Aheberi 7:1-28

7  Melekizedeki ameneyu, mfumu ya mzinda wa Salemu, analinso wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba.+ Iyeyu ndi amene anachingamira Abulahamu pochokera kokagonjetsa mafumu, ndipo anamudalitsa.+  Abulahamu anapereka chakhumi cha zinthu zonse kwa iyeyu.+ Tikamasulira dzina lakeli, iye choyamba ndi “Mfumu Yachilungamo,” kenako, mfumu ya Salemu,+ kutanthauza kuti, “Mfumu Yamtendere.”  Popeza kuti analibe bambo, analibe mayi, analibe mzere wa mibadwo ya makolo ndipo tsiku limene anabadwa+ komanso limene anamwalira silikudziwika, koma anamuchititsa kuti afanane ndi Mwana wa Mulungu,+ iye ndi wansembe kwamuyaya.+  Choncho mungaone kuti munthuyu anali wofunika kwambiri. Moti ngakhale kholo lathu Abulahamu, linapereka kwa iye chakhumi pa zinthu zabwino kwambiri zimene anafunkha.+  Zoonadi, amuna ochokera mwa ana aamuna a Levi,+ amene amalandira udindo wa unsembe, amalamulidwa kulandira zakhumi+ kuchokera kwa anthu+ malinga ndi Chilamulo. Izi zikutanthauza kuti, amalandira zakhumizo kuchokera kwa abale awo, ngakhale kuti abale awowo anachokera m’chiuno mwa Abulahamu.+  Koma munthu amene sanachokere mumzere wobadwira+ wa Levi analandira chakhumi kwa Abulahamu,+ ndipo anadalitsa munthu amene anali ndi malonjezo.+  Tsopano, palibe angatsutse kuti wamng’ono amadalitsidwa ndi wamkulu.+  Alevi anali kulandira zakhumi ndipo ndi anthu oti amafa. Koma munthu wina amene analandira zakhumi,+ Malemba amamuchitira umboni kuti ali moyo.+  Ndiponso, mwina ndifotokoze kuti, kudzera mwa Abulahamu, ngakhale Levi amene amalandira zakhumi, anapereka zakhumi. 10  Izi zinachitika m’njira yakuti iye anali adakali m’chiuno+ mwa kholo lake pamene Melekizedeki anakumana ndi kholo lakelo.+ 11  Ndiyeno, ngati zikanakhala zothekadi kuti munthu akhale wangwiro+ kudzera mu unsembe wa Alevi,+ kodi pakanafunikanso kuti pakhale wansembe wina+ monga mwa unsembe wa Melekizedeki+ osati monga mwa unsembe wa Aroni? (Unsembe wa Alevi unali mbali ya Chilamulo pamene chinaperekedwa kwa anthu.)+ 12  Tsopano popeza kuti unsembewo ukusinthidwa,+ ndiye kuti chilamulonso chifunika kusintha.+ 13  Pakuti munthu amene akufotokozedwa ndi zinthu zimene zatchulidwazi ndi wa fuko lina,+ ndipo palibe aliyense wa fuko limenelo amene anatumikirapo paguwa lansembe.+ 14  Tonse tikudziwa kuti Ambuye wathu anatuluka m’fuko la Yuda,+ ndipo ponena za fuko limeneli Mose sanatchulepo chilichonse chokhudza ansembe. 15  Ndipo kwa ife n’zoonekeratu kwambiri kuti pakhalanso wansembe wina+ wofanana ndi Melekizedeki.+ 16  Iyeyu wakhala wotero, osati malinga ndi zofunika za chilamulo, chimene chimadalira zinthu za padziko lapansi,+ koma malinga ndi mphamvu imene imapatsa moyo wosakhoza kuwonongeka.+ 17  Pakuti Malemba amachitira umboni kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”+ 18  Ndithudi, ndiye kuti malamulo oyambawo akuchotsedwa chifukwa chakuti ndi ofooka+ ndiponso operewera.+ 19  Pakuti Chilamulo sichinapangitse chilichonse kukhala changwiro,+ koma chiyembekezo+ chabwino kwambiri chimene anabweretsa kuwonjezera pa Chilamulocho, chinachita zimenezo. Ife tikuyandikira kwa Mulungu chifukwa cha chiyembekezo chimenecho.+ 20  Komanso zimenezi sizinachitike popanda lumbiro. 21  (Pakuti pali amuna ena amene akhala ansembe popanda lumbiro, koma pali mmodzi amene wakhala wansembe mwa lumbiro. Lumbiro limeneli ndi la Iye amene ananena za wansembeyo kuti: “Yehova walumbira+ (ndipo sadzasintha maganizo) kuti, ‘Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya.’”)+ 22  Pa chifukwa chimenecho, Yesu wakhala chikole cha pangano labwino koposa.+ 23  Ndiponso, panayenera kukhala ansembe ambiri olowana m’malo+ chifukwa imfa+ inali kuwaletsa kupitiriza unsembe wawo. 24  Koma iye chifukwa chokhala ndi moyo kosatha,+ palibe omulowa m’malo pa unsembe wake. 25  Ndiye chifukwa chake iye akhoza kupulumutsa kwathunthu anthu amene akufika kwa Mulungu kudzera mwa iye, chifukwa adzakhalabe ndi moyo nthawi zonse ndipo aziwachonderera kwa Mulungu.+ 26  Pakuti mkulu wa ansembe ngati ameneyu ndiyedi wotiyenerera.+ Iye ndi wokhulupirika,+ wosalakwa,+ wosaipitsidwa,+ wosiyana ndi anthu ochimwa,+ ndipo wakwera pamwamba kwambiri kuposa kumwamba.+ 27  Iye safunikira kupereka tsiku ndi tsiku+ nsembe za machimo ake choyamba,+ kenako za anthu ena, monga mmene amachitira akulu a ansembe.+ (Iye anachita zimenezi kamodzi+ kokha pamene anadzipereka yekha nsembe.+ Nsembe imene anapereka motereyi ithandiza anthu mpaka muyaya.) 28  Chilamulo chimaika amuna okhala ndi zofooka+ kukhala akulu a ansembe.+ Koma mawu a lumbiro+ amene ananenedwa pambuyo pa Chilamulo anaika Mwana, amene anakhala wangwiro+ kosatha.

Mawu a M'munsi