2 Samueli 2:1-32

2  Ndiyeno pambuyo pake, Davide anayamba kufunsira kwa Yehova,+ kuti: “Kodi ndipite ku umodzi mwa mizinda ya Yuda?” Pamenepo Yehova anamuuza kuti: “Pita.” Davide anafunsanso kuti: “Ndipite kuti?” Iye anamuyankha kuti: “Ku Heburoni.”+  Chotero Davide anapita kumeneko pamodzi ndi akazi ake awiri, Ahinowamu+ wa ku Yezereeli ndi Abigayeli+ wa ku Karimeli, amene anali mkazi wa Nabala.  Davide anapitanso ndi amuna+ amene anali kuyenda naye, aliyense ndi banja lake. Iwo anakakhala m’mizinda ya m’dera la Heburoni.  Kenako amuna a ku Yuda+ anabwera ndi kudzoza+ Davide kumeneko kukhala mfumu ya nyumba ya Yuda.+ Ndiyeno anthu anauza Davide kuti: “Anthu a ku Yabesi-giliyadi ndi amene anaika Sauli m’manda.”  Choncho Davide anatumiza mithenga kwa amuna a ku Yabesi-giliyadi+ kuti akawauze kuti: “Yehova akudalitseni,+ chifukwa munasonyeza kukoma mtima kosatha+ kwa mbuye wanu Sauli mwa kumuika m’manda.+  Chotero Yehova akusonyezeni kukoma mtima kosatha+ ndipo muone kukhulupirika kwake. Inenso ndikusonyezani ubwino umenewu chifukwa mwachita zimenezi.+  Tsopano manja anu alimbe ndipo mukhale amuna olimba mtima,+ chifukwa mbuye wanu Sauli wamwalira ndipo anthu a nyumba ya Yuda adzoza ine kukhala mfumu+ yawo.”  Ndiyeno Abineri+ mwana wa Nera, amene anali mtsogoleri wa asilikali a Sauli, anatenga Isi-boseti+ mwana wa Sauli ndi kuwolokera naye ku Mahanaimu.+  Kumeneko anamulonga ufumu kuti azilamulira Giliyadi,+ Aasere, Yezereeli,+ Efuraimu+ ndi Benjamini,+ Isiraeli yense. 10  Isi-boseti mwana wa Sauli anali ndi zaka 40 pamene anakhala mfumu ya Isiraeli, ndipo analamulira zaka ziwiri. Anthu a nyumba ya Yuda+ okha ndi amene anali kutsatira Davide. 11  Nthawi yonse imene Davide anakhala mfumu ku Heburoni, kulamulira nyumba ya Yuda, inali zaka 7 ndi miyezi 6.+ 12  Patapita nthawi, Abineri mwana wa Nera ndi atumiki a Isi-boseti mwana wa Sauli, anachoka ku Mahanaimu+ n’kupita ku Gibeoni.+ 13  Nayenso Yowabu+ mwana wa Zeruya+ ndi atumiki a Davide, anapita kudziwe la Gibeoni ndipo magulu awiriwo anakumana kumeneko. Gulu la Yowabu linangokhala pansi kumbali ina ya dziwe ndipo gulu linalo linakhalanso kumbali inayo. 14  Pamapeto pake Abineri anauza Yowabu kuti: “Bwanji anyamata athu anyamuke ndipo amenyane tione.” Poyankha, Yowabu anati: “Chabwino, zitero.” 15  Chotero iwo ananyamuka. Kumbali ya Benjamini ndi Isi-boseti,+ mwana wa Sauli, anasankha anyamata 12, ndipo kwa atumiki a Davide anasankhanso anyamata 12. 16  Aliyense wa anyamatawo anagwira mnzake kumutu ndipo onse anabayana ndi lupanga m’mimba, moti onsewo anagwa pansi ndi kufa. Malo amenewo anatchedwa dzina lakuti Helikati-hazurimu,* ndipo ali ku Gibeoni.+ 17  Pa tsiku limenelo, kumenyana kunakula ndipo kunali koopsa kwambiri. Pamapeto pake, Abineri+ ndi amuna a Isiraeli anagonjetsedwa ndi atumiki a Davide. 18  Ndiyeno ana atatu aamuna a Zeruya,+ amene ndi Yowabu,+ Abisai,+ ndi Asaheli+ anali pamenepo. Asaheli anali waliwiro kwambiri ngati mbawala+ yothamanga m’thengo. 19  Asaheliyo anayamba kuthamangitsa Abineri. Iye sanafune kutembenukira kudzanja lamanja kapena lamanzere pamene anali kutsatira Abineri. 20  Atamuthamangitsa kwa kanthawi ndithu, Abineri anayang’ana kumbuyo ndi kunena kuti: “Kodi ndiwe Asaheli?” Poyankha, Asaheli anati: “Ndine.” 21  Pamenepo Abineri anamuuza kuti: “Tembenukira kudzanja lako lamanja kapena lamanzere ndipo ugwire mmodzi mwa anyamatawo, kuti utenge zimene ungamuvule+ zikhale zako.” Koma Asaheli sanafune kutembenuka ndi kusiya kumutsatira. 22  Kenako Abineri anauzanso Asaheli kuti: “Tembenuka ndipo usiye kunditsatira, chifukwa ndingakuphe.+ Tsopano ndikakupha ndidzaonana bwanji ndi m’bale wako Yowabu?” 23  Koma Asaheli anakanabe kutembenukira kwina. Choncho Abineri anamubaya* pamimba+ ndi chogwirira cha mkondo, ndipo mkondowo unatulukira kumsana kwake, moti anagwa pansi n’kufera pomwepo. Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, aliyense wofika pamalo amene Asaheli anagwera ndi kufa, anali kuima chilili+ ndi kudabwa kwambiri. 24  Zitatero, Yowabu ndi Abisai anathamangitsa Abineri. Pamene dzuwa linali kulowa, iwo anafika paphiri la Ama, limene lili pafupi ndi Giya panjira yopita kuchipululu cha Gibeoni.+ 25  Ana a Benjamini anayamba kusonkhana kumbuyo kwa Abineri monga gulu limodzi. Iwo anaimabe pamwamba paphiri limodzi. 26  Pamenepo Abineri anayamba kufuulira Yowabu kuti: “Kodi tipitiriza kuphana ndi lupanga mpaka liti?+ Kodi sukudziwa kuti mapeto ake zimenezi zibweretsa mavuto aakulu?+ Kodi uwauza liti anthuwa kuti atembenuke ndi kusiya kutsatira abale awo?”+ 27  Poyankha, Yowabu anati: “Pali Mulungu woona wamoyo,+ ukanapanda kulankhula,+ anthuwa sakanatembenuka aliyense wa iwo kusiya kutsatira m’bale wake kufikira m’mawa.” 28  Tsopano Yowabu analiza lipenga la nyanga ya nkhosa,+ ndipo anthu onse anaima, moti sanapitirizenso kuthamangitsa Isiraeli. Iwo sanayambirenso kumenyana. 29  Abineri ndi amuna amene anali kuyenda naye anayenda kudutsa ku Araba+ usiku wonse mpaka anakawoloka Yorodano.+ Iwo anayenda kudutsa chigwa chonsecho ndi kukafika ku Mahanaimu.+ 30  Chotero Yowabu anasiya kutsatira Abineri ndipo anayamba kusonkhanitsa anthu onse pamodzi. Pagulu la atumiki a Davide panasowa amuna 19 komanso Asaheli. 31  Koma atumiki a Davidewo anali atakantha amuna a Benjamini ndi amuna ena a Abineri, moti amuna 360 anafa.+ 32  Iwo ananyamula mtembo wa Asaheli+ ndi kukauika m’manda a bambo ake+ ku Betelehemu.+ Kenako Yowabu ndi amuna amene anali kuyenda naye anayenda usiku wonse, ndipo kunawachera atafika ku Heburoni.+

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza, “Malo a Mipeni ya Mwala wa Nsangalabwi.”
Ena amati “kugwaza.”