2 Petulo 1:1-21
1 Ine Simoni Petulo, kapolo+ ndi mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndikulembera anthu amene apeza chikhulupiriro chofanana ndi chathu,+ mwa chilungamo+ cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.+
2 Ndikufuna kuti mulandire kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere wowonjezereka.+ Kuti muchite zimenezi, mumudziwe molondola+ Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.
3 Pakuti Mulungu, mwa mphamvu yake, watipatsa kwaulere zinthu zonse zofunika kuti munthu akhale moyo+ wodzipereka kwa Mulungu.+ Talandira zinthu zimenezi kudzera mwa kudziwa molondola za iye amene anatiitana,+ kudzera mu ulemerero+ ndi ubwino wake.
4 Kudzera mwa zimenezi, iye watilonjeza zinthu zamtengo wapatali ndi zazikulu kwambiri,+ kuti mwa malonjezo amenewa mukhale ndi makhalidwe+ a Mulungu.+ Iye watipatsa kwaulere malonjezo amenewa chifukwa tapulumuka ku khalidwe loipa limene lili m’dzikoli,+ limene limayamba chifukwa cha chilakolako choipa.
5 Pa chifukwa chimenechi, inunso yesetsani mwakhama+ kuwonjezera pa chikhulupiriro chanu makhalidwe abwino,+ pa makhalidwe anu abwino muwonjezerepo kudziwa zinthu,+
6 pa kudziwa zinthu kudziletsa, pa kudziletsa+ kupirira, pa kupirira kudzipereka kwa Mulungu,+
7 pa kudzipereka kwa Mulungu kukonda abale, pa kukonda abale, chikondi.+
8 Ngati zinthu zimenezi zili mwa inu ndipo zikusefukira, zidzakutetezani kuti musakhale ozilala kapena osabala zipatso+ pa zimene mukuchita mogwirizana ndi kumudziwa molondola Ambuye wathu Yesu Khristu.
9 Munthu amene alibe zinthu zimenezi ndi wakhungu, wotseka maso ake kuti asaone kuwala,+ ndipo waiwala+ kuti anayeretsedwa+ ku machimo ake akale.
10 Pa chifukwa chimenechi abale, chitani chilichonse chotheka kuti mukhalebe okhulupirika, n’cholinga choti mupitirizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana+ ndi kuwasankha,+ pakuti mukapitiriza kuchita zinthu zimenezi simudzalephera ngakhale pang’ono.+
11 Ndipo mukatero, adzakutsegulirani khomo kuti mulowe+ mwaulemerero mu ufumu wosatha+ wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.+
12 Pa chifukwa chimenechi, nthawi zonse ndizikukumbutsani+ zinthu zimenezi, ngakhale kuti mukuzidziwa kale ndipo ndinu olimba m’choonadi+ chimene munachilandira.+
13 Chotero ndikuona kuti n’koyenera kumakugwedezani mwa kukukumbutsani+ pamene ndidakali mumsasa uno,+
14 popeza ndikudziwa kuti ndatsala pang’ono kutuluka mumsasa wangawu,+ monga momwe Ambuye wathu Yesu Khristu anandisonyezera.+
15 Choncho nthawi zonse ndizichita chilichonse chotheka, kuti ndikadzachoka+ mudzathe kukumbukira zinthu zimenezi.
16 Ndithudi, pamene ifeyo tinakudziwitsani za mphamvu ya Ambuye wathu Yesu Khristu ndi za kukhalapo* kwake,+ sitinatengere nkhani zabodza zopekedwa mochenjera ndi anthu,+ koma tinachita zimenezo chifukwa tinachita kuona ndi maso athu ulemerero wake.+
17 Pakuti iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate,+ pamene mawu anamveka kwa iye kuchokera mu ulemerero waukulu, kuti: “Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye.”+
18 Zoonadi, mawu amenewa tinawamva+ kuchokera kumwamba tili naye limodzi m’phiri loyera.+
19 Choncho mawu aulosiwa+ ndi odalirika kwambiri,+ ndipo mukuchita bwino kuwaganizira mozama. Mawu amenewo ali ngati nyale+ imene ikuwala mu mdima, m’mitima yanu, mpaka m’bandakucha, nthanda*+ ikadzatuluka.
20 Choyamba, mukudziwa kuti ulosi wa m’Malemba suchokera m’maganizo a munthu.+
21 Chifukwa ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu,+ koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu+ motsogoleredwa ndi mzimu woyera.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 8.
^ “Nthanda” ndi nyenyezi yomalizira kutuluka imene imaonekera dzuwa likangotsala pang’ono kutuluka.