2 Samueli 21:1-22

21  Tsopano m’masiku a Davide kunagwa njala+ zaka zitatu zotsatizana. Choncho Davide anafunsira kwa Yehova, ndipo Yehova anamuuza kuti: “Sauli pamodzi ndi nyumba yake ali ndi mlandu wa magazi chifukwa anapha Agibeoni.”+  Choncho mfumu inaitana Agibeoni+ ndi kulankhula nawo. (Agibeoni sanali ana a Isiraeli koma otsala mwa Aamori.+ Ana a Isiraeli analumbira kwa Aamori,+ koma Sauli anali kufuna kuwapha+ onse chifukwa chakuti iye anali kuchitira nsanje+ ana a Isiraeli ndi ana a Yuda.)  Ndiyeno Davide anafunsa Agibeoni kuti: “Ndikuchitireni chiyani ndipo ndipereke chiyani kuti ndiphimbe tchimo+ limeneli, kuti inu mudalitse cholowa+ cha Yehova?”  Choncho Agibeoni anamuyankha kuti: “Sitikufuna siliva kapena golide+ pa nkhani ya Sauli ndi nyumba yake, komanso tilibe ufulu wopha munthu mu Isiraeli.” Ndiyeno Davide anati: “Chilichonse chimene mukufuna ndikuchitirani.”  Pamenepo iwo anauza mfumu kuti: “Tikufuna kuti munthu amene anapulula anthu athu,+ ndi kutikonzera chiwembu+ chotiwononga kuti tisapezeke m’dera lililonse la Isiraeli,  mutipatse ana ake aamuna 7,+ ndipo tionetse+ mitembo yawo kwa Yehova mwa kuipachika ku Gibeya,+ kwawo kwa Sauli, munthu amene Yehova+ anamusankha kukhala mfumu.” Pamenepo mfumu inati: “Ndiwapereka m’manja mwanu.”  Koma mfumu inamvera chisoni Mefiboseti+ mwana wamwamuna wa Yonatani, mwana wa Sauli, chifukwa cha lumbiro+ limene Davideyo ndi Yonatani mwana wa Sauli anachita pakati pawo pamaso pa Yehova.  Chotero mfumu inatenga Arimoni ndi Mefiboseti, amene anali ana awiri aamuna a Rizipa,+ mwana wamkazi wa Aya, amene Rizipayo anaberekera Sauli. Anatenganso ana aamuna asanu a Mikala,*+ mwana wamkazi wa Sauli, amene anaberekera Adiriyeli,+ mwana wa Barizilai Mmeholati.  Iye anawapereka m’manja mwa Agibeoni, ndipo Agibeoniwo anaonetsa mitembo ya ana aamuna a Sauliwo kwa Yehova+ paphiri, moti onse 7 anafera limodzi. Iwo anaphedwa m’masiku oyambirira a nyengo yokolola, kuchiyambi kwa nyengo yokolola balere.+ 10  Koma Rizipa mwana wamkazi wa Aya+ anatenga chiguduli+ ndi kuchiyala pamwala kuti azikhala pamenepo, kuyambira kuchiyambi kwa nyengo yokolola kufikira pamene mvula inagwa pamitemboyo kuchokera kumwamba.+ Iye sanalole mbalame+ zam’mlengalenga kutera pamitemboyo masana, ndipo usiku sanalole zilombo zakutchire+ kufikapo. 11  Patapita nthawi, Davide anauzidwa+ zimene Rizipa mwana wa Aya, mdzakazi wa Sauli anachita. 12  Chotero Davide anapita kukatenga mafupa a Sauli+ ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-giliyadi.+ Anthuwo ndiwo anaba mitembo ya Sauli ndi Yonatani m’bwalo la mzinda wa Beti-sani,+ kumene Afilisiti anali ataipachika,+ tsiku limene anapha Sauli paphiri la Giliboa.+ 13  Iye anabwera ndi mafupa a Sauli ndi mafupa a Yonatani mwana wake. Atatero anasonkhanitsanso mafupa a anthu amene anaonetsedwa aja.+ 14  Kenako anaika mafupa a Sauli ndi Yonatani mwana wake m’dziko la Benjamini ku Zela+ m’manda a Kisi+ bambo ake, kuti achite zonse zimene mfumu inalamula. Izi zitachitika, Mulungu anamvetsera kuchonderera kwawo kuti amvere chisoni dziko lawo.+ 15  Ndiyeno Afilisiti+ anabwera kudzachita nkhondo ndi Isiraeli. Pamenepo Davide ndi atumiki ake anapita komweko n’kumenyana ndi Afilisiti, ndipo Davide anatopa. 16  Zitatero, Isibi-benobi mmodzi wa mbadwa za Arefai,+ amene anali ndi mkondo wamkuwa wolemera+ masekeli 300,* amenenso anali ndi lupanga latsopano m’chiuno mwake, anaganiza zoti aphe Davide. 17  Nthawi yomweyo Abisai+ mwana wa Zeruya anathandiza+ Davide ndipo anakantha Mfilisitiyo ndi kumupha. Pamenepo asilikali a Davide analumbira kwa iye kuti: “Simudzapitanso ndi ife kunkhondo,+ chifukwa mungazimitse+ nyale+ ya Isiraeli!” 18  Ndiyeno pambuyo pa nkhondo imeneyi panabukanso nkhondo ndi Afilisiti ku Gobu. Pa nthawi imeneyo Sibekai+ Mhusati+ anapha Safi, amene anali mmodzi mwa mbadwa za Arefai.+ 19  Kenako panabukanso nkhondo ina ndi Afilisiti ku Gobu, ndipo Elihanani+ mwana wa Yaare-oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliyati Mgiti, amene mtengo wa mkondo wake unali waukulu ngati mtanda wa owomba nsalu.+ 20  Panabukanso nkhondo ina ku Gati,+ pa nthawi imene kunali munthu wa msinkhu waukulu modabwitsa. Iye anali ndi zala 6 kudzanja lililonse ndiponso zala 6 kuphazi lililonse, moti anali ndi zala 24 zonse pamodzi. Ameneyunso anali mmodzi mwa mbadwa za Arefai.+ 21  Iye anali kutonza+ ndi kuderera Isiraeli. Pamapeto pake Yonatani+ mwana wa Simeyi,+ m’bale wake wa Davide, anamupha. 22  Anthu anayi amenewa anali mbadwa za Arefai ku Gati.+ Iwo anaphedwa ndi dzanja la Davide ndi la atumiki ake.+

Mawu a M'munsi

Mipukutu ya Targum imati: “Ana aamuna asanu amene Merabu anabereka (amene Mikala, mwana wamkazi wa Sauli, analera).” Yerekezerani ndi 2Sa 6:23.
Pafupifupi makilogalamu atatu ndi hafu.