2 Samueli 16:1-23

16  Davide atapitirira pang’ono pamwamba pa phiri paja,+ anaona Ziba+ mtumiki wa Mefiboseti+ akubwera kudzakumana naye. Iye anali ndi abulu awiri+ okhala ndi zishalo ndipo abuluwa anali atanyamula mitanda 200 ya mkate,+ mphesa zouma zoumba pamodzi 100,+ zipatso za m’chilimwe* 100+ zouma zoumba pamodzi ndiponso mtsuko waukulu wa vinyo.+  Ndiyeno mfumu inafunsa Ziba kuti: “Kodi zinthu zimene watengazi n’zachiyani?”+ Poyankha Ziba anati: “Abuluwa ndatengera anthu a m’nyumba ya mfumu kuti azikwerapo, mkate ndi makeke a zipatso za m’chilimwe ndatengera anyamata+ kuti adye, ndipo vinyo ndatengera munthu wotopa+ m’chipululu+ kuti amwe.”  Tsopano mfumu inafunsa kuti: “Kodi mwana wa mbuye wako ali kuti?”+ Pamenepo Ziba anauza mfumu kuti: “Watsalira ku Yerusalemu, pakuti wanena kuti, ‘Lero nyumba ya Isiraeli indibwezera ufumu wa bambo anga.’”+  Kenako mfumu inauza Ziba kuti: “Taona, zonse zimene zinali za Mefiboseti+ ndi zako.” Pamenepo Ziba anati: “Ndikuwerama+ pamaso panu. Pitirizani kundikomera mtima mbuyanga mfumu.”  Ndiyeno Mfumu Davide inafika ku Bahurimu.+ Kumeneko inaona mwamuna wina wa m’banja la Sauli, dzina lake Simeyi,+ mwana wa Gera akutuluka ndipo anali kulankhula mawu onyoza.+  Iye anayamba kuponya miyala Davide ndi atumiki onse a Mfumu Davide. Anthu onse ndi amuna onse amphamvu anali kudzanja lamanja ndi lamanzere la mfumu.  Ponyoza, Simeyi anali kunena kuti: “Choka, choka, munthu wa mlandu wamagazi+ ndi wopanda pake iwe!+  Yehova wakubwezera mlandu wonse wa magazi a nyumba ya Sauli amene iwe unamulowa m’malo monga mfumu. Yehova wapereka ufumu m’manja mwa Abisalomu mwana wako. Ndipo tsopano tsoka lakugwera chifukwa uli ndi mlandu wamagazi!”+  Pamapeto pake Abisai mwana wa Zeruya+ anauza mfumu kuti: “N’chifukwa chiyani galu wakufa uyu+ akukunyozani mbuyanga mfumu?+ Ndiloleni ndipite chonde ndikam’dule mutu.”+ 10  Koma mfumu inati: “Ndili nanu chiyani+ inu ana a Zeruya?+ Musiyeni anyoze+ chifukwa Yehova wamuuza kuti,+ ‘Munyoze Davide!’ Choncho ndani angamufunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani iwe wachita zimenezi?’”+ 11  Ndiyeno Davide anapitiriza kuuza Abisai ndi atumiki ake onse kuti: “Ngati mwana wanga weniweni, wotuluka m’chiuno mwanga akufunafuna moyo wanga,+ kuli bwanji M’benjamini uyu!+ Musiyeni anyoze, pakuti Yehova wamuuza kuti atero! 12  Mwina Yehova aona+ ndi diso lake, ndipo lero Yehova abwezeretsa kwa ine zinthu zabwino m’malo mwa temberero la Simeyi.”+ 13  Pamenepo Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye anapitiriza kuyenda mumsewu. Simeyi anali kuyenda m’mbali mwa phiri pafupi ndi Davide ndipo anali kuyenda akulankhula mawu onyoza.+ Iye analinso kuponya miyala akuyenda m’mbali mwa phirimo pafupi ndi Davide ndiponso anali kuwaza fumbi lambiri.+ 14  Patapita nthawi, mfumu ndi anthu onse amene anali naye anafika kumene anali kupita ali otopa. Choncho iwo anaima kuti apume.+ 15  Koma Abisalomu ndi anthu onse, amuna a Isiraeli, analowa mu Yerusalemu+ ndipo Ahitofeli+ anali naye limodzi. 16  Ndiyeno Husai+ Mwareki,+ mnzake wa Davide,+ atangofika kwa Abisalomu anauza Abisalomu kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!+ Mfumu ikhale ndi moyo wautali!” 17  Pamenepo Abisalomu anauza Husai kuti: “Kodi kumeneku ndiko umati kusonyeza mnzako kukoma mtima kosatha? N’chifukwa chiyani sunapite ndi mnzako?”+ 18  Poyankha Husai anauza Abisalomu kuti: “Iyayi, amene Yehova wamusankha komanso amene anthu awa ndi anthu onse a mu Isiraeli amusankha, ine ndidzakhala wake ndipo ndidzakhala ndi iye. 19  Ndibwereze kunena kuti, Ine ndingatumikire ndani? Kodi sindiyenera kutumikira mwana wake? Monga mmene ndinatumikira bambo anu, ndichitanso chimodzimodzi kwa inu.”+ 20  Kenako Abisalomu anafunsa Ahitofeli kuti: “Amuna inu, nenani maganizo anu.+ Tichite chiyani?” 21  Pamenepo Ahitofeli anauza Abisalomu kuti: “Ugone ndi adzakazi a bambo ako+ amene wawasiya kuti azisamalira nyumba.+ Ukatero Aisiraeli onse adzamva kuti wadzinunkhitsa+ pamaso pa bambo ako,+ ndipo manja+ a anthu onse amene ali ndi iwe adzalimba ndithu.” 22  Choncho anamangira Abisalomu hema padenga,+ ndipo Abisalomu anayamba kugona ndi adzakazi a bambo ake,+ Aisiraeli onse akuona.+ 23  Ndiyeno masiku amenewo munthu akalandira malangizo kwa Ahitofeli, zinali ngati kuti munthu wafunsira malangizo kwa Mulungu woona. Umu ndi mmene malangizo+ onse a Ahitofeli+ analili, kwa Davide ndi Abisalomu yemwe.

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “zipatso za m’chilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.