2 Mbiri 4:1-22

4  Ndiyeno anapanga guwa lansembe lamkuwa.+ Guwalo linali lalikulu mikono 20 m’litali, mikono 20 m’lifupi ndipo kuchokera pansi kufika pamwamba linali lalitali mikono 10.+  Kenako iye anapanga thanki yamkuwa.*+ Pakamwa pa thankiyo panali papakulu mikono 10 kuyeza modutsa pakati pake, ndipo panali pozungulira. Thankiyo inali yaitali mikono isanu kuchokera pansi kufika pamwamba. Pankafunika chingwe chotalika mikono 30 kuti ayeze kuzungulira thankiyo.+  M’munsi mwa thankiyo munali zokongoletsa zofanana ndi zipanda kuzungulira+ thankiyo, ndipo zinalipo 10 pamkono uliwonse kuzungulira thanki yonseyo.+ Zokongoletsa zooneka ngati zipandazo zinalipo mizere iwiri, ndipo anaziumbira kumodzi ndi thankiyo.  Thankiyo anaikhazika pang’ombe zamphongo 12.+ Ng’ombe zitatu zinayang’ana kumpoto, zitatu zinayang’ana kumadzulo, zitatu zinayang’ana kum’mwera, ndipo zitatu zinayang’ana kum’mawa. Thankiyo inali pamwamba pa ng’ombezo ndipo mbuyo zonse za ng’ombezo zinaloza mkati.+  Kuchindikala kwa thankiyo kunali chikhatho* chimodzi. Mlomo wake unali ngati wa mphika wakukamwa ngati duwa.+ Thankiyo inali yotha kulowa+ madzi okwana mitsuko* 3,000.+  Iye anapanganso mabeseni 10. Anaika mabeseni asanu mbali ya kudzanja lamanja, mabeseni asanu mbali ya kumanzere.+ M’mabeseniwo anali kutsukiramo ndi kutsukuluziramo+ zinthu zokhudzana ndi nsembe yopsereza.+ Ansembe anali kusamba madzi ochokera m’thanki ija.+  Kenako anapanga zoikapo nyale+ 10 zagolide zofanana,+ n’kuziika m’kachisi. Anaika zisanu mbali ya kudzanja lamanja, zisanu mbali ya kumanzere.+  Anapanganso matebulo 10 n’kuwaika m’kachisi. Anaika asanu mbali ya kudzanja lamanja, asanu mbali ya kumanzere,+ ndipo anapanganso mbale zolowa 100 zagolide.  Ndiyeno anapanga bwalo+ la ansembe+ ndi bwalo lalikulu lamkati+ ndi zitseko za bwalo lalikululo. Zitsekozo anazikuta ndi mkuwa. 10  Thanki ija anaiika mbali ya kudzanja lamanja, kum’mawa chakum’mwera.+ 11  Pomalizira pake Hiramu anapanga ndowa,+ mafosholo+ ndi mbale zolowa.+ Chotero iye anamaliza ntchito imene anali kugwirira Mfumu Solomo pa nyumba ya Mulungu woona. 12  Anapanga zipilala ziwiri,+ mitu ya zipilala yozungulira+ imene anaiika pamwamba pa zipilala ziwirizo, ndiponso maukonde awiri+ okutira mitu iwiri yozungulira imene inali pamwamba pa zipilalazo. 13  Anapanganso makangaza 400+ oika pamaukonde awiri aja, mizere iwiri ya makangaza pa ukonde uliwonse. Makangazawo anali okutira mitu iwiri yozungulira imene inali pazipilala ziwiri zija.+ 14  Anapanganso zotengera 10,+ mabeseni 10+ oika pa zotengera, 15  thanki imodzi,+ ng’ombe zamphongo 12 zokhala pansi pa thankiyo,+ 16  ndowa, mafosholo,+ mafoloko,+ ndi ziwiya zina zonse.+ Hiramu-abivu+ anapanga zinthu zimenezi ndi mkuwa wonyezimira. Anapangira Mfumu Solomo kuti aziike m’nyumba ya Yehova. 17  Mfumuyo inaumbira zinthu zimenezi m’chikombole chochindikala chadongo, m’Chigawo* cha Yorodano, pakati pa Sukoti+ ndi Zereda.+ 18  Chotero Solomo anapanga ziwiya zimenezi zambirimbiri, moti mkuwawo sunadziwike kulemera kwake.+ 19  Solomo anapanga ziwiya zonse+ zimene zinali panyumba ya Mulungu woona, guwa lansembe lagolide,+ matebulo+ oikapo mkate wachionetsero, 20  ndi zoikapo nyale+ ndi nyale zake+ zagolide woyenga bwino, zoti aziziyatsa m’chipinda chamkati+ mogwirizana ndi lamulo. 21  Anapanganso maluwa agolide, nyale zagolide, zopanira+ zagolide zozimitsira nyale, (golide wake anali woyengedwa bwino kwambiri,) 22  zozimitsira nyale, mbale zolowa, makapu, ndi zopalira moto. Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino.+ Anapanganso khomo lolowera m’nyumbayo,+ zitseko zamkati za Chipinda Choyera Koposa, ndi zitseko+ za nyumbayo. Zonsezi zinali zagolide.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “nyanja yosungunula.”
Onani Zakumapeto 12.
Onani Zakumapeto 12.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 13:10.