Danieli 9:1-27

9  M’chaka choyamba cha Dariyo mwana wa Ahasiwero,+ wa mtundu wa Amedi,+ amene anaikidwa kukhala mfumu ya ufumu wa Akasidi,+  m’chaka choyamba cha ulamuliro wake, ineyo Danieli ndinazindikira chiwerengero cha zaka za kuwonongedwa kwa Yerusalemu+ kuti zidzakhala zaka 70.+ Ndinazindikira zimenezi mwa kuwerenga mawu amene Yehova anauza mneneri Yeremiya+ olembedwa m’mabuku.  Ndinayang’ana+ kwa Yehova Mulungu woona kuti ndimufunefune mwa kupemphera,+ kumuchonderera, kusala kudya, kuvala ziguduli* ndi kudzithira phulusa.+  Pamenepo ndinayamba kupemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza machimo athu kuti:+ “Inu Yehova Mulungu woona, Mulungu wamkulu+ ndi wochititsa mantha. Anthu amene amakukondani ndi kusunga malamulo anu+ mumawasungira pangano+ ndi kuwasonyeza kukoma mtima kosatha.+  Ife tachimwa,+ talakwa, tachita zinthu zoipa ndipo takupandukirani.+ Tapatuka ndiponso tasiya malamulo anu ndi zigamulo zanu.+  Sitinamvere atumiki anu aneneri,+ amene analankhula m’dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m’dziko lathu.+  Inu Yehova ndinu wolungama, koma ife manyazi aphimba nkhope zathu lero.+ Manyazi aphimba nkhope za amuna a mu Yuda, anthu a ku Yerusalemu ndi anthu onse a ku Isiraeli, amene ali pafupi ndiponso amene ali kumayiko onse akutali kumene munawabalalitsira chifukwa cha zinthu zosakhulupirika zimene anakuchitirani.+  “Inu Yehova, manyazi aphimba nkhope zathu, za mafumu athu, akalonga athu ndi makolo athu chifukwa takuchimwirani.+  Inu Yehova Mulungu wathu, ndinu wachifundo+ ndi wokhululuka,+ koma ife takupandukirani.+ 10  Sitinamvere mawu anu, inu Yehova Mulungu wathu, mwa kuyenda motsatira malamulo anu amene munatiikira kudzera mwa atumiki anu, aneneri.+ 11  Anthu onse a mu Isiraeli aphwanya malamulo anu ndipo apatuka mwa kusamvera mawu anu.+ Choncho inu mwatitsanulira temberero ndi malumbiro+ amene analembedwa m’chilamulo cha Mose, mtumiki wa Mulungu woona, pakuti takuchimwirani. 12  Inu munachitadi zimene munachenjeza kuti mudzatichitira,+ ifeyo ndi atsogoleri athu.+ Munatigwetsera tsoka lalikulu ndipo tsoka limene lagwera Yerusalemu silinachitikeponso padziko lonse lapansi.+ 13  Masoka onse amene analembedwa m’chilamulo cha Mose+ atigwera,+ ndipo ife sitinakhazike pansi mtima wanu, inu Yehova Mulungu wathu, mwa kusiya zolakwa zathu+ ndi kusonyeza kuti tikumvetsa kuti ndinu wokhulupirika.+ 14  “Inu Yehova, munakhala tcheru kuti mutigwetsere tsoka ndipo pamapeto pake munatigwetseradi tsokalo,+ pakuti inu Yehova Mulungu wathu ndinu wolungama pa ntchito zanu zonse zimene mwachita, koma ife sitinamvere mawu anu.+ 15  “Tsopano inu Yehova Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu m’dziko la Iguputo ndi dzanja lamphamvu,+ amenenso munadzipangira dzina kufikira lero,+ ife tachimwa,+ tachita zinthu zoipa. 16  Inu Yehova, nthawi zonse mumachita zinthu zolungama.+ Chonde, chotsani mkwiyo wanu waukulu pa Yerusalemu, phiri lanu loyera.+ Pakuti chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa za makolo athu,+ Yerusalemu ndi anthu anu takhala chinthu chotonzedwa ndi anthu onse otizungulira.+ 17  Tsopano inu Mulungu wathu, imvani pemphero la mtumiki wanu ndi kuchonderera kwake. Malo anu opatulika amene awonongedwa+ akomereni mtima,+ inu Yehova, chifukwa cha dzina lanu. 18  Mulungu wanga, tcherani khutu lanu kuti mumve.+ Tsegulani maso anu kuti muone kuwonongeka kwathu ndi kwa mzinda wotchedwa ndi dzina lanu.+ Ifeyo tikukuchondererani, osati chifukwa cha zochita zathu zolungama,+ koma chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ 19  Imvani, inu Yehova.+ Tikhululukireni, inu Yehova.+ Timvereni ndipo muchitepo kanthu,+ inu Yehova. Inu Mulungu wanga, chifukwa cha dzina lanu musazengereze,+ pakuti mzinda wanu ndi anthu anu amatchedwa ndi dzina lanu.”+ 20  Pamene ndinali kulankhula, kupemphera ndi kuvomereza machimo anga+ ndi machimo a anthu a mtundu wanga Aisiraeli,+ ndiponso pamene ndinali kupempha pamaso pa Yehova Mulungu wanga kuti andikomere mtima komanso kuti akomere mtima phiri loyera la Mulungu wanga,+ 21  inde, pamene ndinali kulankhula zimenezi m’pemphero, munthu uja Gabirieli,+ amene ndinamuona m’masomphenya nditatopa kwambiri poyamba paja,+ ndinamuona akubwera kwa ine pa nthawi yopereka nsembe yamadzulo, yoperekedwa ngati mphatso.+ 22  Iye anandithandiza kuti ndimvetse pondiuza kuti: “Iwe Danieli, tsopano ndabwera kuti ndikuthandize kumvetsa zinthu zonsezi.+ 23  Pamene unali kuyamba kupemphera ndinalandira uthenga, choncho ndabwera kudzakufotokozera za uthengawo chifukwa iwe ndiwe munthu wokondedwa kwambiri.+ Tsopano khala tcheru,+ ndipo umvetsetse zinthu zimene ukuona. 24  “Pali milungu 70 imene yaikidwa yokhudza anthu a mtundu wako+ ndi mzinda wanu woyera,+ ndi cholinga choti athetse kuphwanya malamulo,+ athetse machimo,+ aphimbe cholakwa,+ abweretse chilungamo kuti chikhalepo mpaka kalekale,+ adinde chidindo+ pa masomphenya ndi maulosi, ndiponso kuti adzoze Malo Opatulikitsa.+ 25  Choncho iwe uyenera kudziwa ndi kuzindikira kuti kuchokera pamene mawu adzamveka+ onena kuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso,+ kufika pamene Mesiya+ Mtsogoleri+ adzaonekere, padzadutsa milungu 7, komanso milungu 62.+ Yerusalemu adzakonzedwa ndi kumangidwanso, ndipo adzakhala ndi bwalo ndi ngalande yachitetezo. Zimenezi zidzachitika mu nthawi zovuta. 26  “Pambuyo pa milungu 62 imeneyi, Mesiya adzaphedwa+ ndipo sadzasiya kalikonse.+ “Gulu lankhondo la mtsogoleri amene akubwera lidzawononga+ mzindawo ndi malo oyera.+ Malo oyera amenewo adzafafanizidwa ndi madzi osefukira, ndipo padzakhala nkhondo mpaka kumapeto. Mulungu wagamula kuti padzakhale chiwonongeko.+ 27  “Mesiyayo* adzasungira anthu ambiri pangano+ kwa mlungu umodzi,+ kenako pakatikati pa mlunguwo adzathetsa nsembe zanyama ndi nsembe zina zoperekedwa ngati mphatso.+ “Wowonongayo+ adzabwera pamapiko a zinthu zonyansa, ndipo zimene Mulungu wagamula zidzakhuthulidwanso pa chowonongedwacho+ kufikira chitafafanizidwa.”

Mawu a M'munsi

Ena amati “masaka.”
Mawu ake enieni, “Iye.”