Akolose 2:1-23
2 Ndikufuna kuti mudziwe nkhondo+ yaikulu imene ndikumenya chifukwa cha inuyo ndi anthu a ku Laodikaya,+ ndi onse amene sanandionepo maso ndi maso.
2 Ndikufuna kuti mtima wa aliyense ulimbikitsidwe,+ ndiponso kuti onse akhale ogwirizana m’chikondi.+ Achite zimenezi kuti onse alandire chuma chimene chimabwera chifukwa chomvetsa bwino zinthu,+ popanda kukayikira chilichonse, ndiponso chifukwa chodziwa molondola chinsinsi chopatulika cha Mulungu, chomwe ndi Khristu.+
3 Chuma chonse chokhudzana ndi nzeru ndiponso kudziwa zinthu+ chinabisidwa mosamala mwa iye.
4 Ndikunena zimenezi kuti munthu aliyense asakunyengeni ndi mfundo zokopa.+
5 Popeza ngakhale kuti sindili kumeneko, ndili nanu ndithu mumzimu.+ Ndine wosangalala poona kuti mumachita zinthu mwadongosolo,+ komanso kuti muli ndi chikhulupiriro+ cholimba mwa Khristu.
6 Tsopano popeza mwalandira Khristu Yesu Ambuye wathu, yendanibe mogwirizana+ naye.
7 Khalanibe ozikika mozama+ mwa iye, ndipo monga mmene munaphunzitsidwira, pitirizani kukula+ pamene mukumuona iye monga maziko anu, ndi kukhazikika m’chikhulupiriro.+ Sefukiranibe ndi chikhulupiriro popereka mapemphero oyamikira.+
8 Samalani: mwina wina angakugwireni+ ngati nyama, mwa nzeru za anthu+ ndi chinyengo chopanda pake,+ malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli,+ osati malinga ndi Khristu,
9 chifukwa iye ndi wodzaza bwino kwambiri+ ndi makhalidwe+ a Mulungu.+
10 Kudzera mwa iyeyo, inu simukusowa kalikonse. Iye ndiye mwini ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse.+
11 Popeza muli naye pa ubwenzi,+ mwadulidwa,+ osati ndi manja a anthu koma mwa kuvula thupi lauchimo,+ chifukwa mdulidwe wa atumiki a Khristu umakhala wotero.
12 Zinatero popeza munakwiriridwa naye limodzi mwa kubatizidwa ubatizo wofanana ndi wake,+ ndipo chifukwa choti muli naye pa ubwenzi, munaukitsidwa+ naye limodzi kudzera m’chikhulupiriro chimene muli nacho+ mu zinthu zimene zinachitika chifukwa cha mphamvu+ ya Mulungu, amene anamuukitsa kwa akufa.+
13 Ndiponso, ngakhale kuti munali akufa m’machimo anu ndipo munali osadulidwa, Mulungu anakupatsani moyo kuti mukhale ogwirizana ndi Khristu,+ ndipo anatikhululukira machimo athu onse motikomera mtima.+
14 Anafafanizanso+ chikalata cholembedwa ndi manja,+ chokhala ndi malamulo+ operekedwa monga malangizo, chimene chinali kutitsutsa.+ Ndipo Iye wachichotsa mwa kuchikhomera+ pamtengo wozunzikirapo.*+
15 Pogwiritsa ntchito mtengo wozunzikirapowo, iye anavula maboma ndi olamulira n’kuwasiya osavala,+ ndipo anawaonetsa poyera pamaso pa anthu onse kuti aliyense aone kuti wawagonjetsa,+ n’kumayenda nawo ngati akaidi.+
16 Choncho munthu asakuweruzeni+ pa nkhani ya kudya ndi kumwa+ kapena chikondwerero chinachake,+ kapenanso kusunga tsiku lokhala mwezi,+ ngakhalenso kusunga sabata,+
17 pakuti zinthu zimenezo ndi mthunzi+ wa zimene zinali kubwera, koma zenizeni+ zake zili mwa Khristu.+
18 Musalole kuti munthu aliyense amene amasangalala ndi kudzichepetsa kwachinyengo komanso ndi kulambira angelo akumanitseni+ mphotoyo.+ Anthu oterowo amaumirira zinthu zimene aona ndipo maganizo awo ochimwa amawachititsa kudzitukumula popanda chifukwa chomveka.
19 Amatero koma osagwira mwamphamvu amene ali mutu,+ amene kuchokera kwa iye, thupi lonselo, limene limapeza zonse zimene limafunikira ndipo ndi lolumikizika bwino+ mwa mfundo zake ndi minyewa, limakulabe mothandizidwa ndi Mulungu.+
20 Ngati munafa+ limodzi ndi Khristu pa mfundo zimene ndi maziko+ a moyo wa m’dzikoli,+ n’chifukwa chiyani mukupitiriza kukhala ngati kuti mudakali mbali ya dzikoli, pogonjeranso malamulo+ akuti:
21 “Usatenge ichi, kapena usalawe ichi,+ kapena usakhudze ichi?”+
22 Zinthu zimenezi zidzawonongedwa mwa kuzigwiritsa ntchito ndipo malamulo amenewa ndi ziphunzitso za anthu basi.+
23 Ndithudi, zinthu zimenezo zimaonekera pa kulambira kochita kudzipangira, podzichepetsa mwachinyengo komanso pozunza thupi,+ ndipo zimaonekadi ngati zanzeru, koma n’zosathandiza kwa munthu polimbana ndi zilakolako za thupi.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 9.