Agalatiya 5:1-26

5  Khristu anatimasula kuti tikhale ndi ufulu umenewu.+ Chotero khalani olimba,+ ndipo musalole kumangidwanso m’goli laukapolo.+  Tamverani! Ine Paulo, ndikukuuzani kuti mukadulidwa,+ Khristu sadzakhala waphindu kwa inu.  Kuwonjezera apo, ndikunenetsa kwa munthu aliyense amene akudulidwa, kuti afunikanso kuchita zonse za m’Chilamulo.+  Inuyo amene mukufuna kuyesedwa olungama mwa chilamulo, mwadzilekanitsa ndi Khristu,+ kaya mukhale ndani, mwagwera kunja kwa kukoma mtima kwake kwakukulu.+  Koma kudzera mwa mzimu, ife tikuyembekezera mwachidwi chilungamo cholonjezedwacho, chimene chimadza mwa chikhulupiriro.+  Pakuti kwa Khristu Yesu, kudulidwa kapena kusadulidwa zilibe phindu,+ koma chikhulupiriro+ chimene chimagwira ntchito kudzera m’chikondi.+  Munali kuthamanga bwino.+ Anakusokonezani ndani kuti musapitirize kumvera choonadi?+  Kukopeka kumeneku sikunachokere kwa Iye amene anakuitanani.+  Chofufumitsa chaching’ono chimafufumitsa mtanda wonse.+ 10  Ndikukhulupirira+ kuti inu amene muli ogwirizana+ ndi Ambuye, simudzasintha maganizo, koma munthu amene amakuvutitsani,+ adzaweruzidwa+ kaya akhale ndani. 11  Kunena za ine abale, ngati ndimalalikirabe kuti anthu azidulidwa, n’chifukwa chiyani ndikuzunzidwabe? Ndithudi, mtengo wozunzikirapo,+ womwe ndi chopunthwitsa,+ ukanakhala utachotsedwa.+ 12  Ndikanakonda kuti anthu amene akufuna kukupotozani maganizo,+ afulidwe.+ 13  Zoonadi abale, munaitanidwa kuti mukhale aufulu,+ musayese ngakhale pang’ono kugwiritsa ntchito ufulu umenewu polimbikitsira zilakolako za thupi,+ koma tumikiranani mwachikondi.+ 14  Pakuti Chilamulo chonse chimakwaniritsidwa+ m’mawu akuti: “Uzikonda mnzako ngati mmene umadzikondera wekha.”+ 15  Koma mukamalumana ndi kudyana nokhanokha,+ chenjerani kuti mungawonongane.+ 16  M’malomwake ndikuti, Pitirizani kuyenda mwa mzimu,+ ndipo simudzatsatira chilakolako cha thupi ngakhale pang’ono.+ 17  Pakuti zilakolako za thupi zimalimbana ndi mzimu,+ mzimunso umalimbana ndi thupi. Zinthu ziwiri zimenezi zimatsutsana, choncho zinthu zimene mumafuna kuchita simuzichita.+ 18  Komanso ngati mukutsogoleredwa ndi mzimu,+ simuli pansi pa chilamulo.+ 19  Tsopano, ntchito za thupi zimaonekera.+ Ntchitozi ndizo dama,*+ zinthu zodetsa, khalidwe lotayirira,+ 20  kupembedza mafano, kuchita zamizimu,+ udani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko, 21  kaduka, kumwa mwauchidakwa,*+ maphwando aphokoso, ndi zina zotero. Ponena za zinthu zimenezi, ndikukuchenjezeranitu, ngati mmene ndinachitira poyamba paja, kuti anthu amene amachita zimenezi+ sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.+ 22  Koma makhalidwe* amene mzimu woyera umatulutsa+ ndiwo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino,+ chikhulupiriro, 23  kufatsa ndi kudziletsa.+ Palibe lamulo loletsa zinthu zoterezi.+ 24  Ndiponso anthu amene ali a Khristu Yesu, anapachika thupi lawo pamodzi ndi zikhumbo zake ndi zilakolako zake.+ 25  Ngati tikukhala mwa mzimu, tiyeninso tipitirize kuyenda motsogoleredwa ndi mzimuwo.+ 26  Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano+ pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 7.
Mawu achigiriki amene tawamasulira kuti “kumwa mwauchidakwa” amatanthauza kumwa mowa kwambiri ndiponso mosadziletsa n’cholinga chofuna kuledzera.
Mawu ake enieni, “chipatso.”