Amosi 3:1-15

3  “Tamverani mawu amene Yehova wanena okhudza inu+ ana Aisiraeli, mawu okhudza banja lonse limene ndinalitulutsa m’dziko la Iguputo.+ Mawuwo ndi akuti,  ‘Pa mabanja onse apadziko lapansi+ ine ndimadziwa inu nokha.+ Choncho ndidzakulangani chifukwa cha zolakwa zanu zonse.+  “‘Kodi anthu awiri amayenda pamodzi asanapangane ndi kukumana mogwirizana ndi pangano lawolo?+  Kodi mkango umabangula m’nkhalango usanagwire nyama?+ Kodi mkango wamphamvu umalira m’malo ake obisalamo usanagwire kalikonse?  Kodi mbalame imakodwa mumsampha pansi, pamene palibe msampha?+ Kodi msampha umafwamphuka kuchokera pansi usanagwire kalikonse?  Lipenga la nyanga ya nkhosa likalira mumzinda, kodi anthu sanjenjemera?+ Kodi tsoka likagwa mumzinda si Yehova amene wachititsa?  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, sangachite kalikonse asanaulule chinsinsi chake kwa atumiki ake, aneneri.+  Mkango wabangula!+ Ndani sachita mantha? Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa walankhula! Ndani sanenera?’+  “‘Lengezani izi pansanja zokhalamo za ku Asidodi ndi pansanja zokhalamo za m’dziko la Iguputo.+ Munene kuti: “Sonkhanani pamodzi kuti muukire mapiri a Samariya+ ndipo onani zinthu zambiri zachisokonezo ndi zachinyengo zimene zikuchitika mumzinda umenewo.+ 10  Anthuwo sadziwa kuchita zolungama,+ ndipo asonkhanitsa munsanja zawo zokhalamo zinthu zimene anafunkha mwachiwawa,”+ watero Yehova.’ 11  “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali mdani amene wazungulira dziko lonse+ ndipo ameneyo adzakukhalitsa wopanda mphamvu ndipo adzafunkha nsanja zako zokhalamo.’+ 12  “Yehova wanena kuti, ‘Monga mmene m’busa amapulumutsira ziboda ziwiri za chiweto ndi kachidutswa ka khutu m’kamwa mwa mkango,+ nawonso ana a Isiraeli amene akukhala m’Samariya pamipando yapamwamba+ ndi kugona pamabedi a ku Damasiko+ adzapulumuka ochepa chabe m’manja mwa adani awo.’ 13  “‘Tamverani ndipo muchitire umboni,+ inu a nyumba ya Yakobo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, Mulungu wa makamu. 14  ‘Pa tsiku limene ndidzalanga Isiraeli+ chifukwa cha kupanduka kwake, ndidzaperekanso chiweruzo pamaguwa ansembe a ku Beteli+ ndipo nyanga za guwa lansembe zidzazulidwa ndi kugwa pansi.+ 15  Nyumba yokhalamo m’nyengo yozizira+ ndi nyumba yokhalamo m’nyengo yotentha+ ndidzazigwetsa.’ “‘Nyumba zaminyanga ya njovu zidzafafanizidwa+ ndipo nyumba zambiri zidzawonongedwa,’+ watero Yehova.”

Mawu a M'munsi