaheli, Yerimoti, Yozabadi, Elieli, Isimakiya, Mahati ndi Benaya anali atumiki othandiza Konaniya ndi Simeyi m’bale wake mwa lamulo la mfumu Hezekiya. Azariya+ ndiye anali mtsogoleri wa nyumba ya Mulungu woona.
14 Kore mwana wa Imuna Mlevi anali mlonda wa pachipata+ chakum’mawa+ amene anali kuyang’anira zopereka zaufulu+ zopita kwa Mulungu woona ndi kugawa zopereka za Yehova+ ndi zinthu zopatulika koposa.+
15 Iye anali kuyang’anira Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya ndi Sekaniya, m’mizinda ya ansembe+ amene anali pa maudindo awo chifukwa cha kukhulupirika kwawo.+ Amenewa ankagwira ntchito yogawa zinthu kwa abale awo amene anali m’magulu.+ Ankawagawira zinthuzo mofanana, kaya akhale wamkulu kapena wamng’ono.+
16 Ankagawira anthu amenewa kuwonjezera pa amene anali pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo,+ komanso amuna oyambira zaka zitatu kupita m’tsogolo.+ Onsewa ankabwera kunyumba ya Yehova tsiku ndi tsiku kudzachita utumiki wawo, umene anayenera kuchita mogwirizana ndi magulu awo.
17 Panali mndandanda wa mayina a ansembe wotsatira makolo awo+ ndi mndandanda wa mayina a Alevi+ kuyambira azaka 20+ kupita m’tsogolo, malinga ndi ntchito zawo m’magulu awo.+
18 Mndandandawo unali wa ana awo onse, akazi awo, ndiponso ana awo aamuna ndi aakazi mumpingo wonsewo, pakuti pa ntchito yawo imene ankagwira chifukwa cha kukhulupirika kwawo,+ anadziyeretsa+ kuti achite utumiki wawo wa zinthu zopatulika.
19 Panalinso mndandanda wa mayina a ana a Aroni,+ ansembe, amene anali kukhala m’malo+ odyetserako ziweto kunja kwa mizinda yawo. M’mizinda yonseyo munali amuna amene anasankhidwa pochita kuwatchula mayina, kuti azipereka magawo a chakudya kwa mwamuna aliyense pakati pa ansembe ndiponso kwa Alevi onse amene anali pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo.
20 Hezekiya anachita zimenezi mu Yuda yense, ndipo anapitiriza kuchita zabwino,+ zoyenera+ ndi zokhulupirika+ pamaso pa Yehova Mulungu wake.
21 Anagwira ndi mtima wake wonse+ ntchito iliyonse imene anaiyamba mu utumiki+ wa panyumba ya Mulungu woona ndi m’chilamulo,+ pofunafuna+ Mulungu wake, ndipo zinthu zinamuyendera bwino.+