Aheberi 9:1-28

9  Tsopano, pangano loyamba lija linali ndi malamulo ake a utumiki wopatulika+ ndiponso malo ake oyera a padziko lapansi.+  Pakuti panamangidwa chipinda choyamba cha chihema.+ M’chipindamo munali choikapo nyale,+ tebulo,+ ndi mitanda ya mkate woonetsedwa,+ ndipo chinali kutchedwa “Malo Oyera.”+  Koma kuseri kwa nsalu yotchinga yachiwiri+ kunali chipinda chinanso chotchedwa “Malo Oyera Koposa.”+  Mmenemu munali chiwaya chagolide chofukizira nsembe,+ ndi likasa la pangano.+ Likasa lonseli linali lokutidwa ndi golide.+ M’likasamo munali mtsuko wagolide wokhala ndi mana.+ Munalinso ndodo ya Aroni imene inaphuka ija,+ komanso miyala yosema+ ya pangano.  Koma pamwamba pa likasalo panali akerubi aulemerero+ amene zithunzithunzi zawo zinali kugwera pachivundikiro chophimba machimo.+ Koma ino si nthawi yofotokoza zinthu zimenezi mwatsatanetsatane.  Zinthu zimenezi zitakonzedwa mwa njira imeneyi, ansembe anali kulowa m’chipinda choyamba+ nthawi zonse kukachita mautumiki opatulika.+  Koma m’chipinda chachiwiricho, mkulu wa ansembe yekha ndiye anali kulowamo kamodzi pa chaka,+ ndipo sanali kulowamo popanda kutenga magazi.+ Magaziwo anali kuwapereka chifukwa cha iye mwini,+ komanso chifukwa cha machimo a anthu amene anachita mosadziwa.+  Chotero mzimu woyera ukuonetsa poyera kuti njira+ yolowera kumalo oyera amkatikati inali isanaonekere pamene chihema choyambacho chinalipo.+  Chihema chimenecho chinali chifaniziro+ cha nthawi yoikidwiratu imene tsopano yafika,+ ndipo mogwirizana ndi chifanizirocho, zonse ziwiri, mphatso ndi nsembe zimaperekedwa.+ Komabe, zimenezi sizipangitsa munthu amene akuchita utumiki wopatulikayo kukhala wangwiro+ m’chikumbumtima chake.+ 10  M’malomwake, zimangokhudza zakudya,+ zakumwa,+ ndi miyambo yosiyanasiyana yoviika zinthu m’madzi.+ Zimenezo zinali zofunika za Chilamulo zokhudza zinthu zathupi,+ ndipo zinakhazikitsidwa kufikira nthawi yoikidwiratu yokonzanso zinthu.+ 11  Komabe, pamene Khristu anabwera monga mkulu wa ansembe,+ wa zinthu zabwino zimene zakwaniritsidwa, anatero kudzera m’chihema chachikulu ndi changwiro kwambiri chimene sichinapangidwe ndi manja a anthu, kutanthauza kuti, sichili mbali ya chilengedwe chapansi pano.+ 12  Choncho iye analowa m’malo oyera amkatikati ndi magazi+ ake, osati ndi magazi a mbuzi kapena a ng’ombe zazing’ono zamphongo. Analowa kamodzi kokha m’malo oyera amkatikatiwo, ndipo anatilanditsa kwamuyaya.+ 13  Pakuti ngati magazi a mbuzi+ ndi a ng’ombe zamphongo+ komanso phulusa+ la ng’ombe yaikazi imene sinaberekepo, zimene amawaza nazo anthu oipitsidwa,+ zimawayeretsa mpaka kukhaladi oyera pamaso pa Mulungu,+ 14  kuli bwanji magazi+ a Khristu, amene anadzipereka wopanda chilema kwa Mulungu kudzera mwa mzimu wamuyaya?+ Kodi magazi amenewo sadzayeretsa+ zikumbumtima zathu ku ntchito zakufa,+ kuti tichite utumiki wopatulika+ kwa Mulungu wamoyo? 15  Chotero, ndiye chifukwa chake iye ali mkhalapakati+ wa pangano latsopano kuti anthu amene aitanidwa alandire lonjezo la cholowa chamuyaya.+ Izi zatheka chifukwa cha imfa yake, imene inali ngati dipo+ lawo lowamasula ku machimo amene iwo anali nawo m’pangano lakale lija.+ 16  Pakuti pamene pali pangano,+ m’poyeneranso kuti munthu wochita naye panganoyo afe. 17  Pakuti pangano limagwira ntchito ngati wina wafapo, popeza siligwira ntchito nthawi iliyonse pamene munthu wochita naye panganoyo ali ndi moyo. 18  Ndiye chifukwa chake ngakhale pangano loyamba+ lija silinakhazikitsidwe popanda magazi.+ 19  Pakuti pamene Mose anatchulira anthu onsewo lamulo lililonse malinga ndi Chilamulo,+ anatenga magazi a ng’ombe zazing’ono zamphongo ndi magazi a mbuzi, pamodzi ndi madzi, ubweya wa nkhosa wofiira kwambiri, ndi timitengo ta hisope,+ n’kuwaza bukulo ndi anthu onse. 20  Iye anati: “Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulani kuti mulisunge.”+ 21  Ndipo anawazanso magazi aja pachihema+ ndi paziwiya zonse zogwiritsa ntchito potumikira ena.+ 22  Inde, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi+ malinga ndi Chilamulo, ndipo popanda kukhetsa magazi+ anthu sangakhululukidwe machimo awo.+ 23  Chotero kunali kofunikira kuti zifaniziro+ za zinthu zakumwamba ziyeretsedwe m’njira imeneyi,+ koma zinthu zakumwamba zenizenizo ziyeretsedwe ndi nsembe zabwino kuposa nsembe zoterezi. 24  Pakuti Khristu sanalowe m’malo oyera amkatikati opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Tsopano ali kumwamba kuti aonekere pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.+ 25  Iye sanapite kumwambako kuti azikadzipereka nsembe mobwerezabwereza, monga mmene mkulu wa ansembe amachitira. Mkulu wa ansembe amalowa m’malo oyera amkatikati+ chaka ndi chaka+ atatenga magazi a nyama osati ake. 26  Zikanatero, akanavutika mobwerezabwereza kuyambira pamene dziko linakhazikitsidwa.+ Koma tsopano iye waonekera+ kamodzi+ kokha pa mapeto a nthawi* zino+ kuti achotse uchimo kudzera mu nsembe yake.+ 27  Monga mmene zilili ndi anthu kuti amayembekezera+ kufa kamodzi kokha, kenako n’kudzalandira chiweruzo,+ 28  n’chimodzimodzinso Khristu. Iye anaperekedwa nsembe kamodzi+ kokha kuti anyamule machimo a anthu ambiri.+ Ndipo nthawi yachiwiri+ imene adzaonekere+ sadzaonekera n’cholinga chochotsa uchimo.+ Anthu amene akumuyembekezera ndi mtima wonse kuti awapulumutse ndi amene adzamuone.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.