2 Mbiri 8:1-18

8  Kumapeto kwa zaka 20+ zimene Solomo anamanga nyumba ya Yehova+ ndi nyumba yake,+  iye anamanganso mizinda imene Hiramu+ anam’patsa n’kuipereka kwa Aisiraeli kuti azikhalamo.  Kuwonjezera pamenepo, Solomo anapita ku Hamati-zoba n’kugonjetsa mzindawo.  Kenako anamanganso mzinda wa Tadimori m’chipululu ndi mizinda yonse yosungiramo zinthu+ imene anamanga ku Hamati.+  Ndiyeno anamanga mzinda wa Beti-horoni Wakumtunda+ ndi Beti-horoni Wakumunsi.+ Imeneyi inali mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri,+ zitseko ndi mipiringidzo.+  Anamanganso Baalati+ ndi mizinda yonse yosungirako zinthu imene inakhala ya Solomo, mizinda yonse yosungirako magaleta,+ mizinda yonse ya amuna okwera pamahatchi,+ ndi chilichonse chimene iye anakonda+ kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni,+ ndi m’dziko lonse limene ankalamulira.  Anthu onse otsala a Ahiti,+ Aamori,+ Aperezi,+ Ahivi,+ ndi Ayebusi,+ amene sanali Aisiraeli,+  ana onse ochokera kwa iwowa amene anatsala m’dzikomo, amene ana a Isiraeli sanawawononge,+ Solomo anali kuwagwiritsa+ ntchito yaukapolo, kufikira lero.+  Koma panalibe ana a Isiraeli amene Solomo anawasandutsa akapolo ogwira ntchito yake,+ chifukwa iwo anali ankhondo ake,+ atsogoleri a asilikali ake othandiza pamagaleta, atsogoleri a asilikali ake oyendetsa magaleta+ ndiponso a amuna ake okwera pamahatchi.+ 10  Panali akuluakulu oyang’anira nduna+ okwana 250 a Mfumu Solomo. Iwowa anali akapitawo oyang’anira anthu ogwira ntchito.+ 11  Solomo anatulutsa mwana wamkazi wa Farao+ mu Mzinda wa Davide+ n’kukamuika m’nyumba imene anam’mangira,+ pakuti iye anati: “Ngakhale ali mkazi wanga, asamakhale m’nyumba ya Davide mfumu ya Isiraeli, chifukwa malo alionse amene likasa la Yehova likukhala ndi oyera.”+ 12  Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anapereka nsembe yopsereza+ kwa Yehova paguwa lansembe+ la Yehova limene iye anamanga patsogolo pa khonde.+ 13  Anapereka nsembezo mogwirizana ndi dongosolo la tsiku ndi tsiku+ loperekera nsembe, malinga ndi chilamulo cha Mose. Nsembezo zinali za pa masabata,+ za pa masiku okhala mwezi,+ ndi za pa zikondwerero zoikidwiratu+ zochitika katatu pa chaka.+ Zikondwererozo zinali chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ chikondwerero cha masabata,+ ndi chikondwerero cha misasa.+ 14  Kuwonjezera pamenepo, Solomo anaika magulu+ a ansembe pa utumiki wawo mogwirizana ndi lamulo la Davide bambo ake.+ Anaikanso Alevi+ pamalo awo a ntchito kuti azitamanda+ ndi kutumikira+ pamaso pa ansembe mogwirizana ndi dongosolo la tsiku ndi tsiku.+ Komanso anaika alonda a pazipata m’magulu awo kuti akhale m’zipata zosiyanasiyana+ chifukwa ndilo linali lamulo la Davide munthu wa Mulungu woona. 15  Iwo sanapatuke pa lamulo limene mfumu inapereka kwa ansembe ndi kwa Alevi lokhudza nkhani ina iliyonse ndi zinthu zina zofunikira.+ 16  Choncho ntchito yonse ya Solomo, kuyambira pa tsiku limene anayala+ maziko a nyumba ya Yehova kufikira pamene inatha,+ inayenda bwino. Motero nyumba ya Yehova inatha kumangidwa.+ 17  Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anapita ku Ezioni-geberi+ ndi ku Eloti,+ kugombe la nyanja m’dziko la Edomu.+ 18  Hiramu,+ kudzera mwa antchito ake, ankatumizira Solomo zombo ndi antchito odziwa za panyanja.+ Iwo ankapita ku Ofiri+ pamodzi ndi antchito a Solomo kukatenga golide+ wokwana matalente* 450,+ ndipo anali kubwera naye kwa Mfumu Solomo.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 12.