2 Samueli 8:1-18
8 Pambuyo pake, Davide anapha Afilisiti+ ndi kuwagonjetsa,+ ndipo anawalanda mzinda wa Metege-ama.
2 Davide anagonjetsanso Amowabu+ ndi kuwayeza ndi chingwe. Iye anawagoneka pansi kuti ayeze zingwe ziwiri ndi kuwapha, ndiponso chingwe chimodzi chathunthu n’kuwasiya amoyo.+ Choncho Amowabu anakhala atumiki a Davide+ ndipo anali kukhoma msonkho kwa iye.+
3 Davide anapha Hadadezeri,+ mwana wa Rehobu mfumu ya Zoba,+ pamene Hadadezeriyo anali kupita kumtsinje wa Firate+ kukabwezeretsa ulamuliro wake kumeneko.
4 Davide anagwira amuna 1,700 okwera pamahatchi ndi amuna 20,000 oyenda pansi+ a Hadadezeri. Kenako Davide anapundula*+ mahatchi onse a magaleta+ kusiyapo mahatchi a magaleta okwana 100.
5 Pamene Asiriya a ku Damasiko+ anabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba, Davide anapha amuna 22,000 a ku Siriya.+
6 Kenako Davide anamanga midzi ya asilikali+ m’dera la Asiriya a ku Damasiko ndipo Asiriyawo anakhala akapolo a Davide moti anali kukhoma msonkho+ kwa iye. Yehova anapitiriza kupulumutsa Davide kulikonse kumene wapita.+
7 Komanso Davide anatenga zishango zozungulira+ zagolide zimene zinali ndi atumiki a Hadadezeri ndipo anabwera nazo ku Yerusalemu.
8 Mfumu Davide inatenga mkuwa wochuluka kwambiri+ ku Beta ndi Berota, mizinda ya Hadadezeri.
9 Tsopano Toi, mfumu ya Hamati+ anamva kuti Davide wapha gulu lonse lankhondo la Hadadezeri.+
10 Choncho Toi anatumiza Yoramu mwana wake kwa Mfumu Davide kukamufunsa za moyo wake+ ndi kumuyamikira chifukwa chomenyana ndi Hadadezeri ndi kumugonjetsa (pakuti Hadadezeri ndi Toi anali kumenyana kawirikawiri). Popita kwa Davide, Yoramu anatenga zinthu zasiliva, zagolide ndi zamkuwa.+
11 Zinthu zimenezi Mfumu Davide inazipatulira Yehova pamodzi ndi siliva ndi golide wochokera ku mitundu yonse imene inagonjetsa.+
12 Inapatula siliva ndi golide wochokera ku Siriya, Mowabu,+ kwa ana a Amoni, Afilisiti,+ Aamaleki+ ndiponso siliva ndi golide amene anafunkha kwa Hadadezeri mwana wa Rehobu mfumu ya Zoba.+
13 Ndipo Davide anadzipangira dzina atabwerako kumene anapha Aedomu 18,000+ m’chigwa cha Mchere.+
14 Davide anakhazikitsa midzi ya asilikali mu Edomu.+ Mu Edomu yense anaikamo midzi ya asilikali, moti Aedomu anakhala antchito a Davide+ ndipo Yehova anali kupulumutsa Davide kulikonse kumene anali kupita.+
15 Davide anapitiriza kulamulira Isiraeli+ yense ndipo nthawi zonse anali kupereka zigamulo ndi kuchita chilungamo+ kwa anthu ake onse.+
16 Yowabu+ mwana wa Zeruya anali mkulu wa asilikali, ndipo Yehosafati+ mwana wa Ahiludi anali wolemba zochitika.
17 Zadoki+ mwana wa Ahitubu ndi Ahimeleki+ mwana wa Abiyatara anali ansembe, pamene Seraya anali mlembi.
18 Benaya+ mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti+ ndi Apeleti.+ Ana aamuna a Davide anakhala ansembe.*+
Mawu a M'munsi
^ Anali kuzipundula mwa kudula mtsempha wakuseri kwa mwendo wam’mbuyo.
^ Kapena kuti “nduna zazikulu zotumikira mfumu.”