Danieli 10:1-21
10 M’chaka chachitatu cha ulamuliro wa Koresi+ mfumu ya Perisiya, panali nkhani imene Danieli anauzidwa. Danieli ameneyu anali kutchedwa Belitesazara.+ Nkhani imene anauzidwayo inali yoona ndipo inali yokhudza nkhondo yaikulu.+ Danieli anamvetsa nkhani imeneyi ndiponso zinthu zimene anaona.+
2 Masiku amenewo, ineyo Danieli, ndinali kulira+ kwa milungu itatu yathunthu.
3 Sindinadye chakudya chokoma, sindinadye nyama kapena kumwa vinyo ndipo sindinadzole mafuta kufikira milungu itatu yonseyo itatha.+
4 Ndipo pa tsiku la 24 la mwezi woyamba, pamene ndinali m’mbali mwa mtsinje waukulu, mtsinje wa Hidekeli,+
5 ndinakweza maso anga ndipo ndinaona munthu atavala nsalu,+ atamanganso mchiuno mwake+ ndi lamba wa golide wabwino wa ku Ufazi.+
6 Thupi lake linali ngati mwala wa kulusolito,+ nkhope yake inali yowala ngati mphezi,+ maso ake anali kuoneka ngati miyuni yamoto,+ manja ake ndi mapazi ake zinali kuoneka ngati mkuwa wonyezimira,+ ndipo mawu ake anali kumveka ngati khamu la anthu.
7 Ineyo Danieli, ndinaona ndekha munthuyo koma amuna amene ndinali nawo sanamuone.+ M’malomwake iwo anayamba kunjenjemera kwambiri moti anathawa n’kukabisala.
8 Choncho ndinatsala ndekha ndipo ndinaona masomphenya odabwitsawa. Pamenepo mphamvu zonse zinandithera, ndipo maonekedwe olemekezeka a nkhope yanga anasintha kwambiri n’kukhala omvetsa chisoni, moti ndinalibenso mphamvu.+
9 Ndiyeno ndinayamba kumva mawu ake. Pamene ndinali kumva mawuwo ndinagona pansi+ chafufumimba n’kugona tulo tofa nato.+
10 Pamenepo ndinamva dzanja la munthu likundikhudza,+ ndipo linayamba kundigwedeza pang’onopang’ono n’kundidzutsa. Nditadzuka ndinagwada ndi kugwira pansi ndi manja anga.
11 Iye anandiuza kuti:
“Iwe Danieli, munthu wokondedwa kwambiri,+ mvetsetsa zinthu zimene ndikukuuza+ ndipo uimirire chifukwa ndatumidwa kwa iwe.”
Atandiuza zimenezi ndinaimiriradi koma ndikunjenjemera.
12 Pamenepo iye anandiuza kuti: “Iwe Danieli, usaope,+ pakuti kuyambira tsiku loyamba pamene unatsegula mtima wako kuti umvetse tanthauzo la zinthu zimenezi,+ ndiponso pamene unadzichepetsa pamaso pa Mulungu wako,+ mawu ako akhala akumveka ndipo ine ndabwera chifukwa cha mawu akowo.+
13 Koma kalonga+ wa ufumu wa Perisiya+ ananditsekereza+ kwa masiku 21, ndipo Mikayeli,+ mmodzi mwa akalonga aakulu+ anabwera kudzandithandiza, ndipo pa nthawi imeneyo ndinakhalabe pafupi ndi mafumu a Perisiya.+
14 Tsopano ndabwera kudzakuthandiza kuzindikira zimene zidzagwera anthu a mtundu wako+ m’masiku otsiriza,+ chifukwa masomphenyawa+ ndi okhudza masiku am’tsogolo.”+
15 Pamene anali kulankhula nane mawu amenewa, ine ndinali nditagona chafufumimba,+ osatha kulankhula kalikonse.
16 Ndiyeno winawake wamaonekedwe ofanana ndi ana a anthu anakhudza milomo yanga.+ Atatero, ndinayamba kulankhula,+ ndipo ndinauza amene anali ataimirira patsogolo panga uja kuti: “Mbuyanga,+ ine ndinayamba kunjenjemera chifukwa cha zimene ndaona ndipo mphamvu zandithera.+
17 Choncho ine mtumiki wanu ndingathe bwanji kulankhula nanu mbuyanga?+ Mpaka pano ndilibe mphamvu, ndipo sindikuthanso kupuma.”+
18 Ndiyeno wamaonekedwe ofanana ndi munthu wochokera kufumbi uja anandikhudza ndi kundilimbikitsa.+
19 Iye anandiuza kuti: “Iwe munthu wokondedwa kwambiri,+ usachite mantha.+ Mtendere ukhale nawe.+ Limba mtima, ndithu, limba mtima.”+ Atangolankhula nane, ndinadzilimbitsa ndipo pamapeto pake ndinati: “Lankhulani mbuyanga+ chifukwa inu mwandilimbikitsa.”+
20 Choncho iye anandiuza kuti:
“Kodi ukudziwadi kuti n’chifukwa chiyani ndabwera kwa iwe? Tsopano ndibwerera kuti ndikamenyane ndi kalonga wa Perisiya.+ Pamene ndikupita, nayenso kalonga wa Girisi akubwera.+
21 Koma ndikuuza zinthu zolembedwa m’buku la choonadi,+ ndipo palibe amene akundithandiza kwambiri pa zinthu zimenezi kupatulapo Mikayeli,+ kalonga wa anthu inu.+