Danieli 3:1-30

3  Nebukadinezara anapanga fano lagolide.+ Fanoli linali lalitali mikono* 60 ndipo m’lifupi mwake linali mikono 6. Analiimika m’chigwa cha Dura, m’chigawo cha Babulo.+  Nebukadinezara monga mfumu anatumiza uthenga kwa masatarapi,* akuluakulu a boma,*+ abwanamkubwa, alangizi, asungichuma, oweruza, akuluakulu apolisi+ ndi oyang’anira onse a zigawo kuti asonkhane ku mwambo wotsegulira+ fano limene mfumu Nebukadinezara inaimika.  Pa nthawi imeneyo masatarapi,+ akuluakulu a boma, abwanamkubwa, alangizi, asungichuma, oweruza, akuluakulu apolisi ndi oyang’anira onse a zigawo, anasonkhana ku mwambo wotsegulira fano limene mfumu Nebukadinezara inaimika. Iwo anaimirira patsogolo pa fano limene Nebukadinezara anaimikalo.  Tsopano wolengeza mauthenga+ anayamba kufuula kuti: “Tamverani inu anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana.+  Mukangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamng’ono, zoimbira zosiyanasiyana za zingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira,+ mugwade ndi kuwerama mpaka nkhope zanu pansi ndi kulambira fano lagolide limene mfumu Nebukadinezara yaimika.  Aliyense amene sagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi ndi kulambira fanolo,+ nthawi yomweyo+ aponyedwa m’ng’anjo yoyaka moto.”+  Chifukwa cha mawu amenewa, patangomveka kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamng’ono, zoimbira zosiyanasiyana za zingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira, anthu onse a mitundu yosiyanasiyana,+ olankhula zinenero zosiyanasiyana, anagwada mpaka nkhope zawo pansi ndi kulambira fano lagolide limene mfumu Nebukadinezara inaimika.  Nthawi yomweyo, Akasidi* ena anapita kwa mfumu kukaneneza Ayuda.+  Iwo anauza mfumu Nebukadinezara kuti: “Inu mfumu, mukhale ndi moyo mpaka kalekale.+ 10  Inuyo mfumu munaika lamulo lakuti munthu aliyense akamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamng’ono, zoimbira zosiyanasiyana za zingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira,+ agwade ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi ndipo alambire fano lagolide. 11  Munalamulanso kuti aliyense amene sagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi n’kulambira fanolo aponyedwe m’ng’anjo yoyaka moto.+ 12  Koma pali Ayuda ena amene munawaika kukhala oyang’anira chigawo cha Babulo.+ Amuna amphamvu amenewa, Sadirake, Mesake ndi Abedinego, sakukumverani inu mfumu. Iwo sakutumikira milungu yanu ndipo sakulambira fano lagolide limene mwaimika.”+ 13  Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima kwambiri+ ndipo analamula kuti abweretse Sadirake, Mesake ndi Abedinego.+ Choncho anabweretsadi amuna amphamvu amenewa pamaso pa mfumu. 14  Ndiyeno Nebukadinezara anawafunsa kuti: “Kodi ndi zoonadi kuti inu Sadirake, Mesake ndi Abedinego simukutumikira milungu yanga+ ndi kulambira fano lagolide limene ndaimika?+ 15  Tsopano ngati mwakonzeka kuti mukamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamng’ono, zoimbira zosiyanasiyana za zingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira,+ mugwada n’kuwerama mpaka nkhope zanu pansi ndi kulambira fano lagolide, zili bwino. Koma ngati simulilambira, nthawi yomweyo muponyedwa m’ng’anjo yoyaka moto. Ndipo ndi mulungu uti amene angakupulumutseni m’manja mwanga?”+ 16  Pamenepo Sadirake, Mesake ndi Abedinego anayankha mfumuyo kuti: “Inu mfumu Nebukadinezara, palibenso chimene ife tinganene kwa inu pa nkhani imeneyi.+ 17  Ngati mungatiponyere m’ng’anjo yoyaka moto, Mulungu wathu amene tikumutumikira akhoza kutipulumutsa. Iye atipulumutsa m’ng’anjo yoyaka moto ndiponso m’manja mwanu mfumu.+ 18  Koma ngati satipulumutsa, dziwani mfumu kuti ife sititumikira milungu yanu, ndipo sitilambira fano limene mwaimika.”+ 19  Pamenepo Nebukadinezara anapsera mtima Sadirake, Mesake ndi Abedinego ndipo nkhope yake inasintha. Iye analamula kuti ng’anjoyo aisonkhezere kuwirikiza ka 7 kuposa mmene anali kuchitira nthawi zonse. 20  Iye anauza asilikali ake ena amphamvu+ kuti amange Sadirake, Mesake ndi Abedinego ndi kuwaponya m’ng’anjo yoyaka motoyo.+ 21  Chotero amuna amphamvuwa anamangidwa atavala nsalu zawo zakunja, zovala zawo, zisoti zawo ndi zovala zawo zina zonse ndipo anawaponya m’ng’anjo yoyaka motoyo. 22  Koma chifukwa chakuti mfumu inalamula zimenezi itapsa mtima kwambiri ndipo ng’anjo ya moto anaisonkhezera mopitirira muyezo, asilikali amphamvu amene anatenga Sadirake, Mesake ndi Abedinego aja ndi amene anaphedwa ndi malawi a moto. 23  Ndipo amuna ena amphamvuwa, Sadirake, Mesake ndi Abedinego, anagwera pakatikati pa ng’anjo yoyaka moto.+ 24  Pamenepo, mfumu Nebukadinezara anachita mantha kwambiri ndipo ananyamuka mwachangu. Iye anauza nduna zake zapamwamba kuti: “Kodi sitinaponye amuna atatu amphamvu pakati pa moto titawamanga?”+ Ndunazo zinamuyankha kuti: “Inde, mfumu.” 25  Ndiyeno mfumu inati: “Taonani! Inetu ndikuona amuna amphamvu anayi akuyendayenda pakati pa moto osapsa, ndipo munthu wachinayiyo akuoneka ngati mulungu.”+ 26  Kenako Nebukadinezara anayandikira khomo la ng’anjo yoyaka motoyo+ ndipo anati: “Sadirake, Mesake ndi Abedinego, inu atumiki a Mulungu Wam’mwambamwamba,+ tulukani ndipo mubwere kuno!” Zitatero, Sadirake, Mesake ndi Abedinego anatuluka pakati pa motopo. 27  Tsopano masatarapi, akuluakulu a boma, abwanamkubwa, ndi nduna zapamwamba+ za mfumu zimene zinasonkhana zinaonadi kuti motowo sunavulaze amuna amphamvu amenewa,+ ndipo tsitsi lawo silinawauke ndi limodzi lomwe.+ Zovala zawo sizinasinthe ndipo sanali kumveka ngakhale fungo la moto. 28  Pamenepo Nebukadinezara anati: “Atamandike Mulungu wa Sadirake, Mesake ndi Abedinego+ amene anatumiza mngelo wake+ ndi kupulumutsa atumiki ake amene anamudalira+ ndiponso amene sanamvere mawu a mfumu, koma anali okonzeka kufa chifukwa sanafune kutumikira+ ndi kulambira+ mulungu wina aliyense kupatulapo Mulungu wawo.+ 29  Tsopano ine ndikuika lamulo+ lakuti, anthu onse a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana amene anganene chilichonse chotsutsana ndi Mulungu wa Sadirake, Mesake ndi Abedinego ayenera kudulidwa nthulinthuli,+ ndipo nyumba zawo zisandutsidwe zimbudzi za anthu onse,+ pakuti palibe mulungu wina amene amatha kupulumutsa chotere.”+ 30  Pamenepo mfumu inachititsa kuti Sadirake, Mesake ndi Abedinego zinthu ziziwayendera bwino m’chigawo cha Babulo.+

Mawu a M'munsi

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Onani mawu a m’munsi pa Eza 8:36.
Onani mawu a m’munsi pa Da 2:48.
Onani mawu a m’munsi pa Da 2:2.