Danieli 8:1-27

8  M’chaka chachitatu cha ulamuliro wa mfumu Belisazara,+ ineyo Danieli ndinaona masomphenya pambuyo pa masomphenya amene ndinaona poyambirira aja.+  Nditayamba kuona masomphenyawo ndinapezeka kuti ndili kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani,+ imene ili m’chigawo cha Elamu.+ M’masomphenyawo ndinapezeka kuti ndili m’mphepete mwa mtsinje wa Ulai.+  Nditakweza maso anga ndinaona nkhosa yamphongo+ itaimirira pafupi ndi mtsinjewo ndipo inali ndi nyanga ziwiri. Nyanga ziwirizi zinali zazitali koma imodzi, imene inamera pomalizira, inali yaitali kuposa inzake.+  Ndinaona nkhosa yamphongoyo ikugunda kumadzulo, kumpoto ndi kum’mwera ndipo palibe zilombo zakutchire zimene zinaima pamaso pake komanso palibe amene anali kupulumutsa aliyense ku mphamvu zake.+ Nkhosa yamphongoyo inali kuchita zofuna zake ndipo inali kudzitama kwambiri.  Pamene ndinali kuganizira zimenezi, ndinangoona mbuzi yamphongo+ ikuchokera kolowera dzuwa kudutsa padziko lonse lapansi koma sinali kukhudza pansi. Pakati pa maso a mbuziyo panali nyanga yoonekera patali.+  Mbuziyo inali kubwera kumene kunali nkhosa yamphongo yokhala ndi nyanga ziwiri ija, imene ndinaiona itaima pafupi ndi mtsinje, ndipo inali kubwera mwamphamvu kwa nkhosayo, ili ndi mkwiyo waukulu.  Mbuzi yamphongo ija ndinaiona itafika pafupi kwambiri ndi nkhosa yamphongoyo ndipo inayamba kuichitira ukali. Kenako inagunda nkhosa yamphongoyo ndi kuthyola nyanga zake ziwiri, ndipo nkhosa yamphongoyo inalibe mphamvu zotha kulimbana ndi mbuzi yamphongoyo. Choncho mbuziyo inagwetsera pansi nkhosa yamphongoyo ndi kuipondaponda ndipo inalibe woti angaipulumutse ku mphamvu za mbuziyo.+  Mbuzi yamphongoyo inali kudzitama mopitirira muyezo,+ koma itangokhala yamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoledwa. Pamalo pake panamera nyanga zinayi zoonekera patali zoloza kumphepo zinayi zakumwamba.+  Imodzi mwa nyangazi inatulutsa nyanga ina yaing’ono+ imene inayamba kukula kwambiri moloza kum’mwera, moloza kotulukira dzuwa ndiponso moloza ku Dziko Lokongola.+ 10  Inapitiriza kukula mpaka inafika kwa khamu lakumwamba,+ moti inachititsa ena mwa khamuli ndi nyenyezi zina+ kugwera padziko lapansi ndipo inazipondaponda.+ 11  Iyo inadzitama kwambiri mpaka kukafika kwa Kalonga wa khamulo.+ Inalanda Kalongayu nsembe yoyenera kuperekedwa nthawi zonse,+ ndipo malo opatulika amene iye anakhazikitsa anagwetsedwa.+ 12  Chifukwa cha uchimo,+ khamulo ndi nsembe yoyenera kuperekedwa nthawi zonse+ zinaperekedwa kwa nyangayo,+ ndipo inali kugwetsera choonadi+ pansi.+ Nyangayo inali kuchita zofuna zake ndipo inapambana.+ 13  Ndiyeno ndinamva woyera winawake+ akulankhula ndipo woyera wina anafunsa woyera amene anali kulankhulayo kuti: “Kodi masomphenya okhudza nsembe yoyenera kuperekedwa nthawi zonse,+ tchimo lobweretsa chiwonongeko+ ndiponso kupondedwapondedwa kwa malo opatulika ndi kwa khamulo,+ adzakhala a nthawi yaitali bwanji?” 14  Iye anandiuza kuti: “Kufikira nsembe za tsiku ndi tsiku zokwanira 2,300, zamadzulo ndi zam’mawa, zitadutsa. Kenako malo opatulika adzakonzedwanso kuti akhale ngati mmene analili poyamba.”+ 15  Ndiyeno pamene ineyo Danieli ndinali kuona masomphenyawo ndi kuyesa kuwamvetsa,+ ndinaona winawake wooneka ngati mwamuna wamphamvu ataima patsogolo panga.+ 16  Kenako ndinamva mawu a munthu wochokera kufumbi ali pakati pa mtsinje wa Ulai.+ Iye anafuula kuti: “Gabirieli,+ thandiza uyo ali apoyo kuti amvetsetse zimene waona.”+ 17  Chotero iye anabwera pafupi ndi pamene ine ndinaima. Atafika, ndinachita mantha ndipo ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi. Ndiyeno anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu,+ dziwa+ kuti masomphenyawa ndi okhudza nthawi ya mapeto.”+ 18  Pamene anali kulankhula nane ndinagona pansi chafufumimba n’kugona tulo tofa nato.+ Ndiyeno iye anandigwira ndi kundiimiritsa pamalo pomwe ndinaima paja.+ 19  Kenako anandiuza kuti: “Ine ndikudziwitsa zimene zidzachitike kumapeto kwa nthawi yopereka chiweruzo, chifukwa chakuti masomphenyawo adzakwaniritsidwa pa nthawi yoikidwiratu ya mapeto.+ 20  “Nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri imene unaona, ikuimira mfumu ya Mediya ndi mfumu ya Perisiya.+ 21  Mbuzi yamphongo yaubweya wambiri ikuimira mfumu ya Girisi,+ ndipo nyanga yaikulu imene inali pakati pa maso ake ikuimira mfumu yoyamba.+ 22  Popeza nyangayi inathyoka ndipo panamera zina zinayi,+ pali maufumu anayi amene adzauke mu mtundu wake, koma sadzakhala ndi mphamvu ngati zake. 23  “Ku mapeto kwa ufumu wawo, uchimo wawo ukadzafika pachimake, padzauka mfumu ya maonekedwe oopsa ndiponso yomvetsa zinthu zovuta kumva.+ 24  Mfumuyo idzakula mphamvu koma osati mwa iyo yokha.+ Idzawononga zinthu zambiri+ ndipo chilichonse chimene izidzachita chidzaiyendera bwino. Idzawononga anthu amphamvu ndi anthu oyera.+ 25  Chifukwa cha kuzindikira kwake idzathadi kugwiritsa ntchito chinyengo.+ Idzadzitukumula kwambiri mumtima mwake,+ ndipo idzawononga anthu ambiri pa nthawi imene zinthu zikuiyendera bwino.+ Mfumuyo idzalimbana ndi Kalonga wa akalonga,+ ndipo idzathyoledwa koma osati ndi dzanja la munthu.+ 26  “Zinthu zimene waziona ndiponso zimene zanenedwa zokhudza madzulo ndi m’mawa, n’zoona.+ Koma iweyo usunge chinsinsi cha masomphenyawo, chifukwa ndi okhudza masiku am’tsogolo.”+ 27  Ndiyeno ineyo Danieli ndinatopa kwambiri ndipo ndinadwala kwa masiku angapo.+ Kenako ndinadzuka ndi kugwira ntchito yotumikira mfumu.+ Koma ndinali wodabwa kwambiri ndi zimene ndinaona, ndipo palibe amene anazimvetsa.+

Mawu a M'munsi