Aefeso 5:1-33

5  Chotero muzitsanzira Mulungu,+ monga ana ake okondedwa,  ndipo yendanibe m’chikondi,+ monganso Khristu anakukondani+ n’kudzipereka yekha chifukwa cha inu. Iye anadzipereka yekha monga chopereka+ ndiponso monga nsembe yafungo lokoma kwa Mulungu.+  Dama*+ ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo+ zisatchulidwe n’komwe pakati panu,+ monga mmene anthu oyera amayenera kuchitira.+  Musatchule ngakhale za khalidwe lochititsa manyazi,+ nkhani zopusa kapena nthabwala zotukwana,+ zomwe ndi zinthu zosayenera. M’malomwake, muziyamika Mulungu.+  Pakuti mfundo iyi mukuidziwa, ndipo mukuimvetsa bwino, kuti wadama+ kapena wodetsedwa kapena waumbombo,+ umene ndiwo kupembedza mafano, sadzalowa mu ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.+  Munthu asakupusitseni ndi mawu opanda pake,+ pakuti mkwiyo wa Mulungu udzafika pa ana a kusamvera, ochita zinthu zimene ndatchulazi.+  Choncho musachite nawo zimenezo.+  Pakuti poyamba munali mdima,+ koma tsopano ndinu kuwala+ mogwirizana ndi Ambuye. Yendanibe ngati ana a kuwala.  Pakuti zipatso za kuwala ndizo chilichonse chabwino ndi chilichonse cholungama ndi choona.+ 10  Nthawi zonse muzitsimikiza kuti chovomerezeka+ kwa Ambuye n’chiti, 11  ndipo musamachite nawo+ ntchito zosapindulitsa za mu mdima.+ M’malomwake, muzidzudzula ntchitozo.+ 12  Pakuti zimene iwo amachita mseri n’zochititsa manyazi ngakhale kuzitchula.+ 13  Tsopano zinthu zimene zikudzudzulidwa+ zimaonekera poyera chifukwa cha kuwala, pakuti chilichonse chimene chaonekera+ chimakhala kuwala. 14  N’chifukwa chake iye akunena kuti: “Dzuka,+ wogona iwe! Uka kwa akufa,+ ndipo Khristu adzakuunika.”+ 15  Choncho samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera+ si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. 16  Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu*+ chifukwa masikuwa ndi oipa.+ 17  Pa chifukwa chimenechi, lekani kukhala opanda nzeru, koma pitirizani kuzindikira+ chifuniro+ cha Yehova. 18  Ndiponso, musamaledzere naye vinyo,+ mmene muli makhalidwe oipa,+ koma khalanibe odzaza ndi mzimu.+ 19  Mukakhala pakati panu muziimba masalimo,+ nyimbo zotamanda+ Mulungu, ndiponso nyimbo zauzimu. Muziimba+ nyimbo zotamanda+ Yehova m’mitima mwanu, 20  m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu. Nthawi zonse muziyamika+ Mulungu, Atate wathu, pa zinthu zonse. 21  Gonjeranani+ poopa Khristu. 22  Akazi agonjere+ amuna awo ngati mmene amagonjerera Ambuye, 23  chifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake+ monganso mmene Khristu alili mutu wa mpingo,+ pokhala mpulumutsi wa thupilo. 24  Ndipotu, monga mmene mpingo umagonjerera Khristu, akazinso agonjere amuna awo m’chilichonse.+ 25  Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu+ monga mmene Khristu anakondera mpingo n’kudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo,+ 26  ndipo anauyeretsa+ pousambitsa m’madzi a mawu a Mulungu.+ 27  Anatero kuti iyeyo alandire mpingowo uli wokongola ndiponso waulemerero,+ wopanda banga kapena makwinya kapenanso chilichonse cha zinthu zotero, koma kuti ukhale woyera ndi wopanda chilema.+ 28  Mwa njira imeneyi amuna akonde akazi awo monga matupi awo. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, 29  pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda,+ mmenenso Khristu amachitira ndi mpingo, 30  chifukwa ndife ziwalo za thupi lake.+ 31  “Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”+ 32  Chinsinsi chopatulika+ chimenechi n’chachikulu. Tsopano ndikulankhula za Khristu ndi mpingo.+ 33  Komabe, aliyense wa inu akonde mkazi wake+ ngati mmene amadzikondera yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambiri+ mwamuna wake.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 7.
Mawu ake enieni, “muzigula nthawi yoikidwa.”