2 Petulo 3:1-18
3 Okondedwa, iyi tsopano ndi kalata yachiwiri imene ndikukulemberani, ndipo monga yoyamba ija,+ ndikulimbikitsa mphamvu zanu zotha kuganiza bwino mwa kukukumbutsani,+
2 kuti mukumbukire mawu amene aneneri oyera ananena kale,+ ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi wathu kudzera mwa atumwi anu.+
3 Choyamba, inu mukudziwa kuti m’masiku otsiriza+ kudzakhala onyodola+ amene azidzatsatira zilakolako zawo,+
4 amene azidzati:+ “Kukhalapo* kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti?+ Taonani, kuchokera tsiku limene makolo athu anamwalira, zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi ngati mmene zakhalira kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe.”+
5 Anthu amenewa, mwa kufuna kwawo amalephera kuzindikira mfundo iyi yakuti, panali kumwamba+ kuchokera kalekale, ndipo mwa mawu a Mulungu, dziko lapansi linali loumbika motsendereka pamwamba pa madzi+ ndi pakati pa madzi,+
6 ndipo mwa zimenezi, dziko la pa nthawiyo linawonongedwa pamene linamizidwa ndi madzi.+
7 Ndipo mwa mawu amodzimodziwo, kumwamba+ kumene kulipo panopa limodzi ndi dziko lapansi,+ azisungira moto+ m’tsiku lachiweruzo+ ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.+
8 Komabe okondedwa, musalephere kuzindikira mfundo imodzi iyi yakuti, tsiku limodzi kwa Yehova* lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi.+
9 Yehova sakuchedwa kukwaniritsa lonjezo lake,+ ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa, koma akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.+
10 Komabe, tsiku la Yehova+ lidzafika ngati mbala,+ pamene kumwamba kudzachoka+ ndi mkokomo waukulu,+ koma zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri n’kusungunuka,+ ndipo dziko lapansi+ ndi ntchito zake zidzaonekera poyera.+
11 Choncho popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka, ganizirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu.
12 Muzichita zimenezi poyembekezera+ ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova,+ pamene kumwamba kudzapsa ndi moto n’kusungunuka,+ ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri n’kusungunuka.
13 Koma pali kumwamba kwatsopano+ ndi dziko lapansi latsopano+ zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.+
14 Chotero okondedwa, pakuti mukuyembekezera zinthu zimenezi, chitani chilichonse chotheka kuti iye adzakupezeni opanda banga,+ opanda chilema ndiponso muli mu mtendere.+
15 Kuwonjezera apo, muone kuleza mtima kwa Ambuye wathu kukhala chipulumutso, monganso mmene m’bale wathu wokondedwa Paulo anakulemberani mogwirizana ndi nzeru+ zimene anapatsidwa.+
16 Iye anafotokoza zimenezi ngati mmene anachitiranso m’makalata ake onse. Komabe m’makalata akewo muli zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osaphunzitsidwa ndi amaganizo osakhazikika akuzipotoza, ngati mmene amachitiranso ndi Malemba ena onse,+ n’kumadziitanira okha chiwonongeko.
17 Choncho inu okondedwa, popeza mukudziwiratu zimenezi,+ chenjerani kuti musasochere pokopeka ndi zolakwa za anthu ophwanya malamulowo, kuopera kuti mungalephere kukhala olimba ndipo mungagwe.+
18 Ndithu musatero ayi, koma pitirizani kulandira kukoma mtima kwakukulu ndi kumudziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.+ Kwa iye kukhale ulemerero, kuyambira panopa mpaka muyaya.+