2 Mbiri 35:1-27

35  Kenako Yosiya+ anachita pasika+ wa Yehova ku Yerusalemu, ndipo iwo anapha nyama ya pasika+ pa tsiku la 14+ la mwezi woyamba.+  Choncho iye anaika ansembe pa ntchito zawo+ ndipo anawalimbikitsa+ pa utumiki wawo wa panyumba ya Yehova.+  Ndiyeno anauza Alevi, alangizi+ a Isiraeli yense, omwe anali oyera kwa Yehova, kuti: “Ikani Likasa lopatulika+ m’nyumba+ imene Solomo mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli anamanga. Lisakhalenso katundu wolemera pamapewa anu.+ Tsopano tumikirani+ Yehova Mulungu wanu ndi anthu ake Aisiraeli.  Konzekerani potsatira nyumba ya makolo anu+ mogwirizana ndi magulu anu,+ malinga ndi zimene analemba+ Davide mfumu ya Isiraeli ndiponso zimene analemba+ Solomo mwana wake.  Muime+ m’malo oyera potsatira magulu a nyumba ya makolo anu kuti mutumikire abale anu, ana a anthuwa, ndipo gulu lililonse la anthu likhale ndi gulu lake la Alevi+ loti liziwatumikira, losankhidwa potsatira makolo awo.+  Muphe nyama ya pasika+ n’kudziyeretsa+ ndipo muikonzere abale anu kuti muchite mogwirizana ndi mawu a Yehova kudzera mwa Mose.”+  Tsopano Yosiya anapereka kwa ana a anthuwo ziweto zokwana 30,000, zomwe zinali ana a nkhosa amphongo ndi ana a mbuzi amphongo. Anapereka zonsezo kuti zikhale nyama zophera pasika za onse amene analipo, ndiponso ng’ombe 3,000.+ Zonsezi zinachokera pa katundu wa mfumu.+  Akalonga ake+ anapereka nsembe yaufulu kwa anthuwo,+ kwa ansembe ndi kwa Alevi. Hilikiya,+ Zekariya ndi Yehiela monga atsogoleri a nyumba ya Mulungu woona, anapereka kwa ansembe nkhosa ndi mbuzi zokwana 2,600 ndiponso ng’ombe 300 kuti zikhale nyama zophera pasika.  Konaniya limodzi ndi Semaya ndi Netaneli abale ake komanso Hasabiya, Yeyeli ndi Yozabadi, amene anali akulu a Alevi, anapereka kwa Alevi nkhosa ndi mbuzi 5,000 ndiponso ng’ombe 500 kuti zikhale nyama zophera pasika. 10  Iwo anamaliza kukonzekera+ ndipo ansembe anaimirirabe+ m’malo awo,+ komanso Alevi anali m’magulu awo+ mogwirizana ndi lamulo la mfumu.+ 11  Atatero anapha nyama ya pasika+ ndipo ansembe+ anawaza+ paguwa lansembe magazi amene anali kupatsidwa, pamene Alevi anali kusenda nyamazo.+ 12  Kuwonjezera apo, anakonza nsembe zopsereza kuti azipereke kwa ana a anthuwo potsatira magulu+ a nyumba ya makolo awo,+ kuti ziperekedwe+ kwa Yehova mogwirizana ndi zimene zinalembedwa m’buku la Mose.+ Anachitanso chimodzimodzi ndi ng’ombe. 13  Kenako anaphika+ nsembe ya pasika+ pamoto malinga ndi mwambo wawo ndipo zinthu zopatulika anaziphika+ m’miphika, m’miphika ya pansi pozungulira ndi m’miphika yosalowa kwambiri. Atatero anapititsa nyamayo msangamsanga kwa ana onse a anthuwo.+ 14  Pambuyo pake anakonza nyama yawo ndi ya ansembe+ chifukwa ansembe, ana a Aroni, anali otanganidwa ndi kupereka nsembe zopsereza+ ndiponso mafuta+ mpaka usiku. Choncho Alevi anakonza+ nyama yawo ndi ya ansembe, ana a Aroni. 15  Oimba,+ ana a Asafu,+ anali pa ntchito yawo mogwirizana ndi lamulo la Davide,+ la Asafu,+ la Hemani+ ndi la Yedutuni+ wamasomphenya+ wa mfumu. Alonda a pazipata+ anali pazipata zosiyanasiyana.+ Panalibe chifukwa choti asiyire ntchito yawo chifukwa abale awo Alevi anawakonzera+ nyama yawo. 16  Iwo anamaliza kukonza zonse zofunikira pochita pasika+ wa Yehova tsiku limenelo, ndi popereka nsembe zopsereza paguwa lansembe la Yehova, mogwirizana ndi lamulo la Mfumu Yosiya.+ 17  Ana a Isiraeli amene analipo anachita pasika+ pa nthawi imeneyo. Anachitanso chikondwerero cha mkate wopanda chofufumitsa kwa masiku 7.+ 18  Panali pasanachitikepo pasika ngati ameneyu mu Isiraeli kuyambira m’masiku a mneneri Samueli.+ Mafumu ena onse+ a Isiraeli anali asanachitepo pasika ngati amene anachita Yosiya, ansembe, Alevi, Ayuda ndi Aisiraeli onse amene analipo, ndiponso anthu okhala mu Yerusalemu. 19  Pasika ameneyu anachitika m’chaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya.+ 20  Pambuyo pa zonsezi, Yosiya atakonza nyumba ya Mulungu, Neko+ mfumu ya Iguputo+ anabwera kudzachita nkhondo ku Karikemisi+ pafupi ndi mtsinje wa Firate, ndipo Yosiya+ anapita kukakumana naye.+ 21  Pamenepo Neko anatumiza anthu kwa iye kukamuuza kuti: “Kodi ndili nawe chiyani iwe mfumu ya Yuda? Lero sindinabwere kudzamenyana ndi iweyo. Ndabwera kudzamenyana ndi mtundu wina umene Mulungu wanena kuti ndikauwopseze. Ngati ukufuna kuti zinthu zikuyendere bwino, usachite zimenezi. Uope Mulungu amene ali nane ndipo usalole kuti iye akuwononge.”+ 22  Koma Yosiya anapitabe kukakumana naye+ ndipo anadzisintha+ kuti amenyane naye. Iye sanamvere mawu a Neko+ ochokera pakamwa pa Mulungu. Choncho anapita kukamenyana naye m’chigwa cha Megido.+ 23  Kenako asilikali oponya mivi+ analasa Mfumu Yosiya. Choncho mfumuyo inauza atumiki ake kuti: “Nditsitseni pakuti ndavulala kwambiri.”+ 24  Atumiki akewo anamutsitsa m’galetalo n’kumukweza m’galeta lake lachiwiri lankhondo, n’kupita naye ku Yerusalemu.+ Choncho iye anafa+ ndipo anamuika m’manda a makolo ake.+ Ayuda onse ndi anthu onse okhala ku Yerusalemu anamulira+ Yosiya. 25  Yeremiya+ anayamba kuimbira Yosiya nyimbo ya maliro.+ Oimba onse aamuna ndi aakazi+ amanenabe za Yosiya m’nyimbo zawo zoimba polira mpaka lero. Nyimbo zimenezi zinakhazikitsidwa ngati lamulo mu Isiraeli, ndipo zinalembedwa m’nyimbo zoimba polira.+ 26  Nkhani zina+ zokhudza Yosiya ndi zochita zake zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha,+ zimene anachita potsatira zomwe zinalembedwa m’chilamulo+ cha Yehova, 27  ndiponso zochita zake, zoyambirira ndi zomalizira,+ zinalembedwa m’Buku+ la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda.

Mawu a M'munsi