Agalatiya 3:1-29
3 Kalanga ine, Agalatiya opusa inu! Kodi ndani anakupotozani maganizo,+ inu amene munakhala ngati mwaona Yesu Khristu atapachikidwa pamtengo?+
2 Ndikufuna mundiuze: Kodi munalandira mzimu+ chifukwa cha ntchito za chilamulo+ kapena chifukwa chokhulupirira zimene munamva?+
3 Kodi ndinu opusa chonchi? Munayamba ndi kudalira mzimu,+ kodi tsopano mukufuna kumaliza ndi kudalira zinthu zochokera kwa anthu opanda ungwiro?+
4 Kodi kuvutika konse kuja kunangopita pachabe?+ Ndikukhulupirira kuti sikunapite pachabe.
5 Iye amene amakupatsani mzimu+ ndi kuchita zinthu zamphamvu+ pakati panu, kodi amazichita chifukwa chakuti inuyo mukuchita ntchito za chilamulo kapena chifukwa chakuti munakhulupirira uthenga wabwino umene munamva?
6 Zili monga mmene Abulahamu “anakhulupirira mwa Yehova, ndipo Mulunguyo anamuona Abulahamu ngati wolungama.”+
7 Ndithudi mukudziwa kuti amene amakhalabe ndi chikhulupiriro+ ndiwo ana a Abulahamu.+
8 Ndiyeno, Malemba ataoneratu kuti Mulungu adzayesa anthu a mitundu ina kukhala olungama chifukwa cha chikhulupiriro, analengezeratu uthenga wabwino kwa Abulahamu, kuti: “Kudzera mwa iwe, mitundu yonse idzadalitsidwa.”+
9 Chotero, amene akugwiritsitsa chikhulupiriro akudalitsidwa+ limodzi ndi Abulahamu wokhulupirikayo.+
10 Pakuti onse odalira ntchito za chilamulo ndi otembereredwa, chifukwa Malemba amati: “Ndi wotembereredwa aliyense wosapitiriza kuyenda m’zinthu zonse zolembedwa mumpukutu wa Chilamulo ndi kuzichita.”+
11 Komanso, mfundo yakuti palibe munthu amene angaonedwe ngati wolungama+ ndi Mulungu mwa chilamulo ndi yoonekeratu, chifukwa “wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.”+
12 Tsopano, Chilamulo sichidalira chikhulupiriro, koma “wochita za m’Chilamulo adzakhala ndi moyo potsatira chilamulocho.”+
13 Khristu anatigula+ ndi kutimasula+ ku temberero la Chilamulo ndipo iyeyo anakhala temberero+ m’malo mwa ife, chifukwa Malemba amati: “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.”+
14 Cholinga chake chinali chakuti mitundu ipeze madalitso amene Abulahamu analonjezedwa kudzera mwa Yesu Khristu,+ kuti tidzalandire mzimu wolonjezedwawo+ chifukwa cha chikhulupiriro chathu.+
15 Abale, ndipereke fanizo mogwirizana ndi zimene zimachitika pakati pa anthu: Pangano likakhazikitsidwa, ngakhale kuti ndi pangano la anthu, palibe angachotsepo kapena kuwonjezerapo mfundo zina.+
16 Tsopano, malonjezo anaperekedwa kwa Abulahamu+ ndi kwa mbewu yake.+ Malemba sanena kuti: “Kwa mbewu zako,” ngati kuti mbewuzo n’zambiri, koma amanena za mbewu imodzi+ kuti: “Kwa mbewu yako,”+ amene ndi Khristu.+
17 Komanso ineyo ndikuti: Chilamulo chimene chinadzakhalapo zaka 430+ pambuyo pa panganolo, limene kalekalelo linatsimikizidwa ndi Mulungu,+ sichingathetse mphamvu ya panganolo, kapena kufafaniza lonjezolo.+
18 Pakuti ngati cholowa chimene Mulungu amapereka chimadzera m’chilamulo, ndiye kuti sichidaliranso lonjezo,+ koma Mulungu mokoma mtima wachipereka kwa Abulahamu mwa lonjezo.+
19 Nanga tsopano Chilamulo chinakhalapo chifukwa chiyani? Anachiwonjezerapo kuti machimo aonekere,+ mpaka amene ali mbewuyo atafika,+ amene anapatsidwa lonjezolo. Ndipo Chilamulocho chinaperekedwa kudzera mwa angelo,+ kudzeranso m’dzanja la mkhalapakati.+
20 Tsopano, sipakhala mkhalapakati ngati pangano lili la munthu mmodzi yekha, koma Mulungu anali yekha.+
21 Chotero kodi Chilamulo chimatsutsa malonjezo a Mulungu?+ Zimenezo sizingachitike ngakhale pang’ono. Pakanaperekedwa lamulo lopatsa moyo,+ bwenzi chilungamo chikudzera m’chilamulo.+
22 Koma Malemba+ anatsekera zinthu zonse n’kuziika pansi pa uchimo,+ kuti lonjezolo, limene limakhalapo mwa kukhulupirira Yesu Khristu, liperekedwe kwa okhulupirirawo.+
23 Komabe chikhulupirirocho chisanafike,+ chilamulo chinali kutiyang’anira+ ndipo chinatiika mu ukapolo. Pa nthawi imeneyo, tinali tikuyembekezera chikhulupiriro chimene chinali kudzaonekera.+
24 N’chifukwa chake Chilamulo chakhala mtsogoleri* wotifikitsa kwa Khristu,+ kuti tiyesedwe olungama+ chifukwa cha chikhulupiriro.
25 Koma popeza chikhulupirirocho tsopano chafika,+ sitilinso pansi pa mtsogoleriyo.+
26 Koma nonsenu ndinu ana+ a Mulungu chifukwa cha chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu.
27 Pakuti nonsenu amene munabatizidwa mwa Khristu+ mwavala Khristu.+
28 Palibe Myuda kapena Mgiriki,+ palibe kapolo kapena mfulu,+ palibenso mwamuna kapena mkazi.+ Nonsenu ndinu munthu mmodzi mwa Khristu Yesu.+
29 Ndiponso ngati muli a Khristu, ndinudi mbewu ya Abulahamu,+ olandira cholowa mogwirizana ndi lonjezolo.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu achigiriki amene tawamasulira kuti “mtsogoleri” amatanthauza munthu amene anali kugwira ntchito yoyang’anira kapena kuteteza ana.