Aheberi 2:1-18
2 Ndiye chifukwa chake n’kofunika kuti tiganizire mozama, kuposa nthawi zonse, zinthu zimene tinamva,+ kuti tisatengeke pang’onopang’ono n’kusiya chikhulupiriro.+
2 Pakuti ngati mawu amene angelo ananena+ analidi osagwedezeka, ndipo pa tchimo lililonse ndi kusamvera kulikonse, chilango chinaperekedwa mogwirizana ndi chilungamo,+
3 tidzapulumuka bwanji+ ngati tanyalanyaza+ chipulumutso chachikulu chonchi?+ Ambuye wathu ndi amene anayamba kunena za chipulumutso chimenechi,+ ndipo anthu amene anamumva anatitsimikizira zimenezo.+
4 Mulungu nayenso anachitira umboni za chipulumutsocho ndi zizindikiro, zinthu zodabwitsa, ntchito zamphamvu zosiyanasiyana+ komanso mwa kupereka mphatso zosiyanasiyana+ za mzimu woyera malinga ndi chifuniro chake.+
5 Pakuti dziko lapansi lokhalamo anthu limene likubweralo,+ limene ife tikunena, sanaliike pansi pa ulamuliro wa angelo.
6 Koma mboni ina inachitira umboni penapake, kuti: “Munthu ndani kuti muzimuganizira,+ kapena mwana wa munthu ndani kuti muzimusamalira?+
7 Munamutsitsa pang’ono poyerekeza ndi angelo. Munamuveka ulemerero ndi ulemu+ monga chisoti chachifumu, ndipo munamuika kuti alamulire ntchito za manja anu.+
8 Zinthu zonse munaziika pansi pa mapazi ake.”+ Popeza kuti anaika zinthu zonse pansi pa mwana wake,+ Mulungu sanasiye kanthu kalikonse, osakaika pansi pa mwana wakeyo.+ Komabe, padakali pano sitikuona kuti zinthu zonse zili pansi pake.+
9 Koma tikuona Yesu, amene pa nthawi ina anamutsitsa pang’ono poyerekeza ndi angelo.+ Tikumuona atamuveka ulemerero+ ndi ulemu ngati chisoti chachifumu chifukwa chakuti anazunzika mpaka imfa.+ Zimenezi zinamuchitikira kuti mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.+
10 Zinthu zonse zilipo kuti zipereke ulemerero kwa Mulungu ndipo zinakhalapo kudzera mwa iye.+ Choncho pamene akuika ana ambiri pa ulemerero,+ n’koyenera kuti achititse Mtumiki Wamkulu+ wa chipulumutso chawo kukhala wangwiro kudzera m’masautso.+
11 Pakuti onse, woyeretsayo ndi amene akuyeretsedwawo,+ amachokera kwa mmodzi.+ Pa chifukwa chimenechi, iye sachita manyazi kuwatcha “abale,”+
12 pamene akunena kuti: “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga. Ndidzakutamandani mwa kuimba nyimbo pakati pa mpingo.”+
13 Komanso pamene akunena kuti: “Ndidzadalira iye.”+ Ndi kutinso: “Taonani! Ine ndi ana amene Yehova anandipatsa.”+
14 Chotero, popeza kuti “ana” amenewo onse ndi amagazi ndi mnofu, iyenso anakhala wamagazi ndi mnofu.+ Anachita izi kuti kudzera mu imfa yake,+ awononge+ Mdyerekezi,+ amene ali ndi njira yobweretsera imfa.+
15 Anachitanso zimenezi kuti amasule+ onse amene poopa imfa,+ anali mu ukapolo moyo wawo wonse.+
16 Pakuti iye sakuthandiza angelo ngakhale pang’ono, koma akuthandiza mbewu ya Abulahamu.+
17 Chotero, iye anayenera ndithu kukhala ngati “abale” ake m’zonse,+ kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika pa zinthu za Mulungu.+ Cholinga chake chinali choti apereke nsembe yophimba machimo+ kuti tikhalenso ogwirizana ndi Mulungu.+
18 Popeza kuti iye mwini anavutika pamene anali kuyesedwa,+ amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.+