2 Samueli 23:1-39
23 Mawu omaliza amene Davide ananena ndi awa:+“Mawu a Davide mwana wa Jese,+Mawu a munthu wamphamvu amene anakwezedwa pamwamba,+Wodzozedwa+ wa Mulungu wa Yakobo,Munthu wosangalatsa wotchulidwa m’nyimbo zokoma+ za Isiraeli.
2 Mzimu wa Yehova unandilankhulitsa,+Ndipo mawu ake anali palilime langa.+
3 Mulungu wa Isiraeli analankhula,Thanthwe la Isiraeli linandiuza kuti,+‘Munthu wolamulira anthu akakhala wolungama,+N’kumalamulira moopa Mulungu,+
4 Ulamuliro wake umakhala ngati kuwala kwa m’mawa pamene dzuwa lawala,+M’mawa wopanda mitambo.Umakhala ngati msipu womera padziko mvula ikakata, dzuwa n’kuwala.’+
5 Kodi si mmene nyumba yanga ilili kwa Mulungu?+Chifukwa chakuti anachita nane pangano lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+Analikonza bwino ndipo n’lotetezeka.+Chifukwa ndilo chipulumutso changa+ ndi chondikondweretsa,Kodi chimenechi sindicho chifukwa chake adzakulitsa panganoli?+
6 Koma anthu onse opanda pake+ amawakankhira kutali+ ngati zitsamba zaminga.+Pakuti zitsamba zamingazo sizigwiridwa ndi manja pozichotsa.
7 Munthu akamazigwiraAyenera kukhala ndi zida zachitsulo ndi mkondo,Ndipo zidzatenthedwa ndi moto n’kupseratu.”+
8 Mayina a amuna amphamvu+ a Davide ndi awa: Yosebu-basebete+ Mtahakemoni, mtsogoleri wa amuna atatu. Iye anatenga mkondo wake n’kupha anthu 800 ulendo umodzi.
9 Womutsatira anali Eleazara+ mwana wa Dodo+ mwana wa Ahohi. Iye anali mmodzi mwa amuna atatu amphamvu amene anali ndi Davide pamene anatonza Afilisiti. Iwo anasonkhana kumeneko kuti amenye nkhondo, ndipo amuna a Isiraeli anali atathawa.+
10 Eleazara ndi amene anaimirira ndipo anali kupha Afilisiti mpaka dzanja lake linatopa, koma anagwirabe lupanga+ moti Yehova anapereka chipulumutso chachikulu pa tsiku limenelo.+ Koma anthu ena onse anamutsatira pambuyo pake kuti avule zovala za anthu ophedwawo.+
11 Womutsatira anali Shama, mwana wamwamuna wa Age Mharari.+ Tsopano Afilisiti anasonkhana pamodzi ku Lehi, kumene kunali munda wodzaza ndi mphodza.+ Kumeneko anthu anali atathawa chifukwa choopa Afilisitiwo.
12 Koma iye anaima pakati pa kachigawo ka mundako ndi kukalanditsa ndipo anapitiriza kupha Afilisiti, moti tsiku limenelo Yehova anapereka chipulumutso chachikulu.+
13 Ndiyeno pa nthawi yokolola, atatu mwa atsogoleri 30+ anapita kwa Davide kuphanga la Adulamu.+ Apa n’kuti Afilisiti atamanga msasa wa mahema m’chigwa cha Arefai.+
14 Pamenepo n’kuti Davide ali m’malo ovuta kufikako,+ ndiponso n’kuti mudzi wa asilikali+ a Afilisiti uli ku Betelehemu.
15 Patapita nthawi, Davide anafotokoza zimene anali kulakalaka kuti: “Ndikanakonda ndikanamwa madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu chimene chili pachipata!”+
16 Pamenepo amuna atatu amphamvu aja anakalowa mwamphamvu mumsasa wa Afilisiti, n’kutunga madzi m’chitsime cha ku Betelehemu chimene chinali pachipata. Atatero ananyamula madziwo n’kupita nawo kwa Davide.+ Koma iye anakana kumwa madziwo. M’malomwake anawapereka kwa Yehova mwa kuwathira pansi.+
17 Ndiyeno iye anati: “Sindingachite zimenezo+ inu Yehova! Kodi ndimwe magazi+ a amuna amene anaika miyoyo yawo pangozi kuti akatunge madziwa?” Choncho iye sanavomere kumwa madziwo.
Izi n’zimene amuna atatu amphamvuwo anachita.
18 Koma Abisai,+ m’bale wake wa Yowabu mwana wa Zeruya+ anali mtsogoleri wa anthu 30 amenewo. Iye ananyamula mkondo ndi kupha nawo anthu 300. Abisai anali wotchuka ngati amuna atatu aja.+
19 Ngakhale kuti anali wolemekezeka kwambiri kuposa amuna ena 30 aja, ndipo anali mtsogoleri wawo, komabe sanafanane ndi amuna atatu oyamba aja.+
20 Benaya+ mwana wa Yehoyada,+ mwana wa munthu wolimba mtima, anachita zinthu zambiri ku Kabizeeli.+ Iye anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Mowabu, ndipo analowanso m’chitsime chopanda madzi n’kupha mkango+ umene unali m’chitsimemo pa tsiku limene kunagwa chipale chofewa.+
21 Benaya ndiye anaphanso Mwiguputo wa msinkhu waukulu modabwitsa.+ Ngakhale kuti Mwiguputoyo anali ndi mkondo m’manja mwake, Benaya anapitabe kukakumana naye atanyamula ndodo, n’kulanda mkondowo ndipo anamupha ndi mkondo wake womwewo.+
22 Zimenezi n’zimene Benaya+ mwana wa Yehoyada anachita. Iye anali wotchuka ngati amuna atatu amphamvu aja.+
23 Ngakhale kuti anali wolemekezeka kwambiri kuposa amuna ena 30 aja, sanafanane ndi amuna atatu aja. Koma Davide anamuika kukhala msilikali wake womulondera.+
24 Asaheli+ m’bale wake wa Yowabu anali m’gulu la amuna 30 aja. M’gululi munalinso Elihanani+ mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,
25 Shama+ Mharodi, Elika Mharodi,
26 Helezi+ Mpaliti, Ira+ mwana wa Ikesi+ Mtekowa,
27 Abi-ezeri+ Muanatoti,+ Mebunai Mhusati,+
28 Zalimoni Mwahohi,+ Maharai+ Mnetofa,
29 Helebi+ mwana wa Bana Mnetofa, Itai+ mwana wa Ribai wa ku Gibeya wa fuko la ana a Benjamini,
30 Benaya+ Mpiratoni, Hidai wa kuzigwa* za Gaasi,+
31 Abi-aliboni Mwaraba, Azimaveti+ M’bahurimu,
32 Eliyaba Msaaliboni, ana a Yaseni, Yonatani,+
33 Shama Mharari, Ahiyamu+ mwana wa Sarari Mharari,
34 Elifeleti mwana wa Ahasibai, mwana wa Mmaakati, Eliyamu mwana wa Ahitofeli+ Mgilo,
35 Heziro+ wa ku Karimeli, Paarai Mwarabu,
36 Igali mwana wa Natani+ wa ku Zoba, Bani Mgadi,
37 Zeleki+ Muamoni, Naharai M’beeroti, onyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya,
38 Ira Muitiri,+ Garebi+ Muitiri,
39 ndi Uriya+ Mhiti, onse pamodzi 37.