Aheberi 8:1-13
8 Ndiye kunena za zinthu zimene tikukambiranazi, mfundo yaikulu ndi iyi: Tili ndi mkulu wa ansembe+ ngati ameneyu, ndipo iye wakhala pansi kumwamba, kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Wolemekezeka.+
2 Iye ndi wantchito wotumikira ena wa m’malo oyerawo+ komanso m’chihema chenicheni, chomangidwa ndi Yehova,+ osati munthu.+
3 Pakuti mkulu wa ansembe aliyense amaikidwa kuti azipereka zonse ziwiri, mphatso ndi nsembe.+ Ndiye chifukwa chake kunali kofunika kuti uyunso akhale ndi chinachake chopereka.+
4 Choncho, iye akanakhalabe padziko lapansi, sakanakhala wansembe,+ popeza amuna opereka mphatsozo malinga ndi Chilamulo, alipo kale.
5 Koma amuna amenewo akuchita utumiki wopatulikawo m’chifaniziro+ ndi mu mthunzi+ wa zinthu zakumwamba. Izi zinaonekera mu lamulo limene Mulungu anapatsa Mose, atatsala pang’ono kumanga chihema.+ Lamulo lake linali lakuti:+ “Uonetsetse kuti wapanga zinthu zonse motsatira chitsanzo chimene wasonyezedwa m’phiri.”+
6 Koma tsopano Yesu walandira ntchito yapamwamba kwambiri yotumikira ena, moti wakhalanso mkhalapakati+ wa pangano labwino kwambiri,+ limene lakhazikitsidwa mwalamulo pa malonjezo abwinonso.+
7 Pangano loyamba lija likanakhala lopanda zolakwika, sipakanafunikanso pangano lachiwiri.+
8 Pakuti iye akuimba anthu mlandu pamene akunena kuti: “‘Taonani! Masiku adzafika, pamene ndidzachita pangano latsopano ndi nyumba ya Isiraeli komanso ndi nyumba ya Yuda,’ watero Yehova.+
9 ‘Koma pangano+ limeneli si lofanana ndi limene ndinapangana ndi makolo awo pamene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse m’dziko la Iguputo,+ chifukwa iwo sanapitirize kusunga pangano+ langalo moti ndinasiya kuwasamalira,’ watero Yehova.”+
10 “‘Pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Isiraeli pambuyo pa pangano loyamba lija ndi ili: Ndidzaika malamulo anga m’maganizo mwawo ndi kuwalemba m’mitima yawo.+ Ine ndidzakhala Mulungu wawo+ ndipo iwo adzakhala anthu anga,’+ watero Yehova.
11 “‘Munthu sadzaphunzitsa nzika inzake kapena m’bale wake kuti: “Um’dziwe Yehova!”+ Pakuti aliyense wa iwo adzandidziwa,+ kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu.
12 Ine ndidzawachitira chifundo pa zochita zawo zosalungama, ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.’”+
13 Ponena kuti “pangano latsopano,” iye wapanga loyambalo kukhala lotha ntchito.+ Tsopano pangano limene latha ntchito ndipo likukalamba, latsala pang’ono kufafanizika.+