2 Timoteyo 1:1-18

1  Ine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu,+ malinga ndi lonjezo la moyo+ loperekedwa kwa ogwirizana ndi Khristu Yesu,+  ndikulembera iwe Timoteyo mwana wanga wokondedwa:+ Kukoma mtima kwakukulu, chifundo, ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu+ zikhale nawe.  Ndikuyamika Mulungu, amene ndikumuchitira utumiki wopatulika+ monga mmene makolo anga+ anachitira, ndipo ndikuuchita ndi chikumbumtima choyera.+ Ndikumuyamika chifukwa chakuti sindiiwala za iwe m’mapembedzero anga,+ usana ndi usiku,  ndipo ndikakumbukira misozi yako ndimalakalaka kukuona+ kuti ndidzasangalale kwambiri.  Pakuti ndikukumbukira chikhulupiriro+ chopanda chinyengo+ chimene uli nacho, chimene chinayamba kukhazikika mwa agogo ako aakazi a Loisi, ndi mayi ako a Yunike, ndipo ndikukhulupirira kuti chilinso mwa iwe.  Pa chifukwa chimenechi, ndikukukumbutsa kuti mphatso+ ya Mulungu imene ili mwa iwe, yomwe unailandira pamene ndinaika manja anga pa iwe,+ uikolezere ngati moto.+  Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wamantha,+ koma wamphamvu,+ wachikondi, ndi woti tiziganiza bwino.+  Chotero, usachite manyazi ndi ntchito yochitira umboni za Ambuye wathu,+ kapena za ineyo amene ndine mkaidi chifukwa cha iye.+ Khala wokonzeka kumva zowawa+ mu mphamvu ya Mulungu+ chifukwa cha uthenga wabwino.  Iye anatipulumutsa+ ndi kutiitana kuti tikhale oyera,+ osati chifukwa cha ntchito zathu,+ koma mwa chifuniro chake ndi kukoma mtima kwake kwakukulu. Iye anatikomera mtima m’njira imeneyi kalekalelo mwa Khristu Yesu.+ 10  Koma tsopano izi zatsimikizirika bwino chifukwa cha kuonekera+ kwa Mpulumutsi wathu Khristu Yesu, amene wathetsa mphamvu imfa.+ Kudzera mu uthenga wabwino,+ iye watidziwitsa bwinobwino+ mmene tingapezere moyo+ wosawonongeka.+ 11  Uthenga wabwino umenewu ndi umene anandiikira kuti ndikhale mlaliki, mtumwi ndi mphunzitsi.+ 12  N’chifukwa chake ndikuvutika chonchi,+ koma sindikuchita manyazi.+ Pakuti ndikudziwa amene ndikumukhulupirira, ndipo ndikukhulupirira kuti adzasunga+ chimene ndachiika m’manja mwake kufikira tsikulo.+ 13  Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olondola+ amene unawamva kwa ine, komanso chikhulupiriro ndi chikondi zomwe zili mwa Khristu Yesu.+ 14  Chuma chapadera+ chimene anachiika m’manja mwakochi, uchisunge mothandizidwa ndi mzimu woyera umene uli mwa ife.+ 15  Iwe ukudziwa kuti anthu onse m’chigawo cha Asia+ andisiya.+ Ena mwa iwo ndi Fugelo ndi Heremogene. 16  Ambuye achitire chifundo banja la Onesiforo,+ chifukwa iye anali kubwera kawirikawiri kudzandilimbikitsa,+ ndipo sanachite manyazi ndi maunyolo anga.+ 17  M’malomwake, pamene anali ku Roma, anandifunafuna mwakhama mpaka anandipeza.+ 18  Ambuye amulole kukapeza chifundo+ chochokera kwa Yehova m’tsikulo.+ Za utumiki wonse umene anachita ku Efeso, iwe ukuzidziwa bwino.

Mawu a M'munsi